Mutu 13
Kuphunzira Kuchokera Kuziyeso za Yesu
MWAMSANGA pambuyo pa ubatizo wake, Yesu akutsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu kuloŵa m’chipululu cha Yudeya. Iye ali nzambiri zakuzilingalira, chifukwa chakuti paubatizo wake “miyamba inamtsegukira iye,” kotero kuti azindikire zinthu zakumwamba. Ndithudi, pali zambiri zoti iye azisinkhesinkhe!
Yesu akutha masiku 40 usana ndi usiku m’chipululu ndipo sakudya kanthu kalikonse mkati mwa nthaŵi imeneyi. Pamenepo, pamene Yesu ali wanjala kwambiri, Mdyerekezi akuyandikira kumuyesa, akumati: “Ngati muli mwana wa Mulungu, tauzani kuti miyala iyi isanduke mikate.” Koma Yesu akudziŵa kuti kuli kulakwa kugwiritsira ntchito mphamvu zake zozizwitsa kukhutiritsa zikhumbo za iye mwini. Chotero iye akukana kuyesedwa.
Koma Mdyerekezi sakuleka. Iye akuyesa mwa kafikidwe kena. Iye akupereka chitokoso kwa Yesu cha kulumpha patsindwi la kachisi kotero kuti angelo a Mulungu amlanditse. Koma Yesu akukana chiyeso cha kupanga chisonyezero cha kudziwonetsera chimenecho. Akumagwira mawu Malemba, Yesu akusonyeza kuti kuli kolakwa kuika Mulungu pachiyeso mwa njira imeneyi.
M’chiyeso chachitatu, Mdyerekezi akusonyeza Yesu maufumu onse a dziko mwa njira yozizwitsa ndipo akuti: “Zonse ndikupatsani inu, ngati mudzagwa pansi ndi kundigwadira ine.” Koma kachiŵirinso Yesu akukana kugonjera kuchiyeso cha kuchita cholakwa, akumasankha kukhala wokhulupirika kwa Mulungu.
Tingathe kuphunzira kuchokera kuziyeso za Yesu zimenezi. Mwachitsanzo, izo zimasonyeza kuti Mdyerekezi saali kokha lingaliro loipa, monga momwe anthu ena amanenera, koma kuti iye ali munthu weniweni, wosawoneka. Chiyeso cha Yesu chimasonyezanso kuti maboma onse a dziko ndiwo chuma cha Mdyerekezi. Chifukwa chakuti kodi chiyeso cha Mdyerekezi cha kuwapereka kwa Kristu chikanakhala kwenikweni motani ngati iwo sanalidi ake?
Ndipo talingalirani izi: Mdyerekezi ananena kuti anali wofunitsitsa kupereka mfupo kwa Yesu kaamba kakachitidwe kamodzi ka kulambira, ngakhale kumpatsa maufumu onse adziko. Mdyerekezi angayesedi kutiyesa mwanjira yofananayo, mwinamwake kuika pamaso pathu mwaŵi waukulu wa kupeza chuma cha dziko, ulamuliro, kapena malo antchito. Koma tikakhala anzeru chotani nanga kutsatira chitsanzo cha Yesu mwa kukhala wokhulupirika kwa Mulungu mulimonse mmene chiyesocho, chingakhalire! Mateyu 3:16; 4:1-11; Marko 1:12, 13; Luka 4:1-13.
▪ Kodi ndizinthu ziti zimene mwachiwonekere Yesu akuzisinkhasinkha mkati mwa masiku ake 40 m’chipululu?
▪ Kodi Mdyerekezi akuyesayesa motani kuyesa Yesu?
▪ Kodi tingaphunzirenji kuchokera kuziyeso za Yesu?