Mutu 11
Kodi Nchifukwa Ninji Mulungu Walola Kuipa?
1. (a) Kodi mkhalidwe padziko lapansi lerolino ngwotani? (b) Kodi anthu ena amakhala ndi chodandaula chotani?
KULIKONSE kumene muyang’ana m’dziko, kuli upandu, udani ndi vuto. Kawirikawiri ndiwo opanda liwongo amene amavutika. Anthu ena amapaka Mulungu liwongo. Iwo anganene kuti: ‘Ngati kuli Mulungu, kodi nchifukwa ninji akulola zinthu zowopsa zonsezi kuchitika?’
2. (a) Kodi ndani amene akuchita zinthu zoipa? (b) Kodi ndimotani mmene kuvutika kochuluka padziko lapansi kukanapewedwera?
2 Komabe kodi ndani amene akuchitira ena zinthu zoipa zimenezi? Ndiwo anthu, osati Mulungu. Mulungu amatsutsa machitidwe oipa. Kunena zowona, kuvutika kwambiri padziko lapansi kukanapewedwa ngati anthu akanamvera malamulo a Mulungu. Iye amatilamulira kuti tikonde. Iye amaletsa mbanda, kuba, chigololo, umbombo, kuledzera ndi machitidwe ena a cholakwa amene amachititsa anthu kuvutika. (Aroma 13:9; Aefeso 5:3, 18) Mulungu analenga Adamu ndi Hava ali ndi ubongo wodabwitsa ndi thupi ndipo ndi kuthekera kwa kusangalala ndi moyo mokwanira. Iye sanawafune kapena ana awo kuvutika kapena kukhala ndi vuto.
3. (a) Kodi ndani amene akuchititsa kuipa? (b) Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti Adamu ndi Hava akanakaniza ziyeso za Satana?
3 Anali Satana Mdyerekezi amene anayambitsa kuipa padziko lapansi. Koma Adamu ndi Hava analinso ndi liwongo. Iwo sanali ofooka kwambiri chakuti iwo sakanatha kukaniza pamene Mdyerekezi anawayesa. Iwo akadauza Satana “kuchoka,” monga momwedi munthu wangwiroyo Yesu anachitira pambuyo pake. (Mateyi 4:10) Koma iwo sanatero. Chifukwa cha chimenecho, iwo anakhala opanda ungwiro. Ana awo onse, kuphatikizapo ife, talandira kupanda ungwiro kumeneko, kumene kunadza ndi utenda, chisoni ndi imfa. (Aroma 5:12) Koma kodi nchifukwa ninji Mulungu walola kuvutika kupitirizabe?
4. Kodi nchiyani chimene chikutithandiza kuzindikira kuti Mulungu wachikondi akalola kwakanthawi kuipa?
4 Munthu poyamba angaganizire kuti sipangakhale chifukwa chachikulu mokwanira chakuti Mulungu alolere kuvutika kwa anthu konse kumene kwakhalapo mkati mwa zaka mazana ambiri. Komabe, kodi nkoyenera kufika lingaliro limenelo? Kodi makolo amene amakondadi ana awo sanawalole kuchitidwa oparesheni yopweteka kuti achotse vuto lina? Inde, kulola kuvutika kwakanthawi kawirikawiri kwatheketsa ana kukhala ndi thanzi labwinopo pambuyo pake m’moyo. Kodi ndi ubwino wotani umene wachitidwa ndi kulola kwa Mulungu kuipa?
NKHANI YAIKULU YOTI ITHETSEDWE
5. (a) Kodi ndimotani mmene Satana anatsutsira Mulungu? (b) Kodi Satana analonjezanji Hava?
5 Kupandukira Mulungu m’munda wa Edene kunadzutsa nkhani kapena funso lalikulu. Tifunikira kuipenda kuti tidziwe chifukwa chake Mulungu walola kuipa. Yehova anauza Adamu kuti asadye mtengo wina m’mundamo. Ngati Adamu akadadya, kodi nchiyani chimene chikadachitika? Mulungu anati: “Udzafa ndithu.” (Genesis 2:17) Komabe, Satana ananena zosemphana kotheratu. Iye anauza mkazi wa Adamu, Hava, kuti asaleke ndipo mtengo woletsedwawo. “Sudzafa ndithu,” anatero Satana. Kunena zowona, anapitiriza kuuza Hava kuti: “Pakuti Mulungu akudziwa kuti tsiku lenilenilo la kudya kwanu maso anu ayenera kutseguka ndipo inu muyenera kukhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.”—Genesis 3:1-5, NW.
6. (a) Kodi nchifukwa ninji Hava sanamvere Mulungu? (b) Kodi kudya mtengo woletsedwa kunatanthauzanji?
6 Hava samavere Mulungu ndipo anadya. Nchifukwa ninji? Hava anakhulupirira Satana. Iye mwayekha anaganiza kuti akapindula mwa kusamvera Mulungu. Analingalira kuti iye kapena Adamu sakafunikiranso kuyankha kwa Mulungu. Iwo sakanafunikiranso kugonjera ku malamulo ake. Iwo akatha kudzisankhira chimene chiri “chabwino” ndi chimene chiri “choipa.” Adamu anagwirizana ndi Hava nadyanso. Pofotokoza tchimo loyambirira la munthu kwa Mulungu, mawu amtsinde mu The Jerusalem Bible akuti: “Ndilo mphamvu ya kudzisankhira chimene chiri chabwino ndi chimene chiri choipa ndi ya kuchita mogwirizana nazo, kufuna kudziimira kotheratu . . Tchimo loyambalo linali kuukira ulamulo wa Mulungu.” Ndiko kuti, kunali kuukira kuyenera kwa Mulungu kwa kukhala wolamulira kapena mkulu wotheratu wa Munthu.
7. (a) Kodi ndinkhani yotani imene inadzutsidwa ndi kusamvera kwa munthu? (b) Kodi ndimafunso otani ofuna kuyankha mogwirizana ndi nkhani imeneyi?
7 Motero mwa kudya chipatso choletsedwacho, Adamu ndi Hava anadzifumutsa mu ulamuliro wa Mulungu. Anatulukamo okha, akumachita chimene chinali “chabwino” kapena “choipa” mogwirizana ndi zosankha zawo. Motero nkhani kapena funso lalikulu lodzutsidwa linali: Kodi Mulungu ali ndi kuyenera kwa kukhala wolamulira wotheratu wa anthu? M’kunena kwina, kodi Yehova Ndiye woti asankhire anthu chimene chiri chabwino kapena choipa? Kodi iye Ndiye woti anene chimene chiri khalidwe labwino ndi chimene sichiri? Kapena kodi munthu angachite ntchito yabwinopo ya kudzilamulira? Kodi ndinjira ya yani yolamulira imene iri yabwino kwambiri? Kodi anthu, pansi pa chitsogozo chosawoneka cha Satana, angalamulire bwino lomwe popanda chitsogozo cha Yehova? Kapena kodi chitsogozo cha Mulungu chikufunika kuti akhazikitse boma lolungama limene lidzadzetsa mtendere wosatha kudziko lapansi? Mafunso onse oterowo anadzutsidwa m’chiukiro chimenechi pa ulamuliro wa Mulungu, pa kuyenera kwake kwa kukhala wolamulira yekha ndi wotheratu wa anthu.
8. Kodi nchifukwa ninji Yehova sanaphe opandukawo nthawi yomweyo?
8 Ndithudi, mwamsanga pamene chipanduko chinachitika Yehova akadawononga opanduka atatuwo. Panalibe kukayikira kuti iye anali wamphamvu kwambiri koposa Satana kapena Adamu ndi Hava. Koma kuwapha sikukanathetsa nkhaniyo m’njira yabwino koposa. Mwa chitsanzo, sikukanayankha funso lakuti kaya anthu akadadzilamulira bwino lomwe popanda chithandizo chochokera kwa Mulungu. Motero Yehova anapereka nthawi kuti athetse nkhani yaikulu imene inadzutsidwayo.
KUTHETSA NKHANIYO
9, 10. Kodi zotulukapo za anthu oyesa kudzilamulira popanda chitsogozo cha Mulungu zakhala zotani?
9 Tsopano popeza kuti nthawi yapita, kodi nchiyani chimene chakhala chotulukapo? Eya, kodi inu mungati nchiyani? Kodi zaka 6,000 zapitazo za mbiri zasonyeza kuti anthu akhala ochita bwino m’kudzilamulira popanda chitsogozo cha Mulungu? Kodi anthu apereka boma labwino kaamba ka dalitso ndi chimwemwe cha onse? Kapena kodi cholembedwa cha mbiri chasonyeza kuti mawu a mneneri Yeremiya ngowona: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake”?—Yeremiya 10:23.
10 Mkati mwa mbiri mitundu yonse ya maboma yayesedwa, koma palibe lirilonse limene lapereka chisungiko ndi chimwemwe chenicheni kwa awo onse okhala mu ulamuliro wawo. Anthu ena angasonye ku zizindikiro za kupita patsogolo. Koma kodi munthu angatchule kupita patsogolo kwenikweni pamene uta ndi muvi zalowedwa m’malo ndi bomba la atomiki, ndi pamene dziko tsopano liri m’mantha akulu a nkhondo ina yadziko? Kodi ndikupita patsogolo kwamtundu wanji pamene anthu angayende pamwezi koma sangathe kukhala limodzi mu mtendere padziko lapansi? Kodi ziri ndi ubwino wanji kwa anthu kumanga nyumba zokhala ndi mitundu yonse ya ziwiya zamakono pamene mabanja amene akukhalamo alekanitsidwa ndi mavuto? Kodi ziwawa m’makwalala, kuwonongedwa kwa chuma ndi moyo ndi kufala kwa kusamvera malamulo ndizo zinthu zozinyadira? Kutalitali! Koma zimenezi ndizo zotulukapo za anthu oyesa kudzilamulira popanda Mulungu.—Miyambo 19:3.
11. Motero, mwachiwonekere, kodi nchiyani chimene anthu akufunikira?
11 Umboni uyenera kukhala womvekera bwino kwa onse. Zoyesayesa za munthu za kudzilamulira mosadalira Mulungu zakhala kulephera kowopsa. Izo zachititsa kuvutika kwakukulu kwa anthu. “Wina apweteka mnzake pomlamulira,” Baibulo limatero. (Mlaliki 8:9) Mwachiwonekere, anthu akufunikira chitsogozo cha Mulungu m’kuyendetsa zochita zawo. Monga momwedi Mulungu analengera munthu nd kufunikira kudya chakudya ndi kumwa madzi, momwemonso munthu analengedwa ndi kufunikira kwa kumvera malamulo a Mulungu. Ngati munthu anyalanyaza malamulo a Mulungu, adzalowa m’vuto, motsimikizirika monga momwedi iye akavutikira ngati atanyalanyaza zofunika za thupi lake za chakudya ndi madzi.—Miyambo 3:5, 6.
NCHIFUKWA NINJI NTHAWI YAITALI KWAMBIRI?
12. Kodi nchifukwa ninji Mulungu walola nthawi yaitali yotero kuthetsa nkhaniyo?
12 Komabe, munthu angafunse kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji Mulungu walola nthawi yochuluka kwambiri, pafupifupi zaka 6,000 tsopano, kuti athetse nkhani imeneyi? Kodi sikanathetsedwa m’njira yokhutiritsa kalekale? Osati kwenikweni. Ngati Mulungu akanaloweramo kalekale, chinenezo chikadapangidwa chakuti anthu sanapatsidwe nthawi yokwanira kuti ayese. Koma monga momwe ziriri, anthu akhala ndi nthawi yochuluka ya kupanga boma limene likakwaniritsa zosowa za anthu ake onse, kuphatikizapo kupanga zotulukiridwa zausayansi zimene zikatha kuchititsa ulemerero wa onse. Mkati mwa zaka mazana ambiri anthu ayesa pafupifupi mpangidwe uliwonse wa boma. Ndipo kupita kwawo patsogolo m’mbali yasayansi kwakhala kwapadera. Iwo asonkhanitsa maatomu ndipo apita ku mwezi. Koma kodi nchiyani chimene chakhala chotulukapo? Kodi kwadzetsa dongosolo latsopano labwino kwambiri kaamba ka kudalitsidwa kwa anthu?
13. (a) Mosasamala kanthu za kupita patsogolo kwasayansi kwa munthu konse, kodi mkhalidwe ngowotani lerolino? (b) Kodi zimenezi zikutsimikiziranji mwachiwonekere?
13 Kutalitali! M’malo mwake, padziko lapansi pali kupanda chimwemwe ndi vuto zowonjezereka koposa kale lonse. Kunena zowona, upandu, kuipitsa, nkhondo, kusweka kwabanja ndi mavuto ena zafika pa mlingo wowopsa kwambiri chakuti asayansi amakhulupirira kuti kukhalapo kwenikweniko kwa munthu kukuwopsezedwa. Inde, pambuyo pa zaka pafupifupi 6,000 za kudziwa zinthu m’kudzilamulira, pambuyo pa kufika pamwamba “m’kupita patsogolo” kwasayansi, anthu tsopano akuyang’anizana ndi kudzipha! Nkowonekera bwino kwambiri chotani nanga mmene kuliri kuti anthu sangadzilamulire bwino lomwe popanda Mulungu! Ndiponso palibe aliyense tsopano angadandaule kuti Mulungu sanapereke nthawi yokwanira yothetsa nkhani imeneyi.
14. Kodi nchifukwa ninji ife tiyenera kulimbikitsidwa kupenda nkhani ina yofunika yodzutsidwa ndi Satana?
14 Ndithudi Mulungu wakhala ndi chifukwa chabwino chololera anthu pansi pa ulamuliro wa Satana kuchititsa kuipa kumene kwakhalapo kwa nthawi yaitali kwambiri. Mwa kupanduka kwake Satana anadzutsa nkhani ina imene yafunanso nthawi kuti ithetsedwa. Kupendedwa ka nkhani imeneyi kudzapereka chithandizo chowonjezereka m’kuzindikira kwathu chifukwa chake Mulungu walola kuipa. Muyenera kukondwera kwambiri ndi nkhani imeneyi chifukwa chakuti inu mwini mukulowetsedwamo.
[Chithunzi patsamba 100]
Limodzi ndi chifukwa chabwino, kholo lidzalola mwana wokondwedwa kuchitidwa oparesheni yopweteka. Mulungu alinso ndi zifukwa zabwino zololera anthu kuvutika kwakanthawi
[Chithunzi patsamba 101]
Adamu ndi Hava, mwa kudya zipatso zoletsedwa, anasiya ulamuliro wa Mulungu. Iwo anayamba kupanga zosankha zawozawo ponena za chimene chinali chabwino kapena choipa
[Zithunzi patsamba 103]
Monga momwedi munthu analengedwa ndi kufunikira kudya ndi kumwa madzi, analengedwanso, ndi kufunikira chitsogozo cha Mulungu