Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/95 tsamba 8
  • Thandizani Ena Kuti Apindule

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Thandizani Ena Kuti Apindule
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Tsatirani Okondwerera Onse kuti Mupindulitse Ena
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Zitsanzo za Maulaliki a Utumiki wa Kumunda
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Bwererani Kumene Munapeza Wokondwerera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Lalikirani Mwaluntha
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 9/95 tsamba 8

Thandizani Ena Kuti Apindule

1 Yehova amalonjeza kutiphunzitsa zimene tifunika kudziŵa. Amatitsimikizira motere pa Salmo 32:8: “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.” Chitsimikizo chimenechi chili ndi phindu lalikulu kwa ife. Mopanda dyera, tiyenera kusonyeza ena mmene angapindulire mwa kulabadira uphungu wanzeru wa m’Baibulo. (Yes. 48:17) Tingachite zimenezi m’September mwa kugaŵira buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha. Popereka maulaliki athu, pali njira zosiyanasiyana zimene tingasonyezere phindu lake la Baibulo.

2 Chifukwa cha kuchuluka kwa zothetsa nzeru m’maukwati lerolino, mungasankhe kugwiritsira ntchito lingaliro lotsatirali la m’buku la “Kukhala ndi Moyo Kosatha”:

◼ “Anthu ochuluka omwe ndalankhula nawo akuda nkhaŵa ndi kuwonjezeka kwakukulu kwa kusoŵa chimwemwe m’maukwati ndi zisudzulo. Kodi muganizapo bwanji pa vuto limeneli? [Yembekezani yankho.] Ambiri alephera kuona zinthu zazikulu zochititsa zimenezo. Ngati mabanja ayesayesa mwa khama, angapulumutse maukwati awo ndi kupezanso chimwemwe chenicheni. Chinsinsi chake chili pa kugwiritsira ntchito uphungu wopezeka m’Baibulo.” Ŵerengani Aefeso 5:28, 29, 33. Tsegulani patsamba 243, kambitsiranani ndime 16 ndi 17, ndiyeno gaŵirani bukulo pa chopereka chake.

3 Ana amafuna nthaŵi ndi maphunziro opindulitsa kwa makolo awo. Pogaŵira buku la “Kukhala ndi Moyo Kosatha,” munganene kuti:

◼ “Tonsefe timafuna kuti ana athu akakhale ndi mtsogolo mwabwino. Malinga ndi kuganiza kwanu, kodi njira yabwino koposa imene makolo angathandizire ana awo kukhala ndi mtsogolo mosungika njotani? [Yembekezani yankho.] Tamvetserani uphungu uwu wa mwambi wa m’Baibulo wolembedwa pafupifupi zaka 3,000 zapitazo. [Ŵerengani Miyambo 22:6.] Pamene kuli kwakuti ana athu angapindule ndi malangizo omwe amalandira kusukulu, maphunziro awo opindulitsa koposa amaperekedwa panyumba ndi makolo awo. Pamafunika nthaŵi, chisamaliro, ndi chikondi, koma kuyesayesa kumeneko nkoyenera kwambiri.” Tsegulani patsamba 245, kambitsiranani ndime 20 ndi 21, ndiyeno fotokozani mmene angagŵiritsirire ntchito bukulo pa phunziro la Baibulo labanja.

4 Mungafune kugaŵira buku la “Kukhala ndi Moyo Kosatha” mwa kusonyeza mmene dziko lapansi lidzakhalira paradaiso:

◼ “Ndikhulupirira kuti mumafuna kudziŵa mmene moyo wanu udzakhalira mtsogolo. M’Pemphero la Ambuye, Yesu anatiphunzitsa kupempherera chifuniro cha Mulungu kuti chichitidwe pansi pano monga kumwamba. Kodi dziko lapansi lidzakhala lotani zitachitika zimenezo? [Yembekezani yankho.] Nachi chithunzithunzi chosonyeza dziko la paradaiso. [Sonyezani chithunzithunzi chimene chili pamasamba 12 ndi 13. Ndiyeno ŵerengani lemba la Yesaya 11:6-9, limene lili m’ndime 12.] Kodi kukhala ndi moyo m’dziko lotere sikungakhale kwabwino? Bukuli lidzakusonyezani mmene inuyo ndi banja lanu mungakhalire m’paradaiso wonga uyu.”

5 Kukonzekera ulaliki wanu pasadakhale kungakuthandizeni kwambiri kukhoza pakhomo la munthu. Musanagogode, tsimikizirani kuti muli nako kanthu kena konena pa lingaliro la Malemba. Ndiponso, khalani ndi ndemanga yachidule m’maganizo ponena za mfundo ina yosangalatsa ya magazini kapena trakiti imene mudzafuna kugaŵira ngati buku silinatengedwe. Pezeranipo mwaŵi panthaŵi yabwino iliyonse imene muli nayo wa kufesa mbewu za choonadi cha Ufumu m’September. (Mlal. 11:6) Mudzakhala mukuthandiza ena kupeza mapindu osatha.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena