Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/95 tsamba 1
  • Kuyesedwa ndi Yehova—Nchifukwa Ninji Kuli Kwaphindu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyesedwa ndi Yehova—Nchifukwa Ninji Kuli Kwaphindu?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Sungirirani Chikhulupiriro Chanu ndi Umoyo Wauzimu
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Samalirani Thanzi Lanu M’njira Yogwirizana ndi Malemba
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Mumadya Bwino Mwauzimu?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Mungathe Kupeŵa Matenda a Mtima Wauzimu
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 9/95 tsamba 1

Kuyesedwa ndi Yehova—Nchifukwa Ninji Kuli Kwaphindu?

1 Aliyense amafuna thanzi labwino. Limapangitsa moyo kukhala wosangalatsa kwambiri. Komabe, ambiri amene ali ndi thanzi labwino amapimidwa nthaŵi ndi nthaŵi. Chifukwa? Amafunafuna kudziŵa za mavuto ena alionse a umoyo amene angabuke kotero kuti achitepo kanthu kuwathetsa. Zimenezi nzofunika koposa kuti tichinjirize thanzi lathu lauzimu. Chiyanjo cha Yehova chimadalira pa kukhalabe kwathu “olama m’chikhulupiriro.”—Tito 1:13.

2 Tsopano ndiyo nthaŵi yoyenera ya kuyesedwa ndi Yehova. Chifukwa ninji zili choncho? Chifukwa chakuti Yehova ali m’kachisi wake woyera, ndipo akuyesa mitima ya anthu onse. (Sal. 11:4, 5; Miy. 17:3) Mofanana ndi Davide, timapempha Yehova kuti atiyese mokwanira kuti: “Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe; yeretsani imso zanga ndi mtima wanga.”—Sal. 26:2.

3 Tiyenera kukhala maso pa zinthu zimene zingawononge thanzi lathu lauzimu zimene zingatifikire chifukwa cha thupi lopanda ungwiro. Miyambo 4:23 imalangiza kuti: “Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.”

4 Thanzi lathu lauzimu lingawopsezedwenso ndi dziko lotizinga la makhalidwe oipa. Ngati tilola kuyandikirana kwambiri ndi dongosolo ili loipa, tikhoza kuyamba kuganiza monga mmene limaganizira ndi kukulitsa njira zaudziko. Kapena mwina tingatengere moyo wadziko ndi kugonjetsedwa ndi mzimu wa dziko.—Aef. 2:2, 3.

5 Satana angagwiritsire ntchito chizunzo kapena chitsutso chachindunji poyesayesa kuwononga mkhalidwe wathu wauzimu. Komabe, kaŵirikaŵiri iye mwamachenjera amagwiritsira ntchito zinthu zokopa za dziko kutinyenga. Petro akutilimbikitsa ‘kukhala odzisungira ndi kudikira,’ popeza Satana ali “monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire.” Tikulimbikitsidwa ‘kumkaniza ameneyo, kukhala okhazikika m’chikhulupiriro.’—1 Pet. 5:8, 9.

6 Tifunikira kutetezera thanzi lathu lauzimu, kusunga chikhulupiriro chathu chili cholimba mwa kuchilimbitsa tsiku lililonse. Mtumwi Paulo akunena kuti tifunikira kuyesa chikhulupiriro chathu mosalekeza. Monga momwe mwanzeru timamvera uphungu woperekedwa kwa ife ndi dokotala wodziŵa bwino, timamvetseranso Yehova pamene kuyesa Kwake kwauzimu kusonyeza vuto limene lifunikira kuwongoleredwa. Zimenezi zimatikhozetsa “kukonzedwa.”—2 Akor. 13:5, 11, NW.

7 Yehova alidi Woyesa wamkulu. Kupima kwake nthaŵi zonse nkolondola. Amadziŵa kwenikweni zimene tifunikira. Kupyolera m’Mawu ake ndi “kapolo wokhulupirika,” amatipatsa mankhwala a chakudya chauzimu chopatsa thanzi. (Mat. 24:45; 1 Tim. 4:6) Kudya chakudya chomanga thupi chimenechi chauzimu nthaŵi zonse panyumba ndi kumisonkhano ya mpingo kumatikhozetsa kukhala athanzi mwauzimu. Kulimbitsa thupi kwauzimu kwa masiku onse mu utumiki ndi m’ntchito ina Yachikristu kulinso kopindulitsa. Chotero, timayamikira kutiyesa kwa Yehova nthaŵi zonse, tili ndi chidaliro chakuti adzatithandiza kukhala ndi thanzi labwino koposa lauzimu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena