Nyimbo 204
“Ndine Pano! Munditumize Ine”
1. Lero anthu alitonza
Dzina labwino la Mlungu.
Ena amyesa wankhanza.
Atinso “palibe Mlungu!”
Ndani adzayeretsadi
Dzina lake la Mulungu?
“Mbuye, ine ndiri pano!
Ndidzaimba za inuyo;
(Korasi)
2. Anthu anyoza