Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 26
  • Kodi Mulungu Angandithandize Ndikapemphera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Angandithandize Ndikapemphera?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • Kodi Yehova Amamvetsera Mapemphero Athu?
    Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Kodi Mulungu Amamva Mapemphero Athu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
  • Kuyandikira kwa Mulungu m’Pemphero
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 26

Kodi Mulungu Angandithandize Ndikapemphera?

Yankho la m’Baibulo

Inde, Mulungu amathandiza anthu amene amapempha kuchokera pansi pa mtima zinthu zogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. Mwina inu simunapempherepo koma mukhoza kulimbikitsidwa kuona zitsanzo za m’Baibulo za anthu amene anapemphera kwa Mulungu kuti, “Ndithandizeni” kapena kuti, “Inu ndinu mthandizi wanga.” Mwachitsanzo:

  • “Ndithandizeni Yehova, Mulungu wanga: Ndipulumutseni monga mwa chifundo chanu.”—Salimo 109:26, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

  • “Ine ndine wozunzika ndi waumphawi . . . Inu ndinu mthandizi wanga, ndi mpulumutsi wanga.”—Salimo 40:17, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

N’zoona kuti amene analemba mawu amenewa ankakhulupirira kwambiri Mulungu. Koma Mulungu amamvetseranso munthu aliyense amene akupemphera ndi cholinga chabwino. Mwachitsanzo amamvetsera anthu “a mtima wosweka” kapena “odzimvera chisoni mumtima mwawo.”—Salimo 34:18.

YMusamaganize kuti Mulungu ali kutali kwambiri ndi inuyo moti mavuto anu alibe nawo ntchito. Baibulo limanena kuti: “Ngakhale kuti Yehova ali pamwamba, amaona wodzichepetsa, koma wodzikuza samuyandikira.” (Salimo 138:6) Yesu anauzanso ophunzira ake kuti: “Ndipotu tsitsi lenilenilo la m’mutu mwanu amaliwerenga.” (Mateyu 10:30) Mulungu amakudziwani bwino kwambiri kuposa mmene inuyo mumadzidziwira. Choncho n’zosakayikitsa kuti akhoza kuyankha mapemphero anu pamene muli pa mavuto enaake.—1 Petulo 5:7.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena