Mutu 15
Chozizwitsa Choyamba cha Yesu
LANGOKHALA tsiku limodzi chabe kapena aŵiri chiyambire pamene Andreya, Petro, Yohane, Filipi, Natanayeli, ndipo mwinamwake Yakobo akhala ophunzira a Yesu oyamba. Ameneŵa tsopano ali paulendo wa kwawo kuchigawo cha ku Galileya, kumene onsewo anachokera. Malo a ulendowo ndiwo Kana, tauni ya kwawo kwa Natanayeli, yokhala m’mapiri osati kutali ndi Nazarete, kumene Yesu mwiniyo anakulira. Iwo aitanidwa kudza kuphwando laukwati m’Kana.
Nawonso amake a Yesu adza kuukwatiwo. Monga bwenzi la banja la okwatiranawo, Mariya akuwonekera kukhala atadziphatikiza m’kutumikira zofunika za alendo ochuluka. Chotero iye akufulumira kuwona zosoŵeka zimene akudziŵitsa Yesu: “Alibe vinyo.”
Motero pamene Mariya, m’chenicheni, akupereka lingaliro lakuti Yesu achitepo kanthu ponena za kusoŵeka kwa vinyoyo, Yesu choyamba ali wosafunitsitsa. “Ndiri ndi chiyani ndi inu?” iye akufunsa motero. Monga Mfumu yoikidwa ya Mulungu, iye safunikira kutsogozedwa m’ntchito yake ndi banja kapena mabwenzi. Chotero Mariya mwanzeru akusiya nkhaniyo m’manja mwa mwana wake wamwamunayo, akungonena kokha kwa otumikirawo kuti: “Chimene chirichonse akanena kwa inu, chitani.”
Eya, pali mitsuko yaikulu yamadzi isanu ndi umodzi ya miyala, uliwonse wa imeneyi ungakhale ndi madzi oposa malitala 40. Yesu akulangiza atumikiwo kuti: “Dzazani mitsukoyo ndi madzi.” Ndipo atumikiwo akuidzaza kufikira pamilomo yake. Ndiyeno Yesu akuti: “Tungani tsopano, mupite nawo kwa mkulu wa phwando.”
Mkuluyo akuchititsidwa chidwi ndi mtundu wabwino koposa wa vinyo, wosazindikira kuti wapangidwa mozizwitsa. Poitana mkwati, iye akuti: “Munthu aliyense amayamba kuika vinyo wokoma; ndipo anthu atamwatu, pamenepo wina wosakoma; koma iwe wasunga vinyo wokoma kufikira tsopano lino.”
Ichi ndicho chozizwitsa choyamba cha Yesu, ndipo pakuchiwona kwawo, chikhulupiliro cha ophunzira ake atsopanowo chilimbikitsidwa. Pambuyo pake, limodzi ndi amake ndi abale ake a bambo wina, akuyenda ulendo kumka kumzinda wa Kapernao pafupi ndi Nyanja ya Galileya. Yohane 2:1-12.
▪ Kodi ndiliti mkati mwa uminisitala wa Yesu pamene ukwati m’Kana ukuchitika?
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akukana lingaliro la amake?
▪ Kodi ndichozizwitsa chotani chimene Yesu akuchita, ndipo kodi ndichiyambukiro chotani chimene chiri nacho pa ena?