Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/95 tsamba 2
  • Misonkhano Yautumiki ya September

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yautumiki ya September
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira September 4
  • Mlungu Woyambira September 11
  • Mlungu Woyambira September 18
  • Mlungu Woyambira September 25
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 9/95 tsamba 2

Misonkhano Yautumiki ya September

Mlungu Woyambira September 4

Nyimbo Na. 224

Mph. 10: Zilengezo za pamalopo ndi Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu.

Mph. 20: “Msonkhano Wachigawo Upereka Chiitano Chosonkhezera!—Tamandani Yehova Mwachimwemwe Tsiku ndi Tsiku!” Mafunso ndi mayankho.

Mph. 15: “Thandizani Ena Kuti Apindule.” Fotokozani maulaliki osonyezedwawo, ndiyeno sonyezani zitsanzo ziŵiri zachidule.

Nyimbo Na. 204 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 11

Nyimbo Na. 216

Mph. 5: Zilengezo za pamalopo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 22: “Kodi Muyenera Kukhala Anthu Otani?” Mafunso ndi mayankho. Ndime zonse ziyenera kuŵerengedwa.

Mph. 18: “Kodi Ana Anu Mwawaikira Zonulirapo Zotani?” Mafunso ndi mayankho. Itanani wachichepere mmodzi kapena aŵiri kapena okulirapo amene atumikira Yehova kuyambira paubwana wawo kuti asimbe mwachidule za mmene makolo awo anawathandizira kusankha zonulirapo zabwino zozikidwa pa zinthu za Ufumu.

Nyimbo Na. 187 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 18

Nyimbo Na. 168

Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. “Kodi Tinachita Motani m’May?”

Mph. 15: “Gwiritsirani Ntchito Bwino Koposa Magazini Athu.” Nkhani yaumoyo yoperekedwa ndi woyang’anira utumiki, yozikidwa pa ndime 1 mpaka 12 za mphatika.

Mph. 20: “Tsatirani Okondwerera Onse Kuti Mupindulitse Ena.” Fotokozani maulaliki osonyezedwawo a maulendo obwereza. Mbale wosamalira nkhaniyi akukambitsirana ndi ofalitsa aŵiri kapena atatu za zimene adzanena ndiyeno akuwapempha kuchita chitsanzo cha maulaliki awo.

Nyimbo Na. 162 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 25

Nyimbo Na. 177

Mph. 5: Zilengezo za pamalopo.

Mph. 15: “Chitani Zonse ku Ulemerero wa Mulungu.” Kukambitsirana ndi omvetsera kochitidwa ndi mkulu. Ngati nthaŵi ilola, nenani ndemanga zowonjezera zozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya August 15, 1992, masamba 15-20.

Mph. 10: “Kuyesedwa ndi Yehova—Nchifukwa Ninji Kuli Kwaphindu?” Nkhani yolimbikitsa yokambidwa ndi mkulu.

Mph. 15: “Gwiritsirani Ntchito Bwino Koposa Magazini Athu.” Kambitsiranani ndi omvetsera ndime 13 mpaka 16 za mphatika. Gogomezerani kuti pakhale kuyesayesa kwa kugaŵira masabusikripishoni a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! mu October. Popeza kuti magaziniwo amafalitsidwa m’zinenero zosiyanasiyana, tiyenera kuuza anthu a zinenero zachilendo kuti angathe kulembetsa magazini aŵiri onsewo m’chinenero chakwawo. M’gawo lofoledwa kaŵirikaŵiri, kugaŵira magazini athu kungakhale njira yogwira mtima koposa yokulitsira chikondwerero, popeza kuti amapereka chidziŵitso chatsopano mlungu uliwonse. Itanani banja kuti lidzachite chitsanzo cha kuyeseza, monga momwe kwalongosoledwera m’ndime 13. Ndiponso, tchulani malingaliro ena othandiza a kuwonjezera kugaŵirako.

Nyimbo Na. 193 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena