Nyimbo 112
Yehova, Mulungu Wamkulu
Losindikizidwa
1. Inu Yehova M’lungu wamkulu
Ndinu woyeneradi
Kutamandidwa zedi.
Ndinu wabwino ndi wolungama.
Ndinu M’lungu kosatha.
2. Mumakhululukiradi anthu
Amene monga inu
Ndi achifundo ndithu.
Mumasonyeza kukoma mtima
Pa zonse mumachita.
3. Mutamandidwe ndi anthu onse
Dzina lanu liyere
Wina asalikane.
Dziko lapansi likhale mmene
Inu mumafunira.
(Onaninso Deut. 32:4; Miy. 16:12; Mat. 6:10; Chiv. 4:11.)