Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 11/1 tsamba 5-7
  • Tsiku Lakubwezera la mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tsiku Lakubwezera la mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nchifukwa Ninji Pali Tsiku Lakubwezera?
  • Kodi Tsiku Lakubwezera la Mulungu Lidzakwaniritsanji?
  • Kodi Mudzachitanji?
  • Kodi Kubwezera Nkolakwa?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kulengeza Tsiku Lakubwezera la Yehova
    Imbirani Yehova Zitamando
  • ‘Atate Wanu Ndi Wachifundo’
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 11/1 tsamba 5-7

Tsiku Lakubwezera la mulungu

MONGA momwe tawonera m’nkhani yapitayo, pali zifukwa zambiri zimene kuliri kolakwa kwa ife kufuna kubwezera. Kuli kolakwa chifukwa chakuti m’kupita kwanthaŵi, sikumathetsa chirichonse. Kuli kolakwa chifukwa chakuti kumalimbitsa udani mmalo momangirira ubwenzi. Ndipo kuli kolakwa chifukwa chakuti kumavulaza uyo amene amasunga malingaliro obwezera.

Komabe, chifukwa chofunika koposa chimene kubwezera kwa anthu kuliri kolakwa chikuwoneka m’mawu a Mose kwa Israyeli akuti: ‘Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wachifundo.’ (Deuteronomo 4:31) Popeza kuti Mulungu ali wachifundo, tiyenera kukhala achifundo mofanana ndi iye. Yesu anauza otsatira ake kuti: ‘Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo.’​—Luka 6:36.

Komabe, Baibulo limamfotokozanso Yehova kukhala “Mulungu wakubwezera.” (Salmo 94:1) Mneneri Yesaya amalankhula za ‘chaka chokomera Yehova’ ndiponso “tsiku lakubwezera la Mulungu wathu.” (Yesaya 61:2) Kodi ndimotani mmene Mulungu angakhalire ponse paŵiri wachifundo ndi wobwezera? Ndipo ngati tiyenera kutsanzira chifundo cha Mulungu, kodi nchifukwa ninji sitiyenera kumtsanzira mwakubwezera?

Poyankha funso loyambalo, Mulungu ngwachifundo chifukwa chakuti amakonda anthu, ndipo amawakhululukira nthaŵi zambiri monga momwe angathere kwautali umene angathe kotero kuti apatse anthu mwaŵi wakusintha njira zawo. Ambiri, mofanana ndi mtumwi Paulo, agwiritsira ntchito chifundo chimenechi. Koma Mulungu alinso wobwezera​—m’lingaliro lakufuna chiweruzo cholungama​—chifukwa chakuti chifundo chimenecho chingangopitiriza kwa nthaŵi yakutiyakuti. Pamene ena asonyeza kuti sadzasintha konse njira zawo, Mulungu adzapereka chiweruzo m’nthaŵi imene ikutchedwa tsiku lake lakubwezera.

Poyankha funso lachiŵirilo, ayi, sitimalungamitsidwa mwakukhala obwezera chifukwa chakuti Mulungu amabwezera. Yehova ali wangwiro m’chiweruzo cholungama. Anthu sali otero. Mulungu amawona mbali zonse za nkhaniyo ndipo nthaŵi zonse amapanga chosankha cholungama. Sitingadaliridwe kuchita zofananazo. Chimenecho ndicho chifukwa chake Paulo anapereka uphungu wakuti: ‘Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati [Yehova, NW].’ (Aroma 12:19) Kaamba ka ubwino wathu, tiyenera kusiya kubwezera m’manja mwa Yehova.

Kodi Nchifukwa Ninji Pali Tsiku Lakubwezera?

Komabe, m’malo ambiri Baibulo limavomereza kuti pafunikira kukhala kuŵerengera kwa ochita zoipa. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo ananeneratu kuti Mulungu, kupyolera mwa Yesu, ‘akabwezera chilango kwa iwo osadziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera [mbiri yabwino ya, NW] Ambuye wathu Yesu.’ (2 Atesalonika 1:8) Tiri ndi zifukwa zabwino zosamalitsira mawu amenewo. Chifukwa ninji?

Choyamba, chifukwa chakuti anthu ambiri lerolino amaumirira pa kunyoza uchifumu wa Mlengi, iwo amanyalanyaza malamulo ake olungama. Kaya amanena kuti amakhulupirira Mulungu kapena ayi, khalidwe lawo limasonyeza mowonekeratu kuti samadzimva kukhala oŵerengera kwa Mulungu. Mawu aŵa a wamasalmo amagwira ntchito kwa onse oterowo: ‘Woipa anyozeranji Mulungu, anena m’mtima mwake, Simudzafunsira?’ (Salmo 10:13) Ndithudi, Yehova sadzalola kunyozedwa mwanjira imeneyi kunthaŵi yosatha. Ngakhale kuti ndi Mulungu wachikondi, iye alinso Mulungu wachiweruzo cholungama. Iye adzalabadira mfuu za awo amene amaderadi nkhaŵa ndi chiweruzo cholungama: “Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu; Musaiwale ozunzika.”​—Salmo 10:12.

Ndiponso, anthu onyalanyaza lamulo akuwononga dziko lapansi lenilenilo lomwe timakhalapo. Iwo amaipitsa mpweya, nthaka, ndi madzi; iwo adzaza dziko lapansi ndi chisalungamo ndi nkhalwe. Ndipo awunjika zida zochuluka za makemikolo, nyukliya, ndi zida zina zakupha kuwopseza kukhalapo ndi moyo kwa anthu. Kuloŵereramo kwa Mulungu kuli kofunika kwenikweni kotero kuti pakhale chitsimikizo cha mtsogolo mosungika kwa anthu omvera. (Chibvumbulutso 11:18) Kuloŵereramo kumeneku ndikumene Yesaya anasonyako monga tsiku lakubwezera.

Kodi Tsiku Lakubwezera la Mulungu Lidzakwaniritsanji?

Malinga ndi kunena kwa Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words, m’Malemba Achigiriki, liwu lakuti kubwezera, pamene lagwiritsiridwa ntchito ponena za Mulungu, m’lingaliro lenileni limatanthauza “‘chinthu chomwe chimatulukapo pa chiweruzo cholungama,’ kaŵirikaŵiri osati ndi kubwezera kwa anthu, kochitidwa chifukwa cha lingaliro la kulakwiridwa kapena lingaliro la kukwiyitsidwa wamba.” Chotero, kubwezera kwa Mulungu motsutsana ndi adani ake sikudzakhala nthaŵi yakukhetsa mwazi kosalamulirika, monga kulipsira kwaumwini. ‘[Yehova, NW] adziŵa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe,” limatiuza motero Baibulo.​—2 Petro 2:9.

Atumiki a Mulungu amayang’ana kutsogolo ku tsiku lakubwezera la Mulungu monga nthaŵi imene khalidwe labwino lidzalemekezedwa ndipo olungama adzapulumutsidwa ku chitsenderezo cha oipa. Ichi sichikutanthauza kuti iwo ali anjiru kapena olipsira. Baibulo limachenjeza kuti: ‘Wokondwera ndi tsoka sadzapulumuka chilango.’ (Miyambo 17:5) Mosiyana, iwo amakulitsa chifundo ndi chisoni, nasiyira Mulungu kupanga zosankha zonse za kubwezera.

Zowonadi, sikuli kokhweka kwa anthu okwiya kuchita mwanjira imeneyi. Koma kuli kotheka, ndipo ambiri achita motero. Mwachitsanzo, Pedro sanali wachimwemwe paubwana wake ndipo kaŵirikaŵiri anali kumenyedwa ndi mbale wake wamkulu. Chotero anakula kukhala wachiwawa, nthaŵi zambiri anali m’vuto ndi apolisi ndipo chifukwa cha mkwiyo womwe anali nawo kwa mbale wake, anakhala wosakoma mtima kwa mkazi wake ndi ana ake. Pomalizira pake, anamvetsera kwa mmodzi wa Mboni za Yehova ndipo pambuyo pake anayamba kuphunzira Baibulo. Iye akusimba kuti: “Ndi chithandizo cha Yehova, ndinasintha, ndipo tsopano, m’malo momenyana ndi anthu, ndimawathandiza monga mkulu Wachikristu.” Ndi chithandizo cha Baibulo ndi mzimu woyera, anthu ena osaŵerengeka asintha mofananamo kuleka kukhala amwano kapena obwezera ndikuyamba kusonyeza chikondi ndi kuleza mtima kulinga kwa ena.

Kodi Mudzachitanji?

Kukumbukira kudza kwa tsiku lakubwezera la Mulungu kudzatithandiza kugwiritsira ntchito kuleza mtima kwa Yehova. Koma mwaŵi wakuchita zimenezo suli wopanda malire. Posachedwapa tsiku limenelo lidzafika. Mtumwi Petro anasonyeza chifukwa chake silinafikebe: ‘[Yehova, NW] sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.’​—2 Petro 3:9.

Pamenepo, kuli kofunika koposa kukonzekera tsopano kaamba ka tsiku lakuŵerengera la Mulungu mwakuphunzira Malemba ndikugwiritsira ntchito uphungu wake. Ichi chidzatithandiza kutsatira mawu a wamasalmo akuti: ‘Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo: usavutike mtima ungachite choipa. Pakuti ochita zoipa adzadulidwa: koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.’​—Salmo 37:8, 9.

[Chithunzi patsamba 7]

Pambuyo pa tsiku lakubwezera la Mulungu, ‘iwo akuyembekeza Yehova adzalandira dziko lapansi’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena