Nyimbo 187
Zinthu Zonse Zipangidwa Kukhala Zatsopano
1. Zinthu zisonya M’lungu alamula.
Pa mpando wakhala Mwana wake.
Munkhondo yam’mwamba walakika,
Ndipo kwatsala dziko lapansi.
(Korasi)
2. Anthu awone Yerusalemuyo,
Mkwatibwi wa Mwanawankhosayo.
Wovekedwa tsono mokongola,
Yehova ndiye kuŵala kwake.
(Korasi)
3. Mzindawu udzasangalatsa anthu.
Ndi zipata zake zosatseka.
Anthu adzayenda mu ku’nika.
Gaŵirani kunyezimirako.
(KORASi)
Kondwa. Chifukwa Mulungu
Alitu ndi anthu ake.
Sikudzakhalanso kulira,
Pena zopweteka ndi imfa;
Zidzakhala zatsopano zonse.
Odalirika mawu.