Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • uw mutu 4 tsamba 29-37
  • Uyo Amene Aneneri Onse Anamchitira Umboni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Uyo Amene Aneneri Onse Anamchitira Umboni
  • Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chimene Maulosi Amavumbula
  • Kodi Tingasonyeze Motani Chikhulupiriro Chathu mwa Kristu?
  • Iye Amene Aneneri Onse Anamuchitira Umboni
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Kugwirizana kwa Baibulo Lonse
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
  • Mbewu ya Njoka—Yavumbulidwa Motani?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Njira Yokha ya Moyo Wosatha
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
uw mutu 4 tsamba 29-37

Mutu 4

Uyo Amene Aneneri Onse Anamchitira Umboni

1. Kodi zenizeni zonena za kukhalapo kwa Yesu asanakhale munthu zimasonyezanji ponena za unansi wake ndi Yehova?

POLONGOSOLA unansi wachikondi wa iye mwini ndi Yehova, Yesu anati: “Atate akonda Mwana, namuwonetsa zonse azichita yekha.” (Yoh. 5:19, 20) Kuyandikana kwa unansi kumeneku kunayamba panthawi ya kulengedwa kwake, zaka mazana osawerengeka kubadwa kwake monga munthu kusanachitike. Anali Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, mmodzi yekha wolengedwa ndi Yehova mwiniyo. chinthu china chiriconse kumwamba ndi padziko lapansi chinalengedwa kupyolera mwa Mwana wachisamba wokondedwa kwambiri ameneyo. Iye anatumikiranso monga Mawu kapena wolankhulira wa Mulungu, munthu kupyolera mwa amene chifuniro cha Mulungu chinaperekedwera kwa ena. Ameneyu, Mwana amene Mulungu anamkonda mwapadera, anakhala munthu Yesu Kristu.—Akol. 1:15, 16; Yoh 1:14; 12:49, 50.

2. Kodi maulosi a Baibulo amasonya kwa Yesu mokulira chotani?

2 Kubadwa kwake kozizwitsa monga munthu kusanachitike, maulosi makumi ambiri ouziridwa onena za iye analembedwa. Monga momwe mtumwi Petro anatsimikizirira kwa Korneliyo kuti, “Ameneyu aneneri onse amchitira umboni.” (Mac. 10:43) Kumlingo umenewu ntchito ya Yesu mogwirizana ndi kulambira koyera inasonyezedwa m’Baibulo kotero kuti mngelo anauza mtumwi Yohane kuti: “Lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo mzimu wa chinenero.” (Chiv. 19:10) Maulosi amenewo amamdziwikitsa momvekera bwino ndi kusonyeza mbali za chifuno cha Mulungu ponena za iye zimene ziri zokondweretsa kwambiri kwa ife lerolino.

Chimene Maulosi Amavumbula

3. (a) Mu ulosi wa Genesis 3:14, 15, kodi ndani akuimiridwa ndi “chinjoka”? “Mkaziyo”? ‘Mbewu ya njoka’? (b) Kodi nchifukwa ninji ‘kuzunzundidwa kwa njoka m’mutu’ kukakhalira kokondweretsa kwambiri kwa atumiki a Yehova?

3 Woyamba wa maulosi amenewo unalankhulidwa pambuyo pa chipanduko mu Edeni. Unaphatikizidwa m’chiweruzo cha Yehova choperekedwa ku chinjoka. Yehova anati: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Gen. 3:14, 15) Kodi chimenecho chinatanthauzanji? M’nthawi yokwanira ya Mulungu maulosi ena anamveketsa mfundoyi naiwonjezera. Chotero timadziwa kuti munthu amene anali kunenedwayo, monga momwe anaimiridwira ndi chinjoka, ndiye Satana Mdyerekezi. “Mkazi” ndiye gulu lakumwamba lokhulupirika la Yehova iye mwiniyo, limene kwa iye liri lofanana ndi mkazi wokhulupirika. ‘Mbewu ya njoka’ imaphatikizapo ponse pawiri angelo ndi anthu amene amasonyeza mzimu wa Mdyerekezi, awo amene amatsutsa Yehova ndi anthu ake. Chifukwa cha njira imene chinjoka chinagwiritsiridwa ntchito ndi Mdyerekezi mu Edeni, kungakhoze kulingaliridwa kuchokera mu ulosi kuti ‘kuzunzundidwa mutu kwa njoka’ kunasonya ku chiwonongeko chotsirizira cha mwana wopanduka wa Mulungu ameneyu amene waneneza Yehova ndi kubweretsa chisoni chachikulu pa anthu. Koma ponena za kudziwika kwa “mbewu” imene ikachita kuzunzundako, kunakhalabe chinsinsi chopatulika kwanthawi yaitali.—Aroma 16:25, 26.

4. Kodi ndimotani mmene makolo a Yesu anathandizira kum’dziwikitsa monga Mbewu yolojezedwa?

4 Pambuyo pa zaka zokwanira 2,000 za mbiri ya anthu Yehova anapereka chidziwitso china. Anasonyeza kuti Mbewu ikawonekera mu mzera wa banja la Abrahamu. (Gen. 22:15-18) Komabe, mzera wotsogolera ku Mbewu ukadalira osati kokha pa mbadwa zakuthupi koma pa chosankha cha Mulungu. Mosasamala kanthu za ku konda kwa Abrahamu mwana wake Ismaeli, wobadwa mwa mdzakazi Hagara, Yehova mosabisa mawu anati: “Pangano langa ndidzalimbikitsa ndi Isake, amene Sara adzakubalira iwe.” (Gen. 17:18-21; 21:8-12) Pambuyo pake pangano limenelo linatsimikiziridwa, osati kwa mwana wachisamba wa Isake Esau, koma kwa Yakobo, kwa amene kuchokera mafuko 12 a Israyeli anachokerako. (Gen. 28:10-14) M’nthawi yokwanira kunasonyezedwa kuti Mbewu ikabadwa m’fuko la Yuda, m’nyumba ya Davide.—Gen. 49:10; 1 Mbiri 17:3, 4, 11-14.

5. Ngakhale kuchiyambi kwa uminisitala wapadziko lapansi wa Yesu, kodi nchiyaninso chimene chinasonyeza kuti anali Mesiya?

5 Zoposa zaka 700 pasadakhale, Baibulo linatchula Betelehemu monga malo obadwirako monga munthu a Mbewu komanso linavumbula kuti iye akhala atakhalako kale “kuyambira nthawi yosayamba,” kuyambira nthawi imene analengedwa m’mwamba. (Mika 5:2) Nthawi ya kuwonekera kwake padziko lapansi monga Wodzozedwayo, Mesiya, wa Yehova idanenedweratu kupyolera mwa mneneri Danieli. (Dan. 9:24-26) Ndipo pamene anadzozedwa ndi mzimu woyera, mawu ochokera kumwamba anamdziwikitsa. (Mat. 3:16, 17) Chotero, pambuyo pa kukhala wotsatira wa Yesu, Filipo ananena ndi chikhutiro kuti: “Iye amene Mose analembera za iye chilamulo ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu mwana wa Yosefe [mwa kulera] wa ku Nazarete.”—Yoh. 1:45.

6. (a) Pambuyo pa imfa ya Yesu, kodi nchiyani chimene otsatira ake anazindikira? (b) Kodi ndani, kwakukulukulu, ali ‘mbewu ya mkazi,’ ndipo kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa ndi kuzunzunda kwake mutu wa njoka?

6 Pambuyo pake, otsatira a Yesu anazindikira kuti makumi enieni amalemba olosera za iye analimo ambirimbiri m’Malemba ouziridwa. Pambuyo pa imfa yake ndi chiukiriro, iye mwini “anawatanthauzira iwo m’malembo onse zinthu za iye yekha.” (Luka 24:27) Kuli kwachiwonekere tsopano kuti Yesu, kwakukulukulu, ndiye ‘mbewu ya mkazi,’ uyo amene amazunzunda mutu wa “chinjoka” mwanjira yakuti Satana potsirizira pake aphwanyidwa ndi kusakhalako. Kupyolera mwa Yesu malonjezo onse a Mulungu kwa anthu, zinthu zonse zimene tikulakalaka kwambiri, zidzakwaniritsidwa.—2 Akor. 1:20.

7. Kuphatikiza pa kudziwikitsa uyo wotchulidwa m’maulosi amenewa, kodi nchiyaninso chimene chiri chopindulitsa kuchilingalira?

7 Pamene kwanthawi yoyamba munawerenga ena a maulosi amenewa mwinamwake munafunsa, monga momwe inachitira mfule Yachiaitiopiya kuti, “Mneneri anena ichi za yani?” Koma mfuleyo siinachite kuti nkhani ithere pomwepo pamene idalandira yankho. Pambuyo pa kumvetsera mosamalitsa malongosoledwe amene Filipo anapereka, mwamunayo anazindikira kuti chiyamikiro chake chonena za mmene Yesu anakwaniritsira ulosi chinafunikiritsa kuchitapo kanthu kumbali yake, mwa kubatizidwa kwake. (Mac. 8:32-38; Yes. 53:3-9) Kodi ife timalabadira mofananamo? Nthawi zina kafotokozedwe ka ulosi kamene kamatisonkhezera kwambiri, kapena mtima wathu ungakhudzidwe ndi mawu otengedwa m’Baibulo lenilenilo pamene kukwaniritsidwa kusonyezedwa.

8. Zitsanzo zinai zaulosi zonena za Yesu Kristu zikupendedwa pano. Sinkhasinkhani mafunso ndi malemba zoperekedwa kusonyeza mmene maulosi amenewa amatiyambukirira. Pendani umodzi umodzi.

8 Wonani mmene izi ziriri choncho ndi malonjezo olosera otsatirapowa ndi zitsanzo zonena za Yesu Kristu. mafunsowa ali akuti inu muyankhe mothandizidwa ndi malemba olembedwawo.

(1) Kodi cholembedwa chonena za kuyesayesa kwa Abrahamu kupereka nsembe Isake chimatithandiza motani kuzindikira chimene Yehova anachita m’kupereka dipo mwanjira ya Mwana wake? (Yoh. 3:16; Gen. 22:1-18 [wonani mmene Isake akulongosoledwera m’vesi 2.])

Kodi ichi chiyenera kutipatsa chidaliro chotani? (Aroma 8:32, 38, 39)

Koma kodi nchiyani chofunika kumbali yathu? (Gen. 22:18; Yoh. 3:36)

(2) Podziwikitsa Yesu monga mneneri wofanana ndi Mose, kodi ndizathayo lalikulu lotani limene Baibulo limatikumbutsa? (Mac. 3:22, 23; Deut. 18:15-19)

Kodi zina za zinthu zimene Yesu walankhula nafe nzotani, ndipo kodi nchifukwa ninji ziri za panthawi yake tsopano? (Mat. 28:18-20; 19:4-9; 18:3-6)

(3) Polongosola chimene chinaphiphiritsiridwa ndi unsembe wa Aroni, kodi ndi mikhalidwe yokondweretsa yotani ya Yesu monga mkulu wa ansembe imene Baibulo limasonyeza? (Aheb. 4:15–5:3; 7:26-28)

Chotero kodi ndimotani mmene tiyenera kulingalirira ponena za kufikira Mulungu m’pemphero kupyolera mwa Kristu kupempha thandizo la kugonjetsa zofooka zathu?

(4) Kaamba ka ukulu wansembe ya Yesu (kulowa mmalo mwa zonse zoperekedwa pansi pa Chilamulo cha Mose), kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala osamala kwambiri kupewa kulowa m’chizolowezi cha kuchita kanthu kalikonse kamene tidziwa kuti nkosakondweretsa kwa Mulungu? (Aheb. 10:26, 27)

Ngati ife tiyamikiradi chiyembekezo chamoyo chotheketsedwa ndi nsembe ya Yesu, kodi ndizinthu ziti zimene tidzakhala akhama kuchita? (Aheb. 10:19-25)

Kodi Tingasonyeze Motani Chikhulupiriro Chathu mwa Kristu?

