Mutu 6
Nkhani Imene Cholengedwa Chonse Chiyenera Kuyang’anizana Nayo
1. (a) Kodi ndinkhani iti imene Satana anadzutsa mu Edeni? (b) Kodi nkhaniyo ikutanthauzidwa motani mwa zimene ananena?
PAMENE chipanduko chinayamba m’Edeni nkhani yaikulu inadzutsidwa imene imayambukira chilengedwe chonse. Pofika kwa Hava, Satana anatanthauza kuti iye ndi mwamuna wake Adamu anali kumanidwa kwambiri zina. Iye anafunsa kuti: “Kodi anatitu Mulungu, usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” Hava anayankha kuti unali mtengo umodzi wokha umene Mulungu anati: “Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe.” Pamenepo Satana anaimba Yehova mlandu wa kunama, akumati moyo wa Hava kapenanso wa Adamu sunadalire pa kumvera Mulungu. Iye ananena kuti Mulungu anali kumana zolengedwa zake kanthu kena kabwino—luso la kukhazikitsa miyezo ya iwo eni m’moyo. “Kufa simudzafai,” anatero motsimikiza Satana. “Chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.” (Gen. 3:1-5) Satana anachititsa Hava kukhulupirira kuti akakhala bwinopo mwa kupanga zosankha za iye mwini. Ichi chikutanthauza kuti, iye pamenepo anatokosa kuyenera kwa Mulungu kwa kulamulira ndi njira Yake ya kulamulira. Nkhani yodzutsidwa inaphatikizapo kwakukulukulu ulamuliro wa chilengedwe chonse.
2. Kodi nchiyani chimene chikanatetezera anthu awiri oyambawo?
2 Chikondi cha pa Yehova chikanatetezera Hava. Kulemekeza umutu wa mwamuna wake kukanamchinjirizanso ku kuchita cholakwa. Koma iye analingalira kokha za chimene chinawonekera kukhala phindu lanthawi yomweyo. Chimene chinaletsedwa chinawonekera kukhala cholakalakika m’maso mwake. Atanyengedwa kotheratu ndi machenjera a Satana, anaswa lamulo la Mulungu. Pamenepo analowetsamo Adamu. Ngakhale kuti sananyegedwe ndi bodza la Satana, iyenso, anasonyeza kupanda chiyamikiro kwakukulu kaamba ka chikondi cha Mulungu. Iye ananyozera umutu wa Yehova nasankha kugwirizana ndi mkazi wake wopandukayo.—Gen. 3:6; 1 Tim. 2:13, 14.
3. (a) Kodi ndinkhani yowonjezereka yotani imene ikugwirizanitsidwa kwambiri ndi chiukiro cha Satana pa ulamuliro wa Yehova? (b) Kodi ndani amene akuyambukiridwa nayo?
3 Chiukiro cha Satana pa ulamuliro wa Yehova sichinaimire pa zimene zinachitikira mu Edeni. Chipambano chake cha chiwonekere kumeneko chinatsatiridwa ndi kukaikira kukhulupirika kwa anthu ena kwa Yehova. Pamenepa, ichi, chinakhala chophatikizidwa kwambiri monga nkhani yachiwiri. Chitokoso chake chinakula kuphatikizapo ponse pawiri ana a Adamu ndi ana onse auzimu a Mulungu, ngakhale Mwana wobadwa yekha wokondedwa kwambiri wa Yehova. M’masiku a Yobu, Satana anatsutsa kuti otumikira Yehova anatero osati chifukwa chakuti amakonda Mulungu ndi njira yake ya kulamulira, koma kaamba ka zifukwa zadyera. Iye anatsutsa kuti, pamene achititsidwa kukumana ndi mavuto, onse akagonjera ku zilakolako zadyera. Kodi iye analondola?—Yobu 1:6-12; Chiv. 12:10.
Mmene Anayankhira ku Nkhaniyo
4. Kodi nchifukwa ninji anthu ambiri sanachirikize ulamuliro wa Yehova?
4 Yehova sanalandule kuthekera kwakuti ena akagwirizana ndi Satana m’chipanduko. Kunena zowona, popereka chiweruzo mu Edeni, Mulungu anasonya kwa awo amene akapanga ‘mbewu ya njoka.’ (Gen. 3:15) Afarisi amene analinganiza mwachiwembu imfa ya Yesu ndi Yudase Isikariote, amene anapereka Kristu, anali pakati pa amenewa. Iwo sanachite mwanjira ya kuphophonya chabe asanazindikire. Iwo anadziwa chimene chinali cholungama, ndipo mwadala anatenga kaimidwe kotsutsa Yehova ndi atumiki ake. Komabe, ena osawerengeka amene sanachite mogwirizana ndi zofunika za Yehova achita mosadziwa.—Mac. 17:29, 30.
5. (a) Mosafanana ndi Hava, kodi ndimotani mmene awo amene akhala okhulupirika kwa Yehova awonera mawu ake? (b) Kodi ndimotani mmene Nowa anatsimikizirira kukhulupirika kwake, ndipo kodi ndimotani mmene tingapindulire ndi chitsanzo chake?
5 Mosiyana ndi anthu onsewa panali amuna ndi akazi achikhulupiriro amene anadziphunzitsa ponena za Mlengi wawo natsimikizira kukhulupirika kwawo kwa iye monga Wolamulira. Anakhulupirira Mulungu. Anadziwa kuti miyoyo yawo inadalira pa kumvetsera kwa iye ndi kumvera iye. Nowa anali mwamuna wotero. Chotero, pamene Mulungu anati kwa Nowa, “Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga . . . dzipangire wekha chingalawa,” Nowa anagonjera ku chitsogozo cha Yehova. Anthu ena a m’tsiku limenelo, mosasamala kanthu za kupatsidwa chenjezo, anayenda njira yawo yamoyo yanthawi zonse monga ngati kuti panalibe chinthu chachilendo chidzachitika. Koma Nowa anamanga chingalawa chachikulu natanganitsidwa kulalikira kwa ena za njira zolungama za Yehova. Monga momwe cholembedwacho chikunenera, “chotero anachita Nowa, monga mwa zonse anamulamulira iye Mulungu, momwemo anachita.”—Gen. 6:13-22; wonaninso Ahebri 11:7 ndi 2 Petro 2:5.
6. (a) Kodi nchiyaninso chimene chakhalanso chapadera kwa osunga umphumphu? (b) Kodi ndimotani mmene Sara anasonyezera mikhalidwe imeneyi, ndipo kodi ife tingapindule m’njira yotani ndi chitsanzo chake?
6 Kulemekeza kwambiri lamulo lamakhalidwe abwino laumutu, kuphatikizapo kukonda Yehova kwa aliyense, zakhalanso zapadera pakati pa osunga umphumphuwo. Sanakhale ofanana ndi Hava, amene anapita patsogolo pa mwamuna wake. Kapena monga Adamu amene ananyalanyaza lamulo la Yehova. Sara, mkazi wa Abrahamu anasonyeza mikhalidwe yabwino kwambiri iyi. Abrahamu anali “mbuye” wake osati kokha m’mawu ake komanso mumtima. Ndiponso, iye mwini anakonda Yehova ndipo anali mkazi wachikhulupiriro. Limodzi ndi Abrahamu, iye “analindirira mudzi [Ufumu wa Mulungu] wokhala nawo maziko, mmisiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu.”—1 Pet. 3:5, 6; Aheb. 11:10-16.
7. (a) Kodi Mose anachirikiza ulamuliro wa Yehova pansi pa mikhalidwe yotani? (b) Kodi ndimotani mmene chitsanzo chake chingatipindulitsire?
7 Pafupifupi zaka 430 Abrahamu atachoka kwawo, Mose anachirikiza ulamuliro wa Yehova moyang’anizana maso ndi maso ndi Farao wa Igupto. Sikuti Mose anali wodzidalira. Mmalo mwake, iye anakaikira luso lake la kulankhula bwino mokwanira. Koma anamvera Yehova. Mwa chichirikizo cha Yehova ndi chithandizo cha mbale wake Aroni, Mose anapereka uthenga wa Yehova mobwerezabwereza kwa Farao. Farao anali wouma khosi. Ngakhale ena a ana a Israyeli anali osuliza mwaukali kwa Mose. Koma mokhulupirika Mose anachita chirichonse chimene Yehova anamlamulira, ndipo kupyolera mwa iye Aisrayeli anawomboledwa kutuluka mu Igupto.—Eks. 7:6; 12:50, 51.
8. (a) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti kukhulupirika kwa Yehova kumaphatikizapo zoposa kuchita chimene Mulungu wanena mwachindunji m’malemba? (b) Kodi ndimotani mmene kuzindikira mtundu uwu wa kukhulupirika kungatithandizire kugwiritsira ntchito 1 Yohane 2:15?
8 Awo amene anali okhulupirika kwa Yehova sanalingalire kuti zokha zimene zinali zofunika zinali kugwirizana ndi kalata ya chilamulo, kumvera zokha zimene Mulungu analemba. Pamene mkazi wa Potifara anayesa kunyenga Yosefe kuchita naye chigololo, panalibe chilamulo cholembedwa chochokera kwa Mulungu chomwe chinaletsa mwachindunji kuchita chigololo. Koma zokha zimene Yosefe anadziwa za makonzedwe aukwati zokhazikitsidwa ndi Yehova mu Edeni, iye anazindikira kuti kuchita chigololo ndi mkazi wa mwamuna wina kukanakhala kosakondweretsa kwa Mulungu. Yosefe sanali wokondwera kuyesa mlingo umene Mulungu akanamulola kukhala monga Aigupto. Anachirikiza njira za Yehova mwa kusinkhasinkha pa zochita za Mulungu ndi anthu ndiyeno mwachikumbumtima anagwiritsira ntchito chimene anachilingalira kukhala chifuniro cha Mulungu.—Gen. 39:7-12; yerekezerani Salmo 77:11, 12.
9. Kodi ndimotani mmene Mdyerekezi mobwerezabwereza watsimikizidwira kukhala wabodza m’chinenezo chimene anadzutsa m’tsiku la Yobu?
9 Ngakhale ngati atayesedwa kwambiri awo amene amadziwadi Yehova samafufunuka kwa iye. Satana ananena kuti ngati Yobu akanataikiridwa ndi chuma kapena anavutika kuthupi, ngakhale ameneyo amene Yehova analankhula momtamanda akanachoka kwa Mulungu. Koma Yobu anatsimikizira Mdyerekezi kukhala wabodza, ndipo iye anatero ngakhale sanadziwe chimene anali kuvutikira ndi mavuto onsewa omkweteza. (Yobu 2:3, 9, 10) Akumayesayesabe kutsimikizira mfundo yake, pambuyo pake Satana anachititsa mfumu yokwiyitsidwa ya Babulo kuopseza Ahebri achichepere atatu ndi imfa m’ng’anjo ya moto ngati sanagwade ndi kulambira pamaso pa fano loimikidwa ndi mfumu. Atakakamizidwa kusankha pakati pa lamulo la mfumu ndi lamulo la Yehova lotsutsa kulambira mafano, iwo ananena mwamphamvu kuti iwo anatumikira Yehova ndi kuti anali Wolamulira wawo Wamkulu. Chamtengo wapatali koposa moyo kwa iwo chinali kukhulupirika kwa Mulungu.—Dan. 3:14-18.
10. Kodi ndimotani mmene kuliri kothekera kwa ife anthu opanda ungwiro kutsimikizira kuti tiridi okhulupirika kwa Yehova?
10 Kodi tinene kuti kuchokera pa zimenezi kuti akhale wokhulupirika kwa Yehova munthuyo ayenera kukhala wangwiro, kuti amene amapanga zophophonya walephera kotheratu? Kutalitali! Baibulo limatiuza mwachindunji za zimene Mose analephera. Yehova anakwiya, koma sanakane Mose. Atumwi, ngakhale kuti anali ndi chitsanzo chabwino m’mbali zambiri, anali ndi zofooka zawo. Kukhulupirika kumafunikiritsa kumvera kwenikweni kochokera mu mtima. Koma, polingalira cholowa chathu cha kupanda ungwiro, Yehova ali wokondwera ngati sitinyalanyaza mwadala chifuniro chake m’njira iriyonse. Ngati, chifukwa cha kufooka, tilowa m’cholakwa, kuli kofunika kuti tilape mowona mtima ndipo chotero osapanga chizolowezi chauchimowo. Titatero timasonyeza kuti timakondadi chimene Yehova amati nchabwino ndi kuda chimene amatisonyeza kukhala choipa. Pamaziko a chikhulupiriro chathu munsembe ya Yesu yotetezera machimo yofunikayo, tingakhoze kusangalala ndi kaimidwe koyera pamaso pa Mulungu.—Amosi 5:15; Mac. 3:19; Aheb. 9:14.
11. (a) Kodi ndani pakati pa anthu amene anasunga kudzipereka kwaumulungu kwangwiro, ndipo kodi ichi chinatsimikizira chiyani? (b) Kodi ndimotani mmene timathandizidwira ndi chimene anachita?
11 Komabe, kodi kungakhale kwakuti kudzipereka kwaumulungu kwangwiro sikuli kotheka konse kwa anthu? Kwa zaka zokwanira 4 000 yankho la funsoli linali “chinsinsi chopatulika.” (1 Tim. 3:16) Adamu, ngakhale kuli kwakuti analengedwa ali wangwiro, sanapereke chitsanzo changwiro cha kudzipereka kwaumulungu. Kodi ndani akanatero? Ndithudi palibe aliyense wa mbadwa zake zochimwa akanatero. Yesu Kristu anali munthu yekha amene akanatero. Zimene Yesu anakwaniritsa zinatsimikizira kuti Adamu, amene anali ndi mikhalidwe yabwino yowonjezereka, akanasunga umphumphu wangwiro ngati akanafuna kutero. Cholakwacho sichinali m’ntchito ya kulenga ya Mulungu. Cotero Yesu Kristu ali chitsanzo chimene timafunafuna kutsanzira m’kusonyeza osati kokha kumvera malamulo a Mulungu komanso kulambira kwathu Yehova, Wolamulira wa Chilengedwe chonse.
Kodi Yankho Lathu la Ife Eni Nlotani?
12. Kodi nchifukwa ninji tiyenera nthawi zonse kukhala ogalamuka ponena za mkhalidwe wathu kulinga ku ulamuliro wa Yehova?
12 Aliyense wa ife lerolino ayenera kuyang’anizana ndi nkhani ya chilengedwe chonse. Sitingaizembe. Ngati talankhula poyera kuti tiri ku mbali ya Yehova, Satana amatipanga chandamale. Amabweretsa chitsenderezo kuchokera kumbali yonse yodziwika ndipo adzapitirizabe kutero kufikiradi kumapeto a dongosolo loipa iri lazinthu. Sitiyenera kuchepetsa kudikira kwathu. (1 Pet. 5:8) Khalidwe lathu limasonyeza pamene taima m’nkhani yaikuluyi.
13. (a) Kodi pali chiyani chimene chanenedwa ponena za magwero a mabodza ndi kuba chimene chiyenera kutichititsa kupewa? (b) Yankhani mafunso pa mapeto a ndime ino, limodzi panthawi imodzi, ponena za mikhalidwe imene imachititsa anthu ena kukhoterera kukuchita cholakwa.
13 Sitingakhoze kuwona mkhalidwe wa kusakhulupirika monga wosanunkha kanthu kokha chifukwa chakuti uli wofala m’dziko. Kusunga umphumphu kumafuna kuti tigwiritsire ntchito njira zolungama za Yehova mu nkhani iriyonse m’moyo. Mwachitsanzo, lingalirani zotsatirazi:
(1) Satana anagwiritsira ntchito bodza kulowetsa makolo athu oyambirira mu uchimo. Anafikira kukhala “atate wa bodza.” (Yohane 8:44)
Kodi achichepere nthawi zina amalephera pansi pa mikhalidwe yotani kukhala owona kwa makolo awo? Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwa achichepere Achikristu kupewa izi? (Miy. 6:16-19)
Kodi ndi machitachita a bizinesi otani amene angachititse munthu kufanana ndi “atate wabodza” mmalo mwa kufanana ndi Mulungu wa chowonadi? (Mika 6:11, 12)
Ngati tinena zinthu kupereka thamo la chiphamaso kwa ife eni, kodi zimenezo nzolakwa ngati sizivulaza munthu aliyense? (Sal. 119:163; yerekezerani Machitidwe 5:1-11.)
Ngati munthu alowa m’cholakwa chachikulu, kodi nchifukwa ninji kuli kofunika osayesa kuchiphimba mwa kutembenukira ku mabodza? (Miyambo 28:13)
(2) Pamene Hava ndiyeno Adamu anachita mosonkhezeredwa ndi Satana kupanga zosankha za iwo eni ponena za chabwino ndi choipa, chinthu choyamba chimene anachita chinali kutenga kanthu kena kamene sikanali kawo. Anakhala mbala.
Kodi kuba sikolakwa ngati munthuyo ali wosowa kapena ngati amene akuberedwa zinthuyo ali nzambiri? (Miy. 6:30, 31; 1 Pet. 4:15)
Kodi nzokanizidwa pang’ono ngati chiri chizolowezi chofala kumene timakhala kapena ngati chimene chatengedwa chiri chochepa? (Aroma 12:2; Aef. 4:28; Luka 16:10)
14, 15. (a) Pa mapeto a Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu kodi ndichiyeso chanji chimene chidzafika kwa anthu onse? (b) Kodi ndimotani mmene chimene tichita tsopano chidzayambukirira zotulukapo kwa ife panthawiyo?
14 Mkati mwa Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu, Satana ndi ziwanda zake adzakhala m’phompho, osakhoza kusonkhezera anthu. Ha nchimasuko chotani nanga mmene chimenecho chidzakhalira! Koma pambuyo pa zaka chikwi, adzamasulidwa kwa kanthawi. Satana ndi omtsatira adzabweretsa chitsenderezo pa “oyera mtima,” anthu obwezeretsedwa amenewo amene asunga umphumphu wawo. Iye adzayandikira kwa iwo monga wochita nkhondo motsutsana ndi “mzinda wokondedwa,” Yerusalemu watsopano wakumwamba, mwa kuyesa kufafaniza chilungamo chimene wakhazikitsa padziko lapansi.—Chiv. 20:7-10.
15 Kuli kwachiwonekere kuti, monga m’nthawi zakale, Satana adzagwiritsira ntchito chinyengo, limodzi ndi zosonkhezera dyera ndi kunyada, kunyengera anthu ku machitachita a kusakhulupirika kwa Yehova. Ngati uli mwayi wathu kukhala ndi moyo panthawiyo, kodi ndimotani mmene monga anthu tidzachitira? Kodi mitima yathu idzakhala kuti ponena za nkhani yachilengedwe chonse? Popeza anthu onse panthawiyo adzakhala angwiro, kachitidwe kalikonse ka kusakhulupirika kadzakhala kadala ndipo kadzachititsa chiwonongeko chosatha. Chotero kuti titsimikizire kukhala okhulupirika panthawiyo, ha ndi kofunika chotani nanga mmene kuliri kukulitsa chizolowezi cha kulabadira msanga ndi motsimikizira tsopano ku chitsogozo chirichonse chimene Yehova atipatsa, kaya kupyolera mwa Mawu ake kapena kupyolera mwa gulu lake! Mwa kutero, tikusonyeza kudzipereka kwathu kowona kwa iye monga Wolamulira Wachilengedwe chonse.
Makambitsarano Openda
● Kodi ndinkhani yaikulu iti imene cholengedwa chonse chiyenera kuyang’anizana nayo? Kodi ndimotani mmene timalowetsedweramo?
● Kodi nchiyani chiri chapadera ponena za njira m’zimene aliyense wa amuna ndi akazi osonyezedwa patsamba 49 anatsimikizirira umphumphu kwa Yehova?
● Kodi nchifukwa ninjii kuli kofunika kuti tikhale osamala tsiku ndi tsiku kulemekeza Yehova mwa makhalidwe athu?
[Chithunzi patsamba 49]
Anachirikiza Ulamuliro wa Yehova
Nowa
Sara
Mose
Yosefe
Yobu
Kodi Ndimotani Mmene Tingapindulire ndi Chitsanzo Chawo?