Kuphunzira Baibulo M’malo Osonyezerako Nyama!
NTHAŴI ina kumbuyoku tinasankha malo achilendo kaamba ka makambitsirano athu a Baibulo a banja a mlungu ndi mlungu—Emmen Zoo, pafupi ndi nyumba yathu ku Netherlands. Tinatero pa chifukwa chabwino kwambiri, chimene mudzadziŵa posachedwapa.
Monga mabanja achikristu ambiri kuzungulira dziko lonse lapansi, timakhala ndi phunziro la Baibulo la mlungu ndi mlungu. Mkati mwa phunziro limeneli kaŵirikaŵiri timaŵerenga za nyama zimene m’Baibulo zimagwiritsiridwa ntchito monga zizindikiro za makhalidwe abwino ndi oipa. Tinadzifunsa ngati tingadziŵe nyama zimenezo kwambiri ndipo tinasankha kuchipanga kukhala ntchito ya banja lonse. Aliyense m’banja anapatsidwa nyama imodzi ndipo anapemphedwa kufufuza chidziŵitso pa nyama imeneyo m’zofalitsa monga Insight on the Scriptures ndi mabaundi voliyumu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!
Pamene tikuyandikira chipata cha Emmen Zoo, maso a ana athu, Mari-Claire, Charissa, ndi Pepijn, akuŵala ndi chiyembekezo. Tidzaona ng’ona, zimbalangondo, mbidzi, nyerere, ndipo mwinamwake ngakhale nyama zinanso zimene tinaŵerengapo m’Baibulo. Koma choyamba, tatilolani tikuuzeni za malo osonyezeramo nyama apadera ameneŵa.
Kulibe Zitatanga, Kulibe Zitsulo Zotetezera
Noorder Dierenpark, monga momwe Emmen Zoo imatchedwera m’Chidatchi, ndi paki ya nyama yapadera kwambiri, yopangidwa malinga ndi malamulo amakono. Kuno simudzapeza nyama zokhala m’zitatanga kapena kuseri kwa zitsulo zotetezera. M’malo mwake, mu Emmen anayesayesa kupanga zinthu kotero kuti nyama zikhale m’malo ofanana kwambiri ndi malo ake okhalamo enieni. “M’malo mwake munthu wodzacheza ndi amene amakhala kuseri kwa tchinga, osati nyama ayi,” akutero Wijbren Landman mmodzi wa asayansi ya zamoyo m’pakiyo akumamwetulira.
“Nyamazo sizinaikidwe malinga ndi mtundu wake koma malinga ndi kumene zinachokera. Nchifukwa chake mu savanna yachiafirika yaikuluyi imene mukuona pano, muli nyama zambiri zimene zikusungidwira limodzi zimene zimakhalira limodzi m’thengo.” Ndipo indedi, tikuziona—nyama zazitali koposa m’dziko lonse lapansi, nyamalikiti zazitali makosizo, zimene zingakule kufika pautali wa mamita asanu ndi imodzi. Zili pamodzi ndi ma springbok, nswala, mbidzi, nyumbu, nakhodzwe, ndiponso ngakhale achipembere oŵerengeka.
Koma Wijbren akali ndi zambiri zotiuza ponena za savanna ya mu Emmen: “Nyamazi zili ndi malo aakulu kwambiri kwakuti sizimamva kukhala zomangika. Komabe, tinaikamonso mothaŵira. Kodi mukuiona miyala yaikuluyo? Pakati pake, springbok zingabisalemo kuti achipembere asazivute. Ndipo phiri lili apolo limatheketsa nyama kusaonana mpang’ono pomwe. Koma nthaŵi zambiri nyama sizimaonana kwenikweni. Zimenezidi si zodabwitsa, popeza kuti zakhalira limodzi mu Afirika kwa zaka zikwi zambiri.”
Mbidzi Zaludzu
“Taonani! Mbidzi!” Charissa wakondwa kwambiri. Iye anafufuza chidziŵitso chabwino kwambiri ponena za mbidzi. “Nchocholozi zimasokoneza kwambiri kaonekedwe ka kapangidwe ka mbidzi ndi maonekedwe ake pamene zili pamodzi kwakuti ngakhale anthu a maso akuthwa amene amakhala kumene izo zili kaŵirikaŵiri samaziona pamene zili chabe mamita 40 mpaka 50 kuchoka pamene iwo ali. Mphamvu zazikulu za mbidzi za kuona ndi kununkhiza kuphatikizapo kukhoza kwake kuthamanga paliŵiro lalikulu—ngakhale kuposa makilomita 60 pa ola limodzi—zili ngati chitetezo ku nyama zolusa. Monga mmene Salmo 104:11 limanenera, mbidzi ‘zipherako ludzu lawo.’ Nchifukwa chake kaŵirikaŵiri sizimapezeka makilomita oposa asanu ndi atatu kuchokera pamene pali madzi.” Ndiyeno anawonjezera kuti: “Ifenso tiyenera kupha ludzu lathu lauzimu nthaŵi zonse mwa kuyandikana ndi mpingo, kuphunzira Baibulo, ndi kufika pamisonkhano.”
Tikusiya savanna yachiafirika kumbuyo ndi kuyenda kumene kuli imodzi ya nyama zolusa zazikulu kwambiri padziko lapansi, chimbalangondo cha kodiak. Chimbalangondo chachikulu koposa chimenechi chingatalike kufika pa mamita atatu ndi kulemera kufika pa makilogalamu 780. Kuti malo awo muno akhale monga mmene ayenera kukhalira, anakonzedwa bwino ndi mitsinje ndi miyala yaikulu. Chimbalangondo cha kodiak chimenechi ndicho mkulu wa chimbalangondo chachisuriya chakuda, chimene chinaliko ku Israyeli m’nthaŵi za Baibulo. Malinga ndi kufufuza kwa Mari-Claire, zimbalangondo zimadya zakudya zosiyanasiyana. Zimadya mayani ndi mizu ya zomera pamodzinso ndi zipatso, ma berry, mtedza, mazira, tizilombo, nsomba, mbeŵa zosiyanasiyana, ndi zina zotero, ndipo zimakonda kwambiri uchi. Mu Israyeli wakale pamene zakudya za chimbalangondo zamasamba zinali zochepa, abusa anafunikira kukhala atcheru ndi kuwononga kwa zimbalangondo. Paubwana wake Davide anayang’anizana ndi chimbalangondo kuti atetezere nkhosa za atate wake.—1 Samueli 17:34-37.
“M’Mphuno Mwake Mutuluka Utsi”
Koma pali nyama zambiri zimene tikufunadi kuona. Tsiku lina m’phunziro lathu la Baibulo, tinaŵerenga za ng’ona. Poyamba, Pepijn anaifotokoza kukhala ‘ngati nsomba, komano yaikulu kwambiri!’ Popeza ng’ona zimazindikira msanga kusintha kwa tempechala, izo zimakhala mu Nyumba ya Afirika, mmene mkhalidwe wa m’madera otentha sumasintha. Titangoloŵamo, tikumva kutentha kwake ndi chinyontho, chimene chikuchititsa nthunzi pa mandala athu. Ndiponso, tiyenera kuzoloŵera mdimawo. Pamene tikuyenda pa mlatho wolenjekeka wamatabwa, mwadzidzidzi tikuona ng’ona zingapo zazikulu zimene zikulonda zithapwizo za kumbali zonse ziŵiri za mlatho. Zakhala duu pamenepo kwakuti Pepijn akusonkhezeredwa kunena kuti: “Si zenizeni.”
Ng’ona zili zina za nyama zokwawa zazikulu kwambiri zimene zilipo. Zina zingafike utali wa mamita asanu ndi limodzi ndipo zingalemere kufika pa makilogalamu 900. Mphamvu ya nsagwada zake njodabwitsa—ngakhale ng’ona yaing’onopo yolemera makilogalamu 50 ikhoza kukhala ndi mphamvu zoposa makilogalamu 700. Pamene ng’ona itumphuka pambuyo pa kumira m’madzi kwa nthaŵi yakutiyakuti, kupuma kofulumira m’mphuno mwake kungatulutse madzi amene m’kuŵala kwa dzuŵa la mmaŵa kungakhale ‘kong’anipitsa kuunika’ ndi ‘kutuluka kwa utsi m’mphuno mwake’—kumene buku la Yobu likufotokoza.—Yobu 41:1, 18-21.
“Ochenjera Monga Njoka”
Sitinasiye ng’ona kwenikweni pamene tiona mumdima—mwamwaŵi, kumbuyo kwa makhoma agalasi—mitundu ingapo ya cholengedwa chimene chimagwiritsiridwa ntchito m’Baibulo monga chizindikiro cha mikhalidwe yabwino ndi yoipa yomwe. Tikunena za njoka, nyama yoyamba kutchulidwa dzina m’Baibulo. (Genesis 3:1) Yesu anagwiritsira ntchito kuchenjera kwake monga chitsanzo polangiza ophunzira ake za khalidwe lawo pakati pa otsutsa onga afisi. (Mateyu 10:16) Komabe, zoonadi, njoka kaŵirikaŵiri imazindikiridwa monga “njoka yokalambayo,” Satana Mdyerekezi, amene pa 2 Akorinto 11:3 akufotokozedwa monga wonyenga ndi wochenjera monga njoka.—Chivumbulutso 12:9.
“Pita ku Nyerere, . . . Nuchenjere”
Chinthu chimene sitinayembekezere kuona m’paki ya nyama ndicho chulu chachikulu chimene tikuonacho, chimene chili ndi midzi itatu ya nyerere zodya mayani. Ameneŵa ndiwo alimi pakati pa nyerere. Tikuona mudziwo titaimirira kumbuyo kwa khoma lagalasi; zimenezi zikutithandiza kuphunzira makhalidwe enieni a zolengedwa zazing’onozing’ono zimenezi. Nyerere zikutichititsa chidwi chifukwa m’Baibulo zikugwiritsiridwa ntchito monga chitsanzo cha kukangalika ndi nzeru zachibadwa.—Miyambo 6:6.
Wijbren Landman ndi katswiri wa tizilombo. Iye akufotokoza kuti: ‘Pafupifupi nyerere miliyoni imodzi kuŵirikiza biliyoni imodzi zimagwira ntchito panthaka ya dziko lapansi, kutanthauza kuti pa munthu mmodzi aliyense pali nyerere zosachepera 200,000! Pa mitundu 15,000 yomwazikana pamakontinenti onse kusiyapo kumadera ozizira kwambiri, palibe iŵiri yofanana. Zonse zimapanga mitundu yosiyanasiyana ya nyumba, ndipo zimadya zakudya zosiyanasiyana, koma pafupifupi zonse zili ndi dongosolo lofanana.
‘Nyerere zodya mayani zimalima bowa wakudya, monga mmene anthu amachitira. Monga mmene mukuonera, kulima kumeneku kumachitikira pansi pa nthaka, koma chakudya cha bowa umenewo chimachokera pamwamba pa nthaka. Tsiku lonse, nyerere zantchito zimatuta mayani mokangalika kupita nawo kuchisa chawo. Zimakwera mtengo kapena chitsamba ndi kusankha tsamba. Ndiyeno, zikumagwiritsira ntchito nsagwada zawo ngati zodulira, zimadula mofulumira zidutswa zozungulira kuchoka patsambalo ndipo motsatizana zimanyamula zidutswa zimenezi kuchisa chawo, zikumazinyamula ngati mmwafuli wamtundu wina pamwamba pa mitu yawo. Zimenezi zimafotokoza dzina lawo lachiŵiri, nyerere za amwafuli. Kudula kumeneku kumachitika mofulumira kwambiri kwakuti ku South ndi Central America, zimamaliza mayani a zitsamba kapena mitengo m’maola ochepa okha. Nchifukwa chake si zokondedwa kwambiri kumeneko! M’chisa antchito ena amayeretsa zidutswa za masambazo mosamala asanayambe kuzitafuna. Pambuyo pake, chipondeponde chimene chimakhalapo chimasanganizidwa ndi ma enzyme ndi ma amino acid amene nyererezo zimatulutsa. Tsopano ndiyo nthaŵi pamene chipondepondecho chingakhale chakudya cha bowawo, motero pakumakhala chakudya chosatha cha mudzi wonse.’
Tikuchoka pamudzi wa nyerere tili okondwa kwambiri ndi nzeru ndi luso lakupanga zinthu loonekera mu zolengedwa zosiyanasiyana zosaŵerengeka. Ndi mmadzulo tsopano, ndipo tiyenera kubwerera kunyumba. Koma pali zina zambiri zimene tingafune kuona. Sitinapite kwa akadzidzi (Yesaya 13:21, NW), akatumbu (Eksodo 35:23) mvuu (Yobu 40:15), nthiŵatiŵa (Yeremiya 50:39), kapena nyama zina zambiri zimene zili muno zimene zinatchulidwa m’Baibulo. Iliyonse njoyenera kuiphunzira. Mosakayikira tidzabweranso ku Emmen Zoo!—Yoperekedwa.
[Mawu a Chithunzi patsamba 16]
Nthiŵatiŵa: Yotvatah Nature Reserve