9. Kodi nchifukwa ninji kulibe chipulumutso kwa ife kusiyapo kupyolera mwa Yesu Kristu?

9 Atasonyeza bwalo la pamwamba Lachiyuda m’Yerusalemu mmene ulosi unali utakwaniritsidwira mwa Yesu, mtumwi Petro analankhula mwamphamvu kuti: “Palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo lakumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Mac. 4:11, 12; Sal. 118:22) Mbadwa za Adamu zonse ziri zochimwa, chotero imfa yawo imadza monga chitsutso cha uchimo ndipo iribe kuyenera kumene kungagwiritsiridwe ntchito monga dipo kaamba ka aliyense. Koma Yesu anali wangwiro, ndipo kuperekedwa kwa moyo wake kuli ndi phindu lansembe. (Sal. 49:6-9; Aheb. 2:9) Iye anapereka kwa Mulungu dipo limene linayenerana ndendende mtengo wake ndi chimene Adamu anali atatayira mbadwa zake. Kodi iri latipindulitsa motani?—1 Tim. 2:5, 6.

10. Longosolani njira imodzi mu imene nsembe ya Yesu yatipindulitsira kwakukulu.

10 Yatheketsa kukhala kwathu ndi chikumbumtima choyera chifukwa cha kukhululukidwa kwa uchimo—kanthu kena kokulira koposa kamene kakanapezedwa kaamba ka Israyeli ndi nsembe za nyama pansi pa Chilamulo cha Mose. (Mac. 13:38, 39; Aheb. 9:13, 14) Ndithudi, kupindula nayo, kumafunikiritsa kuti tikhale owona mtima kwa ife eni kuti tikhale ndi chikhulupiriro chowona mtima mwa Yesu Kristu. Kodi ife aliyense payekha timazindikira kuti timafunikira nsembe ya Kristu motani? “Tikati kuti tiribe uchimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe chowonadi. Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chirichonse.”—1 Yoh. 1:8, 9.

11. Kodi nchifukwa ninji kumizidwa m’madzi kuli chinthu chofunika m’kupeza chikumbumtima chabwino kwa Mulungu?

11 Ndithudi, ena amene amanena kuti amadziwa kuti ali ochimwa ndi amene amanena kuti amakukhulupirira Kristu, amenenso kumlingo wakutiwakuti amakhala ndi mbali m’kuuza ena za Ufumu wa Mulungu monga momwe anachitira Yesu, komabe samafika pa kukhala ndi chikhulupiriro chokwanira mwa Yesu. M’njira yotani? Eya, monga momwe kwasonyezedwera m’Baibulo, pamene anthu m’zaka za zana loyamba anakhaladi okhulupirira, kodi iwo anasonyeza poyera motani zimenezo? Anabatizidwa. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Yesu anali atalamulira kuti ophunzira abatizidwe. (Mat. 28:19, 20; Mac. 8:12; 18:8) Pamene mtima wa munthu wasonkhezeredwadi ndi makonzedwe achikondi amene Yehova anapanga kupyolera mwa Yesu Kristu, iye sadzazengereza. Adzapanga masinthidwe ofunikira aliwonse m’moyo wake, kudzipatulira iye mwini kwa Mulungu ndi kukusonyeza mwa kumizidwa m’madzi. Monga momwe Baibulo limasonyezera, kuli mwa kusonyeza chikhulupiriro mwa njira iyi kuti iye amapanga ‘pempho la chikumbumtima chabwino kwa Mulungu.’—1 Pet. 3:21.

12. Ngati tizindikira kuti tachita uchimo, kodi tiyenera kuchitanji, ndipo chifukwa ninji?

12 Ndithudi, ngakhale pambuyo pa zimenezo, zikhoterero zauchimo zidzawoneka. Ndiyeno nkutani? “Ndikulemberani, kuti musachimwe,” anatero mtumwi Yohane. Chotero sitiyenera kulola monyozera uchimo mwa ife eni, kaya uwoneke m’ntchito, mawu kapena khalidwe. “Ndipo akachimwa wina, nkhoswe tiri naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama; ndipo iye ndiye chiwombolo cha machimo athu; koma osati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.” (1 Yoh. 2:1, 2) Kodi izi zikutanthauza kuti, mosasamala kanthu za chimene tikuchita, ngati tipemphera kwa Mulungu kuti, ‘Tikhululukireni machimo athu,’ zonse zidzayenda bwino? Ayi. Mfungulo ya chikhululukiro ndiyo kulapa kowona mtima. Chithandizo chingafunikirenso kuchokera kwa akulu mu mpingo Wachikristu. Tiyenera kuvomereza kuipa kwa chimene chinachitidwa ndi kumva chisoni mowona mtima ndi chinthucho kotero kuti tidzapanga kuyesayesa kwaphamphu kupewa kusachibwerezanso. (Mac. 3:19; Yak. 5:13-16) Ngati tichita izi, tingakhale otsimikizira kulandira chithandizo cha Yesu. Pamaziko a chikhulupiriro chathu m’mtengo wansembe yake yotetezera machimo, kubwezeretsedwa ku chiyanjo cha Yehova nkothekera, ndipo izi nzofunika ngati kulambira kwathu kuti kukhale kovomerezeka kwa iye.

13. (a) Longosolani njira ina mu imene nsembe ya Yesu yatipindulitsira. (b) Kodi nchifukwa ninji utumiki wathu kwa Mulungu sungatipezere mphoto imeneyi? (c) Koma ngati tiridi ndi chikhulupiriro, tidzakhala tikuchita chiyani?

13 Nsembe ya Yesu yatitseguliranso mwayi wa moyo wosatha—m’miyamba kaamba ka “kagulu ka nkhosa,” ndi padziko lapansi la Paradaiso kaamba ka mabiliyoni ena a anthu. (Luka 12:32; Chiv. 20:11, 12; 21:3, 4) Iyi siiri mphotho imene timapeza mwa kuigwirira ntchito. Mulimonse mmene tingachitire mu utumiki wa Yehova, sitingapange konse kuyenerera kwakuti Mulungu nkukhala ndi mangawa a moyo kwa ife. Moyo wamuyaya ndiwo “mphatso yaulere . . . mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23; Aef. 2:8-10) Komabe, ngati tiri ndi chikhulupiriro m’mphatso imeneyo ndi chiyamikiro kaamba ka dongosolo m’limene inachititsidwira kuthekera, tidzakusonyeza poyera. Kuzindikira mmene Yehova mozizwitsa wagwiritsirira ntchito Yesu kukwaniritsa chifuniro chake ndi mmene kuliri kofunika kuti tonsefe titsatire mapazi a Yesu mosamalitsa, tidzapangitsa uminisitala Wachikristu kukhala chimodzi cha zinthu zofunika koposa m’moyo wathu. Chikhulupiriro chathu chidzawoneka kuchokera m’chikhutiro chimene tidzauza nacho ena za mphatso yodabwitsa imeneyi ya Mulungu.—Yerekezerani Machitidwe 20:24.

14. Kodi chikhulupiriro chotero mwa Yesu Kristu chiri ndi chiyambukiro chogwirizanitsa chotani?

14 Ha ndichiyambukiro chogwirizanitsa chabwino kwambiri chotani nanga, mmene chikhulupiriro chimenechi chiriri! Mwa icho timakokedwera pafupi ndi Yehova, ndi Mwana wake ndi kwa wina ndi mnzake mkati mwa mpingo Wachikristu. (1 Yoh. 3:23, 24) Chimatichitsa kukondwera kuti Yehova mwachifundo wapereka kwa Mwana wake “dzina limene liposa maina onse [kusiyapo dzina la Mulungu], kuti m’dzina la Yesu bondo lirilonse lipinde, la zam’mwamba ndi zapadziko, ndi zapansi padziko, ndi malilime onse avomereze kuti Yesu Kristu ali Ambuye kuchitira ulemu Mulungu Atate.”—Afil. 2:9-11.

Makambitsirano a Kupenda

● Pamene Mesiya anawonekera, kodi nchifukwa ninji kudziwika kwake kunali kosabisika kwa awo amene anakhulupiriradi Mawu a Mulungu?

● Kodi ndimotani mmene zitsanzo zaulosi zokwaniritsidwa mwa Yesu, monga zasonyezedwa patsamba 34, zimatiyambukirira?

● Kodi nsembe ya Yesu yatipindulitsa kale m’njira zotani? Kodi tingasonyeze motani kuiyamikira kwathu?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 34]

Zitsanzo Zaulosi Zonena za Yesu—kodi Ziyenera Kukuyambu Kirani Motani?

Abrahamu akupereka nsembe Isake

Mose monga wolankhulira wa Mulungu

Aroni monga mkulu wa ansembe

Nsembe zanyama

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena