Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • uw mutu 7 tsamba 55-61
  • Zimene Timaphunzira m’Kuloleza kwa Mulungu Kuipa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Timaphunzira m’Kuloleza kwa Mulungu Kuipa
  • Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kaamba ka Dzina Lake Lalikulu
  • ‘O Kuyatu Nanga kwa Nzeru za Mulungu!’
  • Mwai wa Kusonyeza Kudzipereka Kwathu
  • Zimene Timaphunzira Chifukwa Chakuti Mulungu Walola Kuipa
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Yehova Ndi Mulungu Woleza Mtima
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Lingalirani Zitsanzo za Kuleza Mtima
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Cholinga cha Yehova Chidzakwaniritsidwa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
uw mutu 7 tsamba 55-61

Mutu 7

Zimene Timaphunzira m’Kuloleza kwa Mulungu Kuipa

1. (a) Ngati Yehova akanawononga mofulumira opandukawo mu Edeni, kodi zimenezo zikanatiyambukira motani? (b) Mmalo mwake, kodi ndimakonzedwe achikondi otani amene Yehova wawachititsa kupezeka kwa ife?

MOSASAMALA KANTHU za mavuto amene tingakumane nawo m’moyo, kubadwa kwathu sikunali chisalungamo chirichonse ku mbali ya Mulungu. Iye anapatsa kwa anthu oyamba ungwiro nawapatsa Paradaiso monga kwawo. Ngati iye akanawapha nthawi yomweyo pambuyo pa kupanduka kwawo, sipakanakhala fuko laumunthu monga momwe tikulidziwira ndi utenda wake, umphawi ndi upandu. Komabe, mwachifundo, Yehova analola Adamu ndi Hava kukhala ndi banja asanafe, ngakhale kuli kwakuti akanakhala ndi cholowa cha kupanda ungwiro. Kupyolera mwa Kristu anapanga makonzedwe kaamba ka mbadwa za Adamu zija zosonyeza chikhulupiriro kukhala ndi chimene Adamu anataya—moyo wamuyaya pansi pa mikhalidwe imene ikatheketsa chisangalalo chachikulu koposa cha moyo.—Deut. 32:4, 5; Yoh. 10:10.

2. Kodi zonsezi zinachitidwa kokha kaamba ka chipulumutso chathu?

2 Mapindu a chimenechi kwa ife mwachindunji ali osayezeka. Koma kuchokera ku cholembedwa cha Baibulo timaphunzira kuti chinthu china chofunika kwambiri kuposa chipulumutso cha ife eni chinaphatikizidwa.

Kaamba ka Dzina Lake Lalikulu

3. Kodi nchiyani chinali pachiyeso mogwirizana ndi kukwaniritsidwa kwa chifuno cha Yehova kaamba ka dziko lapansi ndi anthu?

3 Dzina la Yehova, ulemu wake monga Wolamulira wa Chilengedwe chonse ndi Mulungu wa chowonadi, linaphatikizidwa m’kukwaniritsidwa kwa chifuno chake ponena za dziko lapansi ndi anthu. Chifukwa cha malo a Yehova, mtendere ndi kulemerera kwa chilengedwe chonse zimafunikiritsa kuti dzina lake lipatsidwe ulemu wokwanira umene limayenerera ndi kuti onse akhale omvera kwa iye.

4. Kodi kwenikweni chifunocho chinaphatikizapo chiyani?

4 Pambuyo pa kulenga Adamu ndi Hava anawapatsa gawo lochita. Anamveketsa kuti chifuno chake sichinali kokha kugonjetsa dziko lonse lapansi, mwa kutero kufutukula malire a Paradaiso, koma kulidzadza ndi mbadwa za mwamuna ndi mkazi woyamba, Adamu ndi Hava. (Gen. 1:28) Kodi chifuno ichi chinayenera kulephera chifukwa cha uchimo wawo, ndi chotulukapo cha kutonzedwa kwa dzina la Mulungu?

5. (a) Mogwirizana ndi Genesis 2:17, kodi ndiliti pamene aliyense wakudya za mu mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa akafa? (b) Kodi ndimotani mmene Yehova anakwaniritsira zimenezo, kwinaku akumalemekeza chifuno chake ponena za kudzadza dziko lapansi ndi anthu?

5 Yehova anali atachenjeza Adamu kuti ngati mosamvera anadya za ku mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa akafa ndithu “m’tsiku” limene akadya. (Gen. 2:17) Mowonadi ku mawu a Mulungu, patsiku lenileni lakuchimwa kwa Adamu Yehova anaweruza ochimwawo napereka chilango cha imfa. Chilangocho chinali chosapeweka. Mwa lingaliro la Mulungu, mwa chiweruzo, Adamu ndi Hava anafa tsiku lomwelo. (Yerekezerani Luka 20:37, 38.) Koma kuti akwaniritse chifuno cha iye mwini cholongosoledwa chonena za kudzadza dziko lapansi, Yehova anawalola kutulutsa banja iwo asanafe kwenikweni. Komabe, mwa lingaliro la Mulungu la kuwona zaka 1000 monga tsiku limodzi, pamene moyo wa Adamu unatha pa zaka 930, imfayo inachitika mkati mwa “tsiku” limodzi. (Gen. 5:3-5; yerekezerani ndi Salmo 90:4; 2 Petro 3:8.) Chotero kukhulupirika kwa Yehova kunachirikizidwa ponena za nthawi imene chilangocho chikaperekedwa, ndipo chifuno chake cha kudzadza dziko lapansi ndi ana Adamu sichinalepheretsedwe. Koma chatanthauza kuti, kwa kanthawi, anthu auchimo aloledwa kukhala ndi moyo.

6, 7. (a) Kodi nchiyani chimene Eksodo 9:15, 16 amasonyeza ponena za chifukwa chimene Yehova amalolera oipa kupitirizabe kwa kanthawi? (b) Ponena za Farao, kodi ndimotani mmene mphamvu ya Yehova inasonyezedwera ndipo kodi ndimotani mmene dzina Lake linadziwikitsidwira? (c) Chotero kodi nchiyani chimene chidzakhala chotulukapo pamapeto a dongosolo loipa lamakonoli?

6 Zimene Yehova ananena kwa wolamulira wa Igupto m’masiku a Mose zikusonyezanso chifukwa chake Yehova walolera kuipa kupitirizabe kwa kanthawi. Pamene Farao anakaniza kutuluka kwa ana a Israyeli kuchoka mu Igupto, Yehova sanamkanthe panthawi yomweyo. Miliri khumi inabweretsedwa padzikolo, kusonyeza mphamvu ya Yehova m’njira zodabwitsa ndi zosiyanasiyana. Pochenjeza za wachisanu ndi chiwiri Yehova anauza Farao kuti akanatha kufafaniza Farao ndi anthu ake pa dziko lapansi. “Koma ndithu,” Yehova anatero, “chifukwa chake ndakuimika kuti ndikuwonetse mphamvu yanga, ndikuti alalikire dzina langa padziko lonse lapansi.”—Eks. 19:15, 16.

7 Pamene Yehova analanditsa Israyeli, dzina lake linadziwikadi mofala kwambiri. Lerolino, pafupifupi zaka 3500 pambuyo pake, chimene anachita sichinaiwalike. Sikokha kuti dzina lakelo lakuti Yehova linalengezedwa komanso chowonadi chonena za Uyo wokhala ndi dzina limenelo. Ichi chinatsimikizira mbiri ya Yehova ya kukhala Mulungu amene amasunga mapangano ake nachitapo kanthu mmalo mwa atumiki ake. Kunasonyeza kuti chifukwa cha mphamvu zake zonse palibe chimene chingalepheretse chifuno chake. Champhamvudi chidzakhala chiwonongeko chikudzacho cha dongosolo lonse loipa, lowoneka ndi losawoneka. Kusonyezedwa kwa mphamvu yonse kumeneko ndi ulemerero umene umabweretsa pa dzina la Yehova sizidzaiwalika konse m’mbiri yachilengedwe chonse. Mapindu ake adzakhala osatha!—Ezek. 38:23; Chiv. 19:1, 2.

‘O Kuyatu Nanga kwa Nzeru za Mulungu!’

8. Kodi ndi mbali zowonjezereka zotani zimene Paulo akutichichiza kupenda?

8 M’kalata yake kwa Aroma, mtumwi Paulo anadzutsa funso iri: “Kodi chiripo chosalungama ndi Mulungu?” Ndiyeno akuyankha mwa kugogomezera chifundo cha Mulungu ndi mwa kutchula chimene Yehova ananena kwa Farao. Iye akukumbutsanso chenicheni chakuti anthufe tiri ofanana ndi dongo m’manja a wowumba mbiya. Kodi dongo limadandaula nayo njira mmene lagwiritsiridwira ntchito? Paulo akuwonjezera kuti: “Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna iye kuwonetsa mkwiyo wake, ndi kudziwitsa mphamvu yake, analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chiwonongeko? Ndi kuti Iye akadziwitse ulemerero wake waukulu pa zotengera zachifundo, zimene iye anazikonzeratu kuulemerero, ndi ife amenenso Iye anatiitana, siamwa Ayuda okhaokha, komanso a mwa anthu amitundu?”—Aroma 9:14-24.

9. (a) Kodi ndani amene ali “zotengera zamkwiyo zokonzekera chiwonongeko”? (b) Kodi nchifukwa ninji Yehova wasonyeza kuleza mtima kokulira pamaso pa udani wawo, ndipo kodi ndimotani mmene chotulukapo chotsirizira chidzakhalira kaamba ka ubwino wa awo omkonda?

9 Chiyambire pamene Yehova ananena mawu aulosi olembedwa pa Genesi 3:15, Satana ndi mbewu yake akhala “zotengera za mkwiyo zokonzekera chiwonongeko.” Mkati mwa nthawi yonseyo Yehova wasonyeza kuleza mtima. Oipa anyozera njira zake; azunza atumiki ake, ngakhale kupha Mwana wake. Koma Yehova wasonyeza kudziletsa kwakukulu, nchotulukapo chaphindu losatha kwa atumiki ake. Chilengedwe chonse chakhala ndi mwayi wa kuwona zotulukapo zowononga za kupandukira Mulungu. Panthawi imodzimodziyo, imfa ya Yesu inapereka njira yolanditsira anthu omvera ndi yowonongera ‘ntchito za Mdyerekezi.’—1 Yoh. 3:8; Aheb. 2:14, 15.

10. Kodi nchifukwa ninji Yehova wapitirizabe kulekerera oipa mkati mwa zaka 1900 zapitazo?

10 Mkati mwa zaka zoposa 1900 kuyambira pa chiukiriro cha Yesu Yehova walekeranso “zotengera za mkwiyo” kuimika chiwonongeko chawo. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti wakhala akukonzekera mbali yachiwiri ya mbewu ya mkazi, awo amene adzagwirizana ndi Yesu Kristu mu Ufumu wakumwamba. (Agal. 3:29) Okwanira 144 000 amenewa, ndiwo “zotengera zachifundo” zonenedwa ndi mtumwi Paulo. Choyamba, anthu aliyense payekha payekha ochokera pakati pa Ayuda anaitanidwa kupanga kagulu kameneka. Kenako Asamariya odulidwa anawonjezeredwako ndipo, potsirizira, anthu a amitundu Yachikunja. Mwa kuleza mtima kokulira Yehova wakwaniritsa chifuno chake, wosakakamiza aliyense kumtumikira, koma kupereka madalitso akulu pa awo amene anavomereza moyamikira makonzedwe ake achikondi. Tsopano kukonzekeretsedwa kwa kagulu ka kumwamba kameneko pafupifupi kwatha.

11. Kodi ndikagulu kena kati kamene tsopano kakupindula ndi kuleza mtima kwa Yehova?

11 Koma bwanji ponena za okhala pa dziko lapansi? M’nthawi yokwanira mabiliyoni adzaukitsidwa monga nzika zadziko lapansi za Ufumu. Ndiponso, makamaka chiyambire 1935 C.E. kuleza mtima kwa Yehova kwatheketsa kusonkhanitsidwa kwa “khamu lalikulu” lochokera mwa mitundu yonse ndi cholinga cha chipulumutso chawo.—Chiv. 7:9, 10; Yoh. 10:16.

12. (a) Monga chotulukapo, kodi nchiyani chimene taphunzira ponena za Yehova iyemwiniyo? (b) Kodi mukulabadira motani ponena za mmene Yehova wasamalirira nkhanizi?

12 Kodi pakhala chisalungamo chirichonse m’zonsezi? Ndithudi ayi! Ngati Mulungu aimika chiwonongokeko cha oipa, “zotengera za mkwiyo,” kuchitira kuti asonyeze chifundo kwa ena mogwirizana ndi chifuno chake, kodi ndimotani mmene aliyense moyenerera angadandaulire? Mmalo mwake, pamene tikuwona kukwaniritsidwa kwa chifuno chake, timaphunzira zambiri za Yehova iye mwiniyo. Timazizwa ndi mbali zambiri zaumunthu wake zimene zavumbulutsidwa—chilungamo chake, chifundo chake, kuleza mtima kwake, kusiyanasiyana kwa nzeru zake. Kusamalira mwanzeru kwa Yehova nkhaniyi kudzakhala kosatha monga umboni wa chenicheni chakuti njira yake ya kulamulira ndiyo yabwino koposa. Limodzi ndi mtumwi Paulo tikuti: “Ha! kuya kwake kwa kulemera ndi kwanzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!”—Aroma 11:33.

Mwai wa Kusonyeza Kudzipereka Kwathu

13. (a) Pamene tilowa m’vuto ife enife kodi ndimwayi wotani umene umaperekedwa kwa ife? (b) Kodi nchiyani chimene chidzathandiza kuyankha mwanzeru?

13 Pali mikhalidwe imene imaphatikizapo kuvutika kwa munthu mwini kwenikweni chifukwa chakuti Mulungu sanawonongebe oipa ndi kudzetsa kubwezeretsedwa konenedweratu kwa anthu. Kodi nchiyani chimene chiri kulabadira kwathu ku zimenezo? Kodi timawonamo mwai wa kukhala ndi mbali m’kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova pa chitonzo ndi kutsimikizira Mdyerekezi kukhala wabodza? Tingathe kulimbikitsidwa kwambiri kutero mwa kukumbukira uphungu wakuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miy. 27:11) Satana, amene amatonza Yehova, ananeneza kuti ngati anthu atataikiridwa ndi chuma chakuthupi kapena atadwala nthenda yakuthupi adzasuliza Mulungu, ngakhale kumtukwana. (Yobu 1:9-11; 2:4, 5) Tisangalatsa mtima wa Yehova pamene, mwa kukhulupirika kwathu kwa Mulungu poyayang’anizana ndi mavuto, tisonyeza kuti zimenezo siziri zowona kwa ife. Tiri ndi chidaliro chokwanira kuti Yehova ali ndi chikondi chachikulu kwa atumiki ake ndi kuti, monga momwe zinaliri kwa Yobu, m’nthawi yokwanira Yehova adzatipatsa mphoto moolowa manja ngati titsimikizira kukhala okhulupirika.—Yak. 5:11; Yobu 42:10-16.

14. Ngati tidalira pa Yehova pamene tikumana ndi ziyeso, kodi ndimapindu ena otani amene angadze kwa ife?

14 Ngati mwachidaliro tiyembekezera mwa Yehova pamene tikumana ndi mayeso omvetsa chisoni, tingakhoze kukulitsa mikhalidwe yabwino kopambana. Monga chotulukapo cha zinthu zimene Yesu anavutika nazo, “anaphunzira kumvera” mwa njira imene sanadziwe ndi kalelonse. Ifenso, tingaphunzire—kukulitsa kuleza mtima, chipiriro ndi kuzindikira mozama njira zolungama za Yehova. Kodi ife moleza mtima tidzavomereza kuphunzitsidwa kumeneko?—Aheb. 5:8, 9; 12:11; Yak. 1:2-4.

15. Pamene tipirira mavuto modekha, kodi ndimotani mmene ena angapindulire?

15 Ena adzawona zimene tikuchita. Chifukwa cha zimene tikukumana nazo chifukwa cha kukonda chilungamo, ena a iwo m’nthawi yokwanira angafike pa kuzindikira amene ali kwenikweni “abale” a Kristu lerolino, ndipo mwa kugwirizana ndi “abale” akewo m’kulambira angakhoze kulowa mu mzera womka ku madalitso a moyo wamuyaya. (Mat. 25:34-36, 40, 46) Yehova ndi Mwana wake amafuna kuti iwo akhale ndi mwayi umenewo. Kodi ife timatero? Kodi tiri ofunitsitsa kupirira mavuto kuti utithekere?

16. Kodi ndimotani mmene lingaliro lathu lamavuto aumwini otero liriri logwirizana ndi nkhani yachigwirizano?

16 Ha ndikwabwino kwambiri chotani nanga m’mene kuliri pamene ife motero tiwona ngakhale mikhalidwe yovuta m’moyo monga mwai wosonyezera kudzipereka kwathu kwa Yehova kudzanso njira yokhalira ndi phande m’kuchitidwa kwa chifuniro chake! Kuchita kwathu motero kungapereke umboni wakuti tikupitadi patsogolo kumka ku chigwirizano ndi Mulungu ndi Kristu chimene Yesu anapempherera Akristu onse owona.—Yoh. 17:20, 21.

Makambitsirano Openda

● Pamene akuloleza kuipa, kodi ndimotani mmene Yehova moyenerera wasonyezera ulemu waukulu kaamba ka dzina la iye mwini?

● Kodi ndimotani mmene kulekerera “zotengera zamkwiyo” kwa Mulungu kunakhozetsera chifundo chake kufika mpaka kwa ife?

● Kodi nchiyani chimene tiyenera kuyesayesa kuwona m’mikhalidwe yophatikizapo kuvutika imene ife enife timakumana nayo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena