Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Kubadwanso Ndiyo Njira Yopezera Chipulumutso?
    Nsanja ya Olonda—2009 | April 1
    • Kodi Kubadwanso Ndiyo Njira Yopezera Chipulumutso?

      KODI mungayankhe bwanji munthu atakufunsani kuti: “Kodi ndinu wobadwanso?” Anthu ambiri akhoza kuyankha mosakaika kuti, “Inde.” Iwo amakhulupirira kuti Akhristu onse oona ayenera kubadwanso kapena kuti kubadwa mwatsopano ndipo amati imeneyi ndi njira yokhayo yopezera chipulumutso. Iwo amagwirizana ndi mawu a katswiri wina wamaphunziro a zaumulungu, dzina lake Robert C. Sproul, yemwe analemba kuti: “Ngati munthu sanabadwenso, . . . ndiye kuti si Mkhristu.”

      Kodi inunso mumakhulupirira kuti kubadwa mwatsopano ndiyo njira imene ingakupezetseni chipulumutso? Ngati zili choncho, ndiye kuti mungafune kuthandiza abale anu ndiponso anzanu kuti nawonso apeze njirayo n’kuyamba kuyendamo. Komabe, kuti iwo achite zimenezi, ayenera kumvetsa bwino kusiyana kwa munthu amene anabadwanso ndi wosabadwanso. Ndiyeno, kodi mungawafotokozere bwanji tanthauzo la kubadwanso?

      Anthu ambiri amakhulupirira kuti munthu wobadwanso ndi amene analonjeza ndi mtima wonse kuti adzatumikira Mulungu ndi Khristu, ndipo chifukwa cha zimenezi, amasintha khalidwe lake loipa n’kuyamba ntchito zabwino.

      Koma mukhoza kudabwa kwambiri mutadziwa kuti Baibulo siligwirizana ndi maganizo amenewa. Kodi mungakonde kudziwa zimene Mawu a Mulungu amanena pa nkhani ya kubadwanso? Kunena zoona, mungapindule kwambiri ngati mutafufuza mozama nkhaniyi m’Baibulo chifukwa kudziwa tanthauzo la kubadwanso kungakhudze kwambiri moyo wanu ndiponso chiyembekezo chanu.

      Kodi Baibulo Limati Chiyani Pankhaniyi?

      M’Baibulo lonse, mawu akuti “kubadwanso” amapezeka pa Yohane 3:1-12 pokha. Mavesi amenewa amafotokoza nkhani yochititsa chidwi imene Yesu ndi mtsogoleri wina wachipembedzo ku Yerusalemu anakambirana. Nkhani imeneyi ili m’bokosi limene lili patsamba lotsatirali. Tikukulimbikitsani kuwerenga nkhaniyi mosamala.

      M’nkhaniyi, Yesu anafotokoza mbali zosiyanasiyana za “kubadwa mwatsopano.”a Ndipotu zimene Yesu ananena zikutithandiza kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri awa:

      ◼ Kodi kubadwa mwatsopano n’kofunika motani?

      ◼ Kodi munthu amachita kusankha yekha kuti abadwe mwatsopano?

      ◼ Kodi cholinga cha kubadwa mwatsopano n’chiyani?

      ◼ Kodi chimachitika n’chiyani kuti munthu abadwe mwatsopano?

      ◼ Kodi zimenezi zimathandiza munthu kuti akhale paubwenzi ndi Mulungu?

      Tiyeni tione mafunso amenewa, lililonse palokha.

      [Mawu a M’munsi]

      a Mawu akuti ‘kubadwa mwatsopano’ amapezeka pa 1 Petulo 1:3, 23, ndipo ndi ofanana ndi mawu akuti “kubadwanso.” Mawu awiri onsewa anachokera ku mawu a Chigiriki akuti, gen·naʹo.

      [Bokosi/​Chithunzi patsamba 4]

      “Anthu Inu Muyenera Kubadwanso”

      “Panali Mfarisi wina dzina lake Nikodemo, mmodzi wa olamulira a Ayuda. Iyeyu anabwera kwa Yesu usiku ndi kumuuza kuti: ‘Rabi, tikudziwa kuti inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; chifukwa munthu sangathe kuchita zizindikiro zimene inu mumachita ngati Mulungu sali naye.’ Poyankha Yesu anati kwa iye: ‘Ndithudi ndikukuuza, Munthu sangathe kuona ufumu wa Mulungu atapanda kubadwanso.’ Nikodemo anati kwa iye: ‘Munthu angabadwe bwanji ali wamkulu kale? Kodi angathe kulowa m’mimba mwa mayi wake ndi kubadwanso?’ Yesu anayankha nati: ‘Ndithudi ndikukuuza, Munthu sangathe kulowa mu ufumu wa Mulungu atapanda kubadwa mwa madzi ndi mzimu. Chobadwa mwa thupi n’chanyama, ndipo chobadwa mwa mzimu n’chauzimu. Usadabwe chifukwa ndakuuza kuti, Anthu inu muyenera kubadwanso. Mphepo imawombera kumene ikufuna, ndipo munthu amamva mkokomo wake, koma sadziwa kumene ikuchokera ndi kumene ikupita. N’chimodzimodzinso aliyense wobadwa mwa mzimu.’ Poyankha Nikodemo anati kwa iye: ‘Zimenezi zingatheke bwanji?’ Yesu anamuyankha nati: ‘Kodi iwe sudziwa zinthu zimenezi, chikhalirecho ndiwe mphunzitsi wa Isiraeli? Ndithudi ndikukuuza, Zimene ife timadziwa timazilankhula, ndipo zimene taona timazichitira umboni, koma anthu inu simulandira umboni umene timapereka. Ngati ndakuuzani zinthu za padziko lapansi koma inu osakhulupirira, mudzakhulupirira bwanji ndikakuuzani zinthu za kumwamba?’”​—Yohane 3:1-12.

  • Kodi Kubadwa Mwatsopano N’kofunika Motani?
    Nsanja ya Olonda—2009 | April 1
    • Kodi Kubadwa Mwatsopano N’kofunika Motani?

      POKAMBIRANA ndi Nikodemo, Yesu anatsindika mfundo yakuti kubadwa mwatsopano, kapena kuti kubadwanso, n’kofunika kwambiri. Kodi iye anasonyeza motani zimenezi?

      Taonani mmene Yesu anasonyezera kufunika kobadwa mwatsopano pokambirana ndi Nikodemo. Iye anati: “Munthu sangathe kuona ufumu wa Mulungu atapanda kubadwanso.” (Yohane 3:3) Mawu akuti “sangathe” ndiponso “atapanda” akusonyeza kufunika kobadwa mwatsopano. Mwachitsanzo, munthu atanena kuti, “Dzuwa litapanda kutuluka, kunja sikungache,” akutanthauza kuti dzuwa n’lofunika kwambiri kuti kunja kuche. Mofanana ndi zimenezi, Yesu ananena kuti kubadwanso n’kofunika kwambiri kuti munthu aone Ufumu wa Mulungu.

      Pomalizira, Yesu ananena mawu otsatirawa pofuna kutsindika mfundoyi. Iye anati: “Anthu inu muyenera kubadwanso.” (Yohane 3:7) Choncho, malinga ndi zimene Yesu ananenazi, kuti munthu ‘akalowe mu Ufumu wa Mulungu,’ ayenera kubadwanso.​—Yohane 3:5.

      Yesu anaona kuti kubadwa mwatsopano n’kofunika kwambiri. Choncho, Akhristu ayenera kuonetsetsa kuti nkhani imeneyi akuyimvetsa bwino. Mwachitsanzo, kodi mukuganiza kuti Mkhristu angasankhe yekha kuti abadwenso?

