Mutu 2
Mdani wa Moyo Wosatha
1. Popeza kuti chimwemwe ndi mtendere sizimapezedwa kawirikawiri, kodi ndimafunso otani amene amabuka?
CHIMWEMWE padziko lapansi—pafupifupi munthu aliyense amachifuna. Pamenepa kodi nchifukwa ninji ambirimbiri ali osakondwa? Kodi chalakwika nchiyani? Popeza kuti pafupifupi aliyense amafuna mtendere, kodi nchifukwa ninji mitundu imachita nkhondo ndipo kodi nchifukwa ninji anthu amadana? Kodi pali mphamvu yotsogoza imene imawasonkhezera kuchita zinthu zoipa zimenezi? Kodi kungakhale kwakuti mphamvu imodzi yosawoneka imalamulira mitundu?
2. Kodi ndimaupandu otani m’mbiri amene amachititsa ambiri kudabwa kaya ngati mphamvu yoipa ndi yosawoneka ingakhale ikulamulira anthu?
2 Ambiri adzifunsa ponena za zimenezi pamene iwo alingalira nkhanza yowopsa ya anthu—utsi wowopsa wogwiritsiridwa ntchito m’nkhondo kutsamwitsa ndi kuwotcha anthu kufikira imfa, kuphatikizapo mabomba amoto ndi mabomba aatomiki. Ndiponso, lingalirani choponya malawi amoto, misasa yachibalo, kupululidwa kwa mamiliyoni ambiri a anthu osowa chochita, monga ngati m’Cambodia m’zaka zaposachedwapa. Kodi mukuganiza kuti zoipa zonsezi zinangochitika zokha? Pamene kuli kwakuti munthu ngwokhoza mwa iye yekha kuchita ntchito zowopsa, pamene mulingalira kuipa kwakukulu kwa machitidwe ake, kodi sikukuwonekera kuti iye wakhala akusonkhezeredwa ndi mphamvu ina yoipa ndi yosawoneka?
3. Kodi Baibulo limanenanji ponena za ulamuliro wa dziko?
3 Palibe kufunikira kwa kuyerekezera pa nkhaniyo. Baibulo limasonyeza mwachiwonekere kuti munthu wina wanzeru wosawoneka wakhala akulamulira anthu ndi mitundu yomwe. M’Baibulo, Yesu Kristu amatcha wamphamvu ameneyu “wolamulira wa dziko lino.” (Yohane 12:31; 14:30; 16:11, NW) Kodi iye ndani?
4. Kodi nchiyani chimene Mdyerekezi anasonyeza Yesu, ndipo kodi ndilonjezo lotani limene iye anapereka kwa iye?
4 Kuti atithandize kudziwa amene iye ali, ganizirani zimene zinachitika pachiyambi cha uminisitala wa Yesu padziko lapansi pano. Baibulo limatiuza kuti Yesu atabatizidwa analowa m’chipululu kumene anayesedwa ndi cholengedwa chosawoneka chotchedwa Satana Mdyerekezi. Mbali ya kuyesa kumeneko ikufotokozedwa motere: “Mdyerekezi anamtengeranso ku phiri lalitali kwambiri namsonyeza maufumu onse a dziko lapansi ndi ulemerero wawo, nati kwa iye: ‘Ndidzakupatsani zinthu zonsezi ngati mutagwada ndi kuchita kachitidwe kakundilambira.’”—Mateyu 4:8, 9, NW.
5. (a) Kodi nchiyani chimasonyeza kaya ngati maboma onse adziko ali chuma cha Mdyerekezi? (b) Malinga ndi kunena kwa Baibulo, kodi ndani amene ali “mulungu wa dongosolo lino la zinthu”?
5 Taganizirani zimene Mdyerekezi analonjeza Yesu Kristu. Zinali “maufumu onse a dziko lapansi.” Kodi maboma adziko lapansi onsewa analidi a Mdyerekezi? Inde, pakuti zikanapanda kutero akanawalonjeza motani kwa Yesu? Yesu sanakane kuti iwo anali a Satana, kumene iye akanachita ngati Satana sanali mwini wake. Satana alidi wolamulira wosawoneka wa mitundu yonse ya dziko lapansi! Baibulo mwachimvekere limati: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Kunena zowona, Mawu a Mulungu amatcha Satana “mulungu wa dongosolo lino la zinthu.”—2 Akorinto 4:4 NW.
6. (a) Kodi chidziwitso chimenecho chonena za ulamuliro wa Satana chimatithandiza kuzindikira chiyani (b) Kodi nchiyani chimene Satana angafune kutichitira, motero kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita?
6 Chidziwitso chimenechi chimatithandiza kuzindikira chifukwa chake Yesu anati: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino lapansi.” (Yohane 18:36, NW) Chimatithandizanso kuzindikira chifukwa chake mitundu imadana ndi kuyesa kuwonongana pamene chiri chikhumbo cha anthu onse olama cha kukhala pa mtendere. Inde, “Satana . . . akusocheza dziko lonse lapansi lokhalidwe ndi anthu.” (Chivumbulutso 12:9, NW) Iye akufunanso kutisocheza. Iye sakufuna kuti tilandire mphatso ya Mulungu ya moyo wosatha. Motero tifunikira kumenya nkhondo kuti tisasonkhezeredwe naye kuchira zimene ziri zoipa. (Aefeso 6:12) Tifunikira kudziwa za Satana ndi mmene amagwirira ntchito kuti tikanize zoyesayesa zake za kutisocheza.
Amene Mdyerekezi Ali
7. Kodi nchifukwa ninji sitingawone Mdyerekezi?
7 Satana Mdyerekezi ndimunthu weniweni. Iye sali chabe choipa mwa anthu onse, monga momwe anthu ena angakhulupiririre. Ndithudi, anthu sangawone Mdyerekezi, kaamba ka chifukwa chofananacho chimene iwo sangawonere Mulungu. Mulungu ndi Mdyerekezi yemwe ndianthu auzimu, mitundu ya moyo yokwererapo koposa anthu ndi yosawoneka ndi maso athu. —Yohane 4:24.
8. Kodi nchifukwa ninji anthu ambiri amakhulupirira kuti Mulungu analenga Mdyerekezi?
8 ‘Koma ngati Mulungu ndiye chikondi,’ wina angatero, ‘kodi nchifukwa ninji anapanga Mdyerekezi?’ (1 Yohane 4:8) Chenicheni nchakuti Mulungu sanalenge Mdyerekezi. ‘Komabe ngati Mulungu analenga munthu aliyense,’ munthu angatero, ‘iye ayenera kukhala atalenga Mdyerekezi. Kodi ndaninso akadamlenga? Kodi Mdyerekezi anachokera kuti?’
9. (a) Kodi angelo ndianthu a mtundu wotani? (b) Kodi mawuwo “mdyerekezi” ndi “satana” amatanthauzanji?
9 Baibulo limafotokoza kuti Mulungu analenga anthu auzimu ambirimbiri, olingana ndi iye mwini. M’Baibulo, mizimu imeneyi imatchedwa angelo. Ndiponso, iwo amatchedwa “ana a Mulungu.” (Yobu 38:7; Salmo 104:4; Ahebri 1:7, 13, 14) Mulungu analenga iwo onse angwiro. Palibe mmodzi wa iwo anali mdyerekezi, kapena satana. Liwulo “mdyerekezi” limatatanthauza woneneza ndi liwulo “satana” limatanthauza wotsutsa.
10. (a) Kodi ndani amene anapanga Satana Mdyerekezi (b) Kodi ndimotani mmene munthu wabwino angadzipangire kukhala mpandu?
10 Komabe, nthawi inadza pamene mmodzi wa ana auzimu a Mulungu amenewa anadzipanga kukhala Mdyerekezi, ndiko kuti, wabodza wanjiru amene amanena zinthu zoipa ponena za wina. Iyenso anadzipanga kukhala Satana, ndiko kuti, wotsutsa Mulungu. Iye sanalengedwe wotero, koma pambuyo pake anakhala mtundu umenewo wa munthu. Kofotokoza mwa fanizo: Mbala simabadwa iri mbala. Iyo ingakhale itachokera m’banja labwino, yokhala ndi makolo owona mtima ndi abale ndi alongo omvera malamulo. Koma chikhumbo chake cha iye mwini cha zimene ndalama zingagule ndicho chimene chingakhale chitamchititsa kukhala mbala. Pamenepa, kodi ndimotani mmene mmodzi wa ana auzimu a Mulungu anadzipangira kukhala Satana Mdyerekezi?
11. (a) Kodi ndichifuno cha Mulungu chotani chimene mngelo wopandukayo anadziwa? (b) Kodi ndichikhumbo chotani chimene mngelo ameneyu anali nacho, ndipo kodi chinamtsogoza kuchita chiyani?
11 Mngelo amene anasanduka Mdyerekezi analipo pamene Mulungu analenga dziko lapansi ndi pambuyo pake anthu awiri oyambawo, Adamu ndi Hava. (Yobu 38:4, 7) Motero iye anayenera kukhala atamva Mulungu akuwauza kuti abale ana. (Genesis 1:27, 28) Iye anadziwa kuti pambuyo pa kanthawi dziko lonse lapansi likadzaza anthu olungama olambira Mulungu. Chimenecho chinali chifuno cha Mulungu. Komabe, mngelo ameneyu anaganizira kwambiri za kukongola kwake ndi nzeru nafuna kuti iye alandire kulambira kumene kukaperekedwa ndi nzeru nafuna kuti iye alandire kulambira kumene kukaperekedwa kwaMulungu. (Ezekieli 28:13-15; Mateyu 4:10) M’malo mwa kutchotsa chikhumbo choipa chimenechi m’maganizo mwake, anapitiriza kuchiganizira. Kumeneku kunachititsa kuchitapo kanthu kuti apeze ulemu ndi kukwezeka kumene iye anafuna. Kodi anachitanji? —Yakobo 1:14, 15.
12. (a) Kodi ndimotani mmene mngelo ameneyu analankhulira ndi Hava, ndipo kodi anamuuzanji? (b) Kodi mngelo ameneyu anasanduka Satana Mdyerekezi motani (c) Kodi nchiyani chimene chiri lingaliro lolakwa ponena za kawonekedwe ka Mdyerekezi?
12 Mngelo wopandukayo anagwiritsira ntchito njoka yonyozeka kulankhula ndi mkazi woyambayo, Hava. Iye anachita zimenezi mofanana kwambiri ndi mmene munthu waluso angapangitsire kuwoneka monga ngati kuti nyama yapafupi kapena chifaniziro chikulankhula. Koma analidi mngelo wopanduka ameneyu, iye wotchedwa m’Baibulo “njoka yokalambayo,” amene anali kulankhula ndi Hava. (Chivumbulutso 12:9) Iye ananena kuti Mulungu anali kumnamiza, ndipo anali kumbisira chidziwitso chimene iye anayenera kukhala nacho. (Genesis 3:1-5) Limeneli linali bodza lanjiru ndipo linamsandutsa mdyerekezi. Iye motero anakhalanso wotsutsa Mulungu, kapena Satana. Monga momwe mungawonere, nkolakwa kuganizira Mdyerekezi kukhala cholengedwa chokhala ndi nyanga ndi nchokhotho wotembenuzira amene amayang’anira malo a chizunzo apansi panthaka. Iye alidi mngelo wamphamvu kwambiri, koma woipa.
Magwero A Mavuto Adziko
13. (a) Kodi ndimotani mmene Hava anachitira ndi bodza la Mdyerekezi? (b) Kodi ndimawu otani amene Mdyerekezi ananena?
13 Bodza limene Mdyerekezi anauza Hava linagwira ntchito monga momwedi iye analinganizira. Iye analikhulupirira ndipo motero sanamvere Mulungu. Ndipo iye anali wokhoza kuchititsa mwamuna wake kuswanso lamulo la Mulungu. (Genesis 3:6) Kunena kwa Mdyerekezi kunali kwakuti anthu angathe kukhala popanda Mulungu. Iye ananena kuti anthu angadzilamulire bwino lomwe, popanda chithandizo cha Mulungu. Mdyerekezi ananenanso kuti akatha kupatutsa kwa Mulungu awo onse amene akakhala mbadwa za Adamu ndi Hava.
14. Kodi nchifukwa ninji Mulungu sanawononge Satana nthawi yomweyo?
14 Ndithudi, Mulungu akanatha kuwononga Satana nthawi yomweyo. Koma kumeneko sikukanayankha mafunso amene Satana adadzutsa, mafunso amene akatha kukhalabe m’maganizo mwa angelo amene anali kuwona. Motero Mulungu anapereka nthawi yakuti Satana ayese kutsimikizira mawu ake. Limodzi ndi zotulukapo zotani?
15, 16. (a) Kodi nchiyani chimene kupita kwa nthawi kwatsimikizira ponena za zonena za Mdyerekezi? (b) Kodi nchochitika chotani chimene chayandikira pafupi?
15 Kupita kwa nthawi kwatsimikizira kuti anthu sangadzilamulire bwino lomwe popanda chithandizo cha Mulungu. Zoyesayesa zawo zalephera kotheratu. Anthu avutika mowopsa pansi pa maboma a anthu, amene monga momwe Malemba akusonyezera, akhala akuyendetsedwa chakutseri ndi Mdyerekezi. Ndiponso, kupereka nthawi kwa Mulungu kwasonyeza bwino lomwe kuti Satana sanakhale wokhoza kupatutsa anthu onse ku kulambira Mulungu. Nthawi zonse pakhala ena amene akhalabe okhulupirika ku ulamuliro wa Mulungu. Mwa chitsanzo, mungawerenge m’Baibulo kuti, Satana anayesa, mosaphula kanthu, kuletsa Yobu kutumikira Mulungu. —Yobu 1:6-12.
16 Motero zonena za Mdyerekezi zatsimikiziridwa kukhala zabodza. Iye akuyenereradi chiwonongeko chifukwa cha kukhala atayambitsa kupandukira Mulungu koipa. Mosangalatsa, tsopano tafika nthawi yakuti Mulungu athetse ulamuliro wa Satana. Pofotokoza sitepe loyamba m’kuchita zimenezi, Baibulo limasimba nkhondo yaikulu kumwamba, imene, ndithudi, sinawonedwe kapena kumvedwa ndi anthu padziko lapansi. Werengani bwino lomwe cholembedwa Chabaibulo chotsatirapocho:
17. (a) Kodi ndimotani mmene Baibulo limafotokozera nkhondoyo kumwamba? (b) Kodi chotulukapo chake chinali chotani kwa awo akumwamba, ndi kwa awo apadziko lapansi?
17 “Nkhondo inaulika kumwamba: Mikayeli [amene ali Yesu Kristu woukitsidwayo] ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka, ndipo chinjoka ndi angelo ake chinamenya nkhondo koma sichinapambane, ndiponso malo sanawapezekerenso kumwamba. Motero chinjoka chachikulucho chinaponyedwa pansi, njoka yoyambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheza dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu; iye anaponyedwakudziko lapansi, ndipo angelo ake anaponyedwa naye. ‘Chifukwa chake kondwerani, miyamba inu ndi inu amene mukukhalamo! Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa chakuti Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala ndi mkwiyo waukulu, podziwa kuti ali ndi nyengo ya nthawi yaifupi.’” —Chivumbulutso 12:7-9, 12, NW.
18. (a) Kodi ndiliti pamene nkhondoyo kumwamba inachitika? (b) Kodi nchiyani chimene chakhala chikuchitika padziko lapansi chiyambire pamene Satana “anaponyedwa pansi”?
18 Kodi nkhondo imeneyi kumwamba inachitika liti? Umboni umasonyeza kuti inachitika pafupi ndi nthawi ya Nkhondo Yoyamba Yadziko, imene inayamba mu 1914. Monga momwe Chivumbulutso chikusonyezera, Satana anachotsedwa kumwamba pa nthawi imeneyo, zimene zikutanthauza kuti takhala tikukhala ‘m’nyengo ya nthawi yake yaifupi’ chiyambire pa nthawi imeneyo. Motero, ano ndiwo “masiku otsiriza” a dziko la Satana. Kuwonjezereka kwa kusalamulirika, mantha, nkhondo, kuperewera kwa zakudya, nthenda ndi mikhalidwe ina yosautsa zimene takhala tikuziwona ziri umboni wa chenicheni chimenechi. —Mateyu 24:3-12; Luka 21:26; 2 Timoteo 3:1-5.
19. (a) Kodi nchiyani chimene Satana tsopano akuyesa zolimba kuchita? (b) Kodi nchiyani chimene chikakhala chanzeru kwa ife kuchita?
19 Popeza kuti Satana akudziwa kuti’nyengo yake ya nthawi yaifupi’ iri pafupi kutha, iye akuyesa mwamphamvu kwambiri koposa kale lonse kuletsa anthu kutumikira Mulungu. Iye akufuna kutenga anthu ambiri monga momwe angathere kulowa naye m’chiwonongeko. Limodzi ndi chifukwa chabwino Baibulo limamfotokoza kukhala mkango wobangula umene ukufunafuna munthu woti udye. (1 Petro 5:8, 9) Ngati sitifuna kugwidwa naye, tifunikira kudziwa mmene iye amaukirira ndiponso njira m’zimene iye amasochezera anthu. —2 Akorinto 2:11.
Mmene Satana Amasochezera Anthu
20. (a) Kodi kuukira kwa Satana kwakhala kopambana motani? (b) Kodi nchifukwa ninji tingayembekezere kuti kawirikawiri njira zake zikawonekera kukhala zopanda liwongo, ngakhale zopindulitsa?
20 Musaganize kuti njira za Satana zochititsira anthu kumtsatira nthawi zonse zimakhala zosavuta kuwona. Iye ndikatswiri pa kunyenga anthu. Njira zake mkati mwa zaka zikwi zambiri, kunena zowona, zakhala zochenjera kwambiri chakuti lerolino anthu ambiri samakhulupirira konse kuti iye aliko. Kwa iwo kuipa ndi choipa ziri chabe mikhalidwe yachibadwa imene idzakhalako nthawi zonse. Satana amagwira ntchito mofanana kwambiri ndi atsogoleri a upandu amakono amene amavala chinyawu cha kukhala olemekezeka, koma amene, kutseri, amachita zinthu zoipa kwambiri. Baibulo limafotokoza kuti: “Satanayemwe adziwonetsa ngati mngelo wa kuwunika.” (2 Akorinto 11:14) Motero tingayembekezere kuti njira zake zosochezera anthu kawirikawiri zikawonekera kukhala zopanda liwongo ndipo ngakhale zopindulitsa.
21. Kodi ndinjira imodzi yotani imene Satana wagwiritsira ntchito?
21 Kumbukirani kuti Satana anayerekezera kukhala bwenzi kwa Hava. Ndiyeno iye anamnyenga kulowa m’kuchita chimene Havayo anaganizira kuti chikakhala chabwino kwa iye (Genesis 3:4-6) Kuli chimodzimodzi lerolino. Mwa chitsanzo, kupyolera mwa oimira ake aumunthu Satana mochenjera amalimbikitsa anthu kuika zabwino za maboma aanthu ngakhale pamwamba pa utumiki wawo kwa Mulungu. Kumeneku kwatulutsa mzimu wa utundu, wochititsa nkhondo zowopsa. M’nthawi zaposachedwapa Satana wasonkhezera anthu kupanga njira zosiyanasiyana m’kufunafuna kwawo mtendere ndi chisungiko. Imodzi ya zimenezi ndiyo Mitundu Yogwirizana. Koma kodi imeneyi yapanga dziko lamtendere? Kutalitali! M’malo mwake, yatsimikizira kukhala njira yochotsera maganizo a anthu ku kakonzedwe ka Mulungu kodzetsera mtendere kwa anthu, ufumu wake ulinkudzawo pansi pa Yesu Kristu, “Karonga wa Mtendere.”—Yesaya 9:6; Mateyu 6:9, 10.
22. Kodi ndichidziwitso chotani chimene Satana sakufuna kuti tikhale nacho?
22 Ngati titi tilandire moyo wosatha, tifunikira chidziwitso cholongosoka chonena za Mulungu, Mwana wake Mfumu ndi ufumu wake. (Yohane 17:3) Mungatsimikizire kuti Satana Mdyerekezi sakufuna kuti mukhale ndi chidziwitso chimenechi, ndi kuti iye adzachita zonse zimene angathe kukuletsani kuchipeza. Kodi iye adzachita zimenezi motani? Njira imodzi ndiyo mwa kulinganiza kuti mulandire chitsutso, mwina mwake mu mpangidwe wa chinyodolo. Baibulo limatiuza kuti: “Awo onse ofuna kukhala ndi moyo limodzi ndi kudzipereka kwaumulungu mogwirizana ndi Kristu Yesu adzazunzidwanso.”—2 Timoteo 3:12, NW.
23. (a) Kodi ndimotani mmene Satana angagwiritsire ntchito ngakhale mabwenzi ndi achibale kutilefula? (b) Kodi nchifukwa ninji inu simuyenera kugonjera chitsutso?
23 Kungakhale kwakuti ngakhale mabwenzi enieni kapena achibale adzakuuzani kuti iwo sakufuna kuphunzira kwanu Malemba. Yesu Kristu mwiniyo anachenjezanso kuti: “Ndipo apabanja ake a munthu adzakhala adani ake. Iye wakukonda atate wake, kapena amake koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wakukonda mwana wake wamwamuna, kapena wamkazi koposa Ine, sayera Ine” (Mateyu 10:36, 37) Achibale angayese kukulefulani, akumatero mowona mtima kutheratu chifukwa chakuti iwo sakudziwa chowonadi chodabwitsa chopezam’Baibulo. Koma ngati muleka kuphunzira Mawu a Mulungu pamene chitsutso chifika, kodi Mulungu adzakuwonani motani? Ndiponso, ngati inu muleka, kodi mabwenzi ndi okondedwa amenewo adzathandizidwa motani ndi inu kuzindikira kuti chidziwitso cholongosoka cha Baibulo nchofunika kwambiri? Kukhalabe kwanu ndi zinthu zimene muphunzira m’Mawu a Mulungu m’kupita kwa nthawi kungawayambukire m’njira yofananayo kuphunzira chowonadi.
24. (a) Kodi ndinjira zina zotani zimene Mdyerekezi amagwiritsira ntchito kulepheretsa anthu kupeza chidziwitso chopatsa moyo? (b) Kodi mukulingalira kuti kuli kofunika motani kuphunzira Mawu a Mulungu?
24 Ndiponso, Satana angakhale wochititsa kukuyesani kulowa m’kachitidwe kena koipa, kamene kali kosakondweretsa Mulungu (1 Akorinto 6:9-11) Kapena kungakhale kwakuti iye adzakuchititsani kulingalira kuti muli wotanganitsidwa kwambiri kosati nkuphunzira Baibulo. Koma pamene muganizira, kodi pangakhale chirichonse chofunika kwambiri koposa kupeza mtundu umenewu wa chidziwitso? Musalole chirichonse kukuleketsani kupeza chidziwitso chimenechi chimene chingachititse kulandira kwanu moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi!
25. Ngati tipitiriza kukaniza Mdyerekezi, kodi nchiyani chimene iye sadzakhala wokhoza kutichitira?
25 Baibulo limafulumiza kuti: “Kanizani Mdyerekezi.” Ngati muchita zimenezi, “adzakuthawani.” (Yakobe 4:7) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti ngati ukaniza chiukiro cha Satana iye adzaleka ndi kusakuvutitsanitso? Ayi, iye adzayesa mobwerezabwereza kukuchititsani kuchita zimene akufuna. Koma ngati mupitiriza kumkaniza, iye sadzakuchititsani kutsatira njira yotsutsa Mulungu. Motero, khalani achangu kupeza chidziwitso chofunika kwambiri cha Baibulo ndi kuchita zimene muphunzira. Kumeneku nkofunika kuti kukutetezereni kunyengedwa ndi ina ya njira ya Satana yosochezera anthu, chipembedzo chonyenga.
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Kodi Satana akanalonjeza Kristu maboma adziko onsewa ngati iwo sanali ake?
[Chithunzi patsamba 19]
Mbala iye sinabadwe iri mbala, monga momwedi Mdyerekezi sanalengedwere kukhala “mdyerekezi”
[Chithunzi patsamba 20, 21]
Nkhondo kumwamba inatha ndi kuponyedwa kudziko lapansi kwa Satana ndi ziwanda. Inu tsopano mukumva ziyambukirozo
[Chithunzi patsamba 24]
Pangakhale chitsutso ku kuphunzira kwanu Baibulo kopitiriza