NYIMBO 82
“Muzionetsa Kuwala Kwanu”
Losindikizidwa
1. Yesu walamula
Kuti tiwale.
Monga dzuwa
limawalira onse,
Nafe tifikire
Anthu onsewo.
Choncho tizisonyeza
Kuwala kwake.
2. Uthenga wa M’lungu
ufalikire.
Uzitiwalira
Polalikira.
Tiphunzitse anthu
Choonadichi.
Anthu asankhe okha
Kumva uthenga.
3. Tikamasonyeza
Kukoma mtima
Timawalitsadi
Dziko la mdima.
Choncho tisonyeze
Kuwala kwathu.
Tikatero Mulungu
Asangalala.
(Onaninso Sal. 119:130; Mat. 5:14, 15, 45; Akol. 4:6.)