      [Mawu Otsindika patsamba 5]

      “Dzuwa litapanda kutuluka, kunja sikungache”

  • Kodi Kubadwa Mwatsopano Ndi Nkhani Yoti Munthu Amachita Kusankha Yekha?
    Nsanja ya Olonda—2009 | April 1
    • Kodi Kubadwa Mwatsopano Ndi Nkhani Yoti Munthu Amachita Kusankha Yekha?

      KODI ndani amene amachititsa kuti munthu abadwe mwatsopano? Alaliki ena achikhristu akamalimbikitsa anthu kuti abadwe mwatsopano, amagwiritsa ntchito mawu a Yesu akuti: “Anthu inu muyenera kubadwanso.” (Yohane 3:7) Alaliki amenewa amagwiritsa ntchito mawu akuti “muyenera kubadwanso” ngati lamulo. Motero, iwo amalalikira kuti munthu aliyense ayenera kumvera Yesu ndi kuchita zinthu zonse zimene iwo amati n’zofunika kuti munthu abadwe mwatsopano. Iwo amakhala akutanthauza kuti kubadwa mwatsopano ndi nkhani yoti munthu akhoza kusankha yekha. Koma kodi maganizo amenewa akugwirizana ndi zimene Yesu anauza Nikodemo?

      Tikawerenga mosamala mawu a Yesu, timaona kuti iye sanaphunzitse kuti munthu aliyense ayenera kusankha yekha kuti abadwe mwatsopano kapena ayi. Tikutero chifukwa chakuti mawu a Chigiriki amene anamasuliridwa kuti “kubadwanso” angamasuliridwenso kuti “kubadwa kuchokera kumwamba.”a Mogwirizana ndi mawu amenewa, kubadwa mwatsopano kumachokera “kumwamba,” kapena kuti “kwa Atate.” (Yohane 19:11; Yakobe 1:17) Choncho, Mulungu ndi amene amachititsa kuti munthu abadwe mwatsopano.​—1 Yohane 3:9.

      Tikamakumbukira mawu akuti “kuchokera kumwamba,” sizingativute kumvetsa mfundo yakuti munthu sangasankhe yekha kuti abadwe mwatsopano. Taganizirani zimene zinachitika kuti mubadwe. Kodi munachita kusankha nokha? Ayi, chifukwa makolo anu ndi amene anachititsa kuti mubadwe. Mofanana ndi zimenezi, tingabadwe mwatsopano pokhapokha ngati Mulungu, yemwe ndi Atate wathu wa kumwamba, wachititsa kuti tibadwe mwatsopano. (Yohane 1:13) N’chifukwa chake mtumwi Petulo anati: “Atamandike Mulungu amenenso ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, pakuti mwa chifundo chake chachikulu, anatibala mwatsopano.”​—1 Petulo 1:3.

      Kodi Ndi Lamulo?

      Ena angadabwe kuti, ‘Ngati zili zoona kuti palibe munthu amene amasankha yekha kubadwanso, n’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti: “Anthu inu muyenera kubadwanso”?’ Funso limeneli n’lomveka. Komabe mawu amene Yesu ananenawa akanakhala kuti ndi lamulo, ndiye kuti iye analamula zinthu zimene sitingathe kuchita. Choncho, mfundo yakuti limeneli ndi lamulo ndi yosamveka. Nangano kodi mawu akuti “muyenera kubadwanso” akutanthauza chiyani kwenikweni?

      Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “muyenera kubadwanso,” amasonyeza kuti mawuwa si lamulo. Choncho, pamene Yesu ananena kuti “muyenera kubadwanso,” ankangotchula mfundo yofunika osati kupereka lamulo. Malinga ndi Baibulo lina, iye anati: “M’pofunika kuti mubadwe kuchokera kumwamba.”​—Yohane 3:7, Modern Young’s Literal Translation.

      Kuti timvetse bwino nkhaniyi, tiyerekezere kuti mumzinda winawake muli sukulu ya ana ochokera kumayiko ena. Tsiku lina pasukulupo pakufika mwana wina wam’dziko lomwelo n’kuuza mphunzitsi wamkulu kuti: “Ndabwera kuti ndidzalembetse nawo sukulu.” Mphunzitsi wamkuluyo akumuyankha kuti: “Kuti uyambe sukulu pano, uyenera kukhala wochokera kudziko lina.” Pamenepa sikuti mphunzitsiyu akulamula mwanayu kuti “akhale wochokera kudziko lina.” Koma akungomuuza zomuyeneretsa kuti alembedwe sukulu. Mofanana ndi zimenezi, pamene Yesu ananena kuti “anthu inu muyenera kubadwanso,” sikuti ankapereka lamulo. Koma iye ankangonena zinthu zoyenera zimene zingathandize kuti munthu ‘adzalowe mu Ufumu wa Mulungu.’

      Mawu akuti Ufumu wa Mulungu, omwe ndi omalizira palembali, akutithandiza kupeza yankho la funso linanso lokhudza kubadwa mwatsopano. Funso lake n’lakuti, Kodi cholinga cha kubadwa mwatsopano n’chiyani? Kudziwa yankho la funso limeneli n’kofunika kwambiri chifukwa kungatithandize kumvetsa bwino tanthauzo la kubadwa mwatsopano.

      [Mawu a M’munsi]

      a Mabaibulo ena anamasulira lemba la Yohane 3:3 m’njira imeneyi. Mwachitsanzo, Baibulo lina limati: “Munthu sangathe kuona ufumu wa Mulungu atapanda kubadwa kuchokera kumwamba.”​—A Literal Translation of the Bible.

      [Chithunzi patsamba 6]

      Kodi kubadwa mwatsopano n’kofanana bwanji ndi kubadwa kwenikweni?

  • Kodi Kubadwa Mwatsopano Kuli N’cholinga Chotani?
    Nsanja ya Olonda—2009 | April 1
    • Kodi Kubadwa Mwatsopano Kuli N’cholinga Chotani?

      ANTHU ambiri amaganiza kuti munthu ayenera kubadwanso kuti adzalandire chipulumutso. Koma taonani zimene Yesu ananena zokhudza cholinga cha kubadwa mwatsopano. Iye anati: “Munthu sangathe kuona ufumu wa Mulungu atapanda kubadwanso.” (Yohane 3:3) Choncho, munthu ayenera kubadwanso kuti akalowe mu Ufumu wa Mulungu osati kuti adzapeze chipulumutso. Komabe, ena anganene kuti mawu akuti kulowa mu Ufumu ndiponso kupeza chipulumutso akutanthauza chinthu chimodzi. Koma zimenezi si zoona. Kuti timvetse kusiyana kwake, tiyeni tikambirane kaye tanthauzo la mawu akuti “Ufumu wa Mulungu.”

      Ufumu ndi boma, ndipo mawu akuti “Ufumu wa Mulungu” akutanthauza “boma la Mulungu.” Baibulo limatiuza kuti Yesu Khristu, yemwe amatchedwanso “mwana wa munthu,” ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndipo palinso ena amene adzalamulire naye. (Danieli 7:1, 13, 14; Mateyo 26:63, 64) Kuwonjezera pamenepa, masomphenya amene mtumwi Yohane anaona amasonyeza kuti anthu amene adzalamulire ndi Khristu amasankhidwa kuchokera “mu fuko lililonse, lilime, mtundu, ndi dziko lililonse,” ndipo “adzalamulira dziko lapansi monga mafumu.” (Chivumbulutso 5:9, 10; 20:6) Mawu a Mulungu amatiuzanso kuti anthu amene adzalamulire monga mafumu amapanga “kagulu” ka anthu okwana 144,000 “amene anagulidwa padziko lapansi.”​—Luka 12:32; Chivumbulutso 14:1, 3.

      Kodi likulu la Ufumu wa Mulungu lili kuti? “Ufumu wa Mulungu” umatchedwanso “ufumu wa kumwamba.” Zimenezi zikusonyeza kuti Yesu limodzi ndi olamulira anzake amalamulira kuchokera kumwamba. (Luka 8:10; Mateyo 13:11) Choncho, Ufumu wa Mulungu ndi boma la kumwamba lolamulidwa ndi Yesu Khristu pamodzi ndi olamulira anzake osankhidwa kuchokera mwa anthu.

      Nanga kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene anati munthu ayenera kubadwanso kuti “akalowe mu Ufumu wa Mulungu”? Ankatanthauza kuti munthu ayenera kubadwanso kuti akalamulire ndi Khristu kumwamba. Choncho, cholinga cha kubadwa mwatsopano ndicho kukonzekeretsa kagulu ka anthu amenewa kuti ayenerere kukalamulira kumwamba.

      Pofika pano, taona kuti kubadwa mwatsopano n’kofunika kwambiri, kumachititsidwa ndi Mulungu, ndiponso kuti kumakonzekeretsa kagulu ka anthu kuti ayenerere kukalamulira kumwamba. Koma kodi chimachitika n’chiyani kuti munthu abadwe mwatsopano?

      [Mawu Otsindika patsamba 7]

      Cholinga cha kubadwa mwatsopano ndicho kukonzekeretsa kagulu ka anthu kuti ayenerere kukalamulira kumwamba

      [Chithunzi patsamba 7]

      Yesu Khristu pamodzi ndi olamulira anzake osankhidwa kuchokera mwa anthu ndi amene amapanga Ufumu wa Mulungu

  • Kodi Kubadwa Mwatsopano Kumachitika Motani?
    Nsanja ya Olonda—2009 | April 1
    • Kodi Kubadwa Mwatsopano Kumachitika Motani?

      POLANKHULA ndi Nikodemo za kubadwa mwatsopano, Yesu sanangonena za kufunika kwake, kapena za cholinga chake koma anamuuzanso chimene chimachititsa kuti munthu abadwenso. Iye anati: “Munthu sangathe kulowa mu ufumu wa Mulungu atapanda kubadwa mwa madzi ndi mzimu.” (Yohane 3:5) Choncho, munthu amabadwanso akabatizidwa mwa madzi ndi mzimu. Koma kodi mawu akuti “madzi ndi mzimu” akutanthauza chiyani?

      Tanthauzo la “Kubadwa mwa Madzi ndi Mzimu”

      N’zosakayikitsa kuti Nikodemo, yemwe anali mtsogoleri wachipembedzo cha Chiyuda, ankadziwa bwino tanthauzo la mawu akuti “mzimu wa Mulungu” m’Malemba a Chiheberi. Iye ankadziwa kuti mzimu umenewu ndi mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, imene ingachititse munthu kuchita zozizwitsa. (Genesis 41:38; Eksodo 31:3; 1 Samueli 10:6) Choncho, pamene Yesu anagwiritsa ntchito mawu akuti “mzimu,” Nikodemo ayenera kuti anadziwa tanthauzo limeneli.

      Nanga Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena za madzi? Taonani zimene zinalembedwa, Yesu ndi Nikodemo asanayambe kukambirana ndiponso atangomaliza kukambirana. Zimenezi zimasonyeza kuti Yohane Mbatizi ndiponso ophunzira a Yesu ankabatiza anthu ndi madzi. (Yohane 1:19, 31; 3:22; 4:1-3) Ubatizo wa madzi unali wodziwika kwambiri ku Yerusalemu. Motero, pamene Yesu anatchula za madzi, Nikodemo ayenera kuti anadziwa kuti iye sankatanthauza madzi aliwonse, koma ubatizo wa madzi.a

      Kubatizidwa “ndi Mzimu Woyera”

      Ngati “kubadwa mwa madzi” kukutanthauza kubatizidwa ndi madzi, nanga “kubadwa mwa . . . mzimu” kukutanthauza chiyani? Yesu asanakambirane ndi Nikodemo, Yohane Mbatizi anali atanena kale kuti madzi ndiponso mzimu n’zofunika kwambiri paubatizo. Iye anati: “Ine ndakubatizani m’madzi, koma iye [Yesu] adzakubatizani ndi mzimu woyera.” (Maliko 1:7, 8) Nayenso Maliko, yemwe analemba nawo mabuku a uthenga wabwino anafotokoza nthawi yoyamba imene ubatizo wotere unachitika. Iye analemba kuti: “M’masiku amenewo, Yesu anabwera kuchokera ku Nazarete wa ku Galileya ndipo anabatizidwa ndi Yohane mu Yorodano. Ndipo atangovuuka m’madzimo, anaona kumwamba kukutseguka, ndiyeno mzimu ukutsika ngati nkhunda kudzatera pa iye.” (Maliko 1:9, 10) Yesu atamizidwa mumtsinje wa Yorodano, anabatizidwa ndi madzi. Koma panthawi imene analandira mzimu kuchokera kumwamba, anabatizidwa ndi mzimu woyera.

      Patapita zaka pafupifupi zitatu Yesu atabatizidwa, iye anauza ophunzira ake kuti: “Pasanathe masiku ambiri mudzabatizidwa ndi mzimu woyera.” (Machitidwe 1:5) Kodi zimenezi zinachitika liti?

      Ophunzira a Yesu pafupifupi 120 anasonkhana m’nyumba inayake ku Yerusalemu pa Pentekosite mu 33 C.E. Baibulo limati: “Mwadzidzidzi kumwamba kunamveka mkokomo ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo unadzaza nyumba yonseyo imene iwo anakhalamo. Pamenepo iwo anaona malawi ooneka ngati malilime a moto. . . . Ndipo onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyera.” (Machitidwe 2:1-4) Tsiku lomwelo, mtumwi Petulo analimbikitsa anthu enanso ku Yerusalemu kuti abatizidwe ndi madzi. Iye anauza gulu la anthulo kuti: “Lapani, ndipo aliyense wa inu abatizidwe m’dzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe. Pamenepo mudzalandira mphatso yaulere ya mzimu woyera. Choncho amene analandira mawu akewo ndi mtima wonse anabatizidwa, moti tsiku limenelo anthu pafupifupi 3,000 anawonjezedwa.”​—Machitidwe 2:38, 41.

      Ubatizo wa Mbali Ziwiri

      Kodi ubatizo wa madzi ndi mzimu ukusonyeza chiyani za kubadwa mwatsopano? Ukusonyeza kuti kubadwa mwatsopano kumachitika m’njira ziwiri. Kumbukirani kuti choyamba, Yesu anabatizidwa ndi madzi ndipo kenako analandira mzimu woyera. Mofanana ndi zimenezi, ophunzira oyambirira nawonso ankayamba kubatizidwa ndi madzi (ena anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi), ndipo kenako ankalandira mzimu woyera. (Yohane 1:26-36) Ndiponso anthu 3,000 amene anakhulupirira, choyamba anabatizidwa ndi madzi ndipo kenako analandira mzimu woyera.

      Poganizira ubatizo umene unachitika pa Pentekosite mu 33 C.E., kodi masiku ano munthu amabadwa mwatsopano m’njira yotani? M’njira yofanana ndi mmene atumwi a Yesu ndiponso ophunzira ake oyambirira anachitira. Choyamba, munthu amalapa machimo ake, kusiya njira zake zoipa n’kudzipereka kwa Yehova. Munthu amachita zimenezi kuti azilambira ndi kutumikira Mulungu. Ndiponso amasonyeza poyera kuti anadzipereka kwa Yehova pobatizidwa m’madzi. Kenako, ngati Mulungu angasankhe munthuyo kuti akalamulire mu Ufumu wake, amamudzoza ndi mzimu woyera. Mbali yoyamba ya ubatizowu (kubatizidwa ndi madzi) ndi imene munthu amachita kusankha yekha, pamene mbali yachiwiri (kubatizidwa ndi mzimu), amasankha ndi Mulungu. Choncho, munthu akabatizidwa mwa madzi ndi mzimu, m’pamene amabadwa mwatsopano.

      Nanga n’chifukwa chiyani Yesu pokambirana ndi Nikodemo anagwiritsa ntchito mawu akuti “kubadwa mwa madzi ndi mzimu”? N’chifukwa chakuti ankafuna kutsindika mfundo yakuti moyo wa munthu amene wabatizidwa mwa madzi ndi mzimu umasintha kwambiri. Tikambirana mfundo imeneyi m’nkhani yotsatirayi.

      [Mawu a M’munsi]

      a Panthawi inayake ya ubatizo, mtumwi Petulo ananena kuti: “Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi?”​—Machitidwe 10:47.

      [Chithunzi patsamba 9]

      Yohane ankabatiza Aisiraeli olapa ndi madzi

  • Kodi Kubadwa Mwatsopano Kumakwaniritsa Zinthu Zotani?
    Nsanja ya Olonda—2009 | April 1
    • Kodi Kubadwa Mwatsopano Kumakwaniritsa Zinthu Zotani?

      N’CHIFUKWA chiyani Yesu anagwiritsa ntchito mawu akuti “kubadwa mwa . . . mzimu” polankhula za kubatizidwa ndi mzimu woyera? (Yohane 3:5) Mawu akuti “kubadwa” akagwiritsidwa ntchito mophiphiritsira, amatanthauza “kuyambika,” monga ngati mawu akuti “kubadwa kwa fuko.” Motero, mawu akuti “kubadwa mwatsopano” amatanthauza “kuyambika kwatsopano.” Choncho, mawu ophiphiritsa akuti “kubadwa” ndiponso “kubadwa mwatsopano,” akutsindika mfundo yakuti pamakhala kuyambika kwatsopano kwa ubwenzi wa pakati pa Mulungu ndi anthu amene amabatizidwa ndi mzimu woyera. Kodi kusintha kwakukulu kumeneku kumachitika motani?

      Pofotokoza mmene Mulungu amathandizira anthu kukonzekera kukalamulira kumwamba, mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito fanizo lokhudza banja. Iye analembera Akhristu a m’nthawi yake kuti Mulungu ‘adzawatenga iwo kukhala ana ake.’ Zimene zikusonyeza kuti azidzachita nawo zinthu ‘ngati ana ake.’ (Agalatiya 4:5; Aheberi 12:7) Tiyeni tiganizirenso za fanizo la mwana wofuna kulembedwa sukulu uja, kuti timvetse mmene Mulungu adzatengere anthu amenewa kukhala ana ake. Zimenezi zitithandizanso kumvetsa kusintha kumene kumachitika munthu akabatizidwa ndi mzimu woyera.

      Kutengedwa Ngati Ana a Mulungu Kumasintha Zinthu

      M’chitsanzo chija, mwana uja sanaloledwe kulembetsa sukulu chifukwa si wochokera kudziko lina. Ndiyeno tayerekezerani kuti tsiku lina zinthu zikusintha chifukwa bambo wina wochokera kudziko lina akutenga mwanayo m’njira yovomerezeka ndi lamulo kuti akhale mwana wake. Zimenezi zingachititse kuti mwanayo aloledwe kuphunzira pasukulu ija, popeza kuti tsopano ali ndi ufulu wofanana ndi wa ana ochokera kumayiko ena. Choncho, kutengedwa ngati mwana wa bambo wadziko lina, kwachititsa kuti mwanayo azionedwa kuti ndi wadziko lina.

      Zimenezi zikusonyeza zimene zimachitikira anthu amene abadwa mwatsopano. Taonani kufanana komwe kulipo. Mwana wam’chitsanzo chija angaloledwe kuphunzira pasukulupo pokhapokha ngati ali woyenerera mwalamulo, kutanthauza kuti ayenera kukhala wochokera kudziko lina. Koma iye sangakwanitse kuchita zimenezi payekha. Ndi mmenenso zilili ndi anthu amene adzalamulire mu Ufumu wa Mulungu kapena kuti boma la kumwamba. Iwo angakhale oyenerera pokhapokha ngati ‘atabadwanso.’ Koma iwo sangakwanitse kuchita zimenezi paokha chifukwa Mulungu ndi amene amachititsa kuti munthu abadwe mwatsopano.

      Kodi n’chiyani chimene chinathandiza kuti mwana uja alembedwe sukulu? N’chifukwa choti anatengedwa ndi bambo wochokera kudziko lina n’kukhala ngati mwana wake. Komabe zimenezi sizinasinthe maonekedwe a mwanayo. Ngakhale zili choncho, mwanayo atatengedwa ndi bamboyo anayamba kuonedwa ngati wadziko lina. Pamenepa tinganene kuti mwanayo anayamba moyo watsopano, ndipo anakhala ngati wabadwa mwatsopano. Iye anakhala mwana wa bamboyo, ndipo zimenezi zinam’thandiza kuti akhale ndi ufulu woyamba kuphunzira pasukulu ija.

      Mofanana ndi zimenezi, Yehova anachititsa kuti anthu ena opanda ungwiro asinthe n’kuyenerera kukhala ana ake. Mtumwi Paulo, yemwe anali m’gulu la anthu amenewa, analembera okhulupirira anzake kuti: “Munalandira mzimu wakuti mukhale ana, umene tifuula nawo kuti: ‘Abba, Atate!’ Pakuti mzimuwo uchitira umboni pamodzi ndi mzimu wathu kuti ndife ana a Mulungu.” (Aroma 8:15, 16) Choncho, Akhristu amenewo anakhala mbali ya banja la Mulungu, kapena kuti “ana a Mulungu” chifukwa iye anawatenga n’kukhala ana ake.​—1 Yohane 3:1; 2 Akorinto 6:18.

      Komabe anthu amene anatengedwa kukhala ana a Mulungu sanasinthe matupi awo, iwo anakhalabe opanda ungwiro. (1 Yohane 1:8) Ndipo monga mmene Paulo anafotokozera, anthuwa amasintha n’kukhala ana a Mulungu iye akawatenga mwalamulo. Ndipo nthawi yomweyo, mzimu wa Mulungu unawachititsa kukhulupirira mwamphamvu kuti akakhala ndi Khristu kumwamba. (1 Yohane 3:2) Mzimu woyera ndi umene unachititsa kuti akhale ndi chikhulupiriro chimenecho, chomwe chinasintha kwambiri moyo wawo. (2 Akorinto 1:21, 22) Motero tinganene kuti iwo anakhala ndi chiyambi chatsopano, kapena kuti anabadwa mwatsopano.

      Ponena za anthu amene Mulungu wawatenga kukhala ana ake, Baibulo limati: “Adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye zaka 1,000.” (Chivumbulutso 20:6) Ana a Mulungu amenewa adzalamulira monga mafumu pamodzi ndi Khristu mu Ufumu wa Mulungu, kapena kuti boma lakumwamba. Ndipo mtumwi Petulo analembera okhulupirira anzake kuti adzalandira “cholowa chosawonongeka ndi chosadetsedwa ndi chosasuluka,” chimene Mulungu ‘anawasungira kumwamba.’ (1 Petulo 1:3, 4) Kunena zoona, cholowa chimenechi ndi chamtengo wapatali kwambiri.

      Komabe, nkhani ya ulamuliroyi ikubweretsa funso lina lakuti: Ngati anthu obadwanso adzalamulire monga mafumu kumwamba, kodi iwo adzalamulira ndani? Tikambirana funso limeneli m’nkhani yotsatirayi.

      [Chithunzi patsamba 10]

      Kodi Paulo ananena zotani pankhani ya anthu otengedwa kukhala ana a Mulungu?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena