Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 19
  • Kuphunzitsa Mkazi wa ku Samariya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuphunzitsa Mkazi wa ku Samariya
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Asamariya Ambiri Akhulupilira
  • Yesu Analalikira Mayi wa ku Samariya
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Yesu Anakumana ndi Mayi Pachitsime
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Ndi Mkazi pa Chitsime
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Madzi Opatsa Moyo
    Galamukani!—2009
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 19

Mutu 19

Kuphunzitsa Mkazi wa ku Samariya

PAULENDO wawo kuchokera ku Yudeya kumka ku Galileya, Yesu ndi ophunzira ake akuyenda kudutsa chigawo cha Samariya. Atatopa ndi ulendowo, pafupifupi dzuŵa liri pamutu iwo akuima kuti apume cha pachitsime cha pafupi ndi mzinda wa Sukari. Chitsime chimenechi chinakumbidwa kalero zaka mazana ambiri apitawo ndi Yakobo, ndipo chidakalipobe kufikira lerolino, pafupi ndi mzinda wamakono wa Nablus.

Pamene Yesu akupuma panopo, ophunzira ake akumka kumzinda kukagula chakudya. Pamene mkazi wina Wachisamariya adza kudzatunga madzi, iye akumupempha kuti: “Undipatse ine ndimwe.”

Kaŵirikaŵiri Ayuda ndi Asamariya samadyerana chifukwa cha tsankhu lalikulu. Chotero, modabwa, mkaziyo akufunsa kuti: “Bwanji inu muli Myuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi wa ku Samariya?”

“Ukadadziŵa,” Yesu akuyankha motero, “iye amene alinkunena ndi iwe, ndipatse ndimwe ine; ukadapempha iye, ndipo akanakupatsa madzi a moyo.”

“Ambuye,” iye akuyankha motero, “mulibe chotungira madzi, ndi chitsime chiri chakuya ndipo mwatenga kuti madzi amoyo? kodi muli wamkulu ndi atate wathu Yakobo amene anatipatsa ife chitsimechi, namwamo iye yekha, ndi ana ake, ndi zoŵeta zake?”

“Yense wakumwako madzi aŵa adzamvanso ludzu,” Yesu akutero. “Koma iye wakumwa madzi amene ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthaŵi zonse; koma madzi amene ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira kumoyo wosatha.”

“Ambuye, ndipatseni madzi amene, kuti ndisamve ludzu, kapena ndisadze kuno kudzatunga,” mkaziyo akuyankha motero.

Tsopano Yesu akuti kwa iye: “Muka, kamuitane mwamuna wako, nudze kuno.”

“Ndiribe mwamuna,” iye akuyankha motero.

Yesu akuvomereza mawu akewo. “Wanena bwino, kuti mwamuna ndiribe; pakuti wakhala nawo amuna asanu ndipo iye amene ukhala naye tsopano sali mwamuna wako.”

“Ambuye, ndizindikira kuti muli mneneri,” mkaziyo akutero mozizwa. Povumbula chikondwerero chake chauzimu, iye akusonyeza kuti Asamariya “analambira m’phiri ili [Gerizimu, limene liri pafupi]; ndipo inu [Ayuda] munena, kuti m’Yerusalemu muli malo oyenera kulambiramo anthu.”

Komabe, malo olambilira saali chinthu chofunika, Yesu akusonyeza motero. “Ikudza nthaŵi,” iye akutero, “imene olambira owona adzalambira Atate mumzimu ndi m’chowonadi; pakuti Atate afuna otero akhale olambira ake. Mulungu ndiye Mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m’chowonadi.”

Mkaziyo akuchititsidwa chidwi kwambiri. “Ndidziŵa kuti Mesiya adza wotchedwa Kristu,” iye akutero. “Akadzadza iyeyu, adzatiuza zonse.”

“Ine wakulankhula nawe ndine amene,” Yesu akulengeza motero. Tangoganizani za iko! Mkazi ameneyu amene akudza masana kudzatunga madzi, mwinamwake kuti apeŵe kuwonana ndi akazi a m’tauniyo amene amamnyoza chifukwa cha njira yake ya moyo, akuyanjidwa m’njira yodabwitsa ndi Yesu. Iye akumuuza mwachindunji zimene sanaululepo poyera kwa wina aliyense. Ndi zotulukapo zotani?

Asamariya Ambiri Akhulupilira

Pobwera kuchokera ku Sukari ndi chakudya, ophunzira ake akupeza Yesu pachitsime cha Yakobo pamene anali atamsiya, ndi pamene tsopano iye akulankhula ndi mkazi wa ku Samariya. Pamene ophunzirawo afika, mkaziyo akuchoka, akumasiya mtsuko wake wa madzi, namka kumzinda.

Pokondweretsedwa kwambiri ndi zinthu zimene Yesu wamuuza, iye akuuza amuna ena a m’mzindawo kuti: “Tiyeni, mukawone munthu, amene anandiuza zinthu zirizonse ndinazichita.” Pamenepo, m’njira yakuti adzutse chidwi, iye akufunsa kuti: “Ameneyu saali Kristu nanga?” Funsolo likumaliza chifuno chake—amunawo akukadziwonera okha.

Zidakali choncho, ophunzira akufulumiza Yesu kuti adye chakudya chimene abweretsa kuchokera kumzinda. Koma iye akuyankha kuti: “Ndiri nacho chakudya chimene inu simuchidziŵa.”

“Kodi pali wina anamtengera Iye kanthu kakudya?” ophunzirawo akufunsana. Yesu akufotokoza kuti: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha iye amene anandituma ine, ndi kutsiriza ntchito yake. Kodi simunena inu kuti Yatsala miyezi inayi, kudza kumweta?” Komabe, posonya kukututa kwauzimu, Yesu akunena kuti: “Kwezani maso anu, nimuyang’ane m’minda, kuti mwayera kale kufikira kumweta. Wakumweta alandira kulipira, nasonkhanitsa chobala kumoyo wosatha; kuti wofesayo akakondwere pamodzi ndi womwetayo.”

Mwinamwake Yesu angathe kuwoneratu chiyambukiro chachikulu cha kukumana kwake ndi mkazi wa ku Samariyayo—chakuti ambiri akuika chikhulupiliro mwa iye chifukwa cha kuchitira umboni kwa mkaziyo. Iye akuchitira umboni kwa anthu a m’tauniyo, akumati: “Anandiuza ine zinthu zirizonse ndinazichita.” Chifukwa chake, pamene amuna a Sukari akudza kwa iye pachitsimepo, iwo akumpempha kusotsa komweko ndi kulankhula nawo zowonjezereka. Yesu akuvomereza pempholo ndipo akusotsa nawo masiku aŵiri.

Pamene Asamariyawo akumvetsera Yesu, owonjezereka akukhulupilira. Ndiyeno akuti kwa mkaziyo: “Sitikukhulupilira chifukwa cha kulankhula kwako: pakuti tamva tokha, ndipo tidziŵa kuti mpulumutsi wa dziko lapansi ndi iyeyu ndithu.” Ndithudi mkazi wa ku Samariyayo amapereka chitsanzo chabwino cha mmene tingachitire umboni za Kristu mwa kudzutsa chidwi kotero kuti omvetsera adzafufuza zowonjezereka!

Kumbukirani kuti ndimiyezi inayi kututa kusanakhale—mwachiwonekere kututidwa kwa barele, kumene kumachitika m’ngululu ku Palestina. Chotero tsopano mwinamwake ndiye November kapena December. Zimenezi zikutanthauza kuti Paskha wotsatirayo wa 30 C.E., Yesu ndi ophunzira ake anathera miyezi isanu ndi itatu kapena chapompo m’Yudeya akumaphunzitsa ndi kubatiza. Tsopano akunyamuka kumka kuchigawo chakwawo ku Galileya. Kodi nchiyani chimene chikuwayembekezera kumeneko? Yohane 4:3-43.

▪ Kodi nchifukwa ninji mkazi wa ku Samariya akudabwa kuti Yesu walankhula naye?

▪ Kodi Yesu akumphunzitsanji ponena za madzi a moyo ndi kumene ayenera kulambirako?

▪ Kodi ndimotani mmene Yesu akuvumbulira kwa iye ponena za amene iye ali, ndipo nchifukwa ninji kuulula kumeneku kuli kodabwitsa?

▪ Kodi ndiumboni wotani umene mkazi wa ku Samariyayo akuchita ndipo ndi chotulukapo chotani?

▪ Kodi chakudya cha Yesu chiri chogwirizana motani ndi kututa?

▪ Kodi tingatsimikizire motani utali wa uminisitala wa Yesu mu Yudeya pambuyo pa Paskha wa 30 C.E.?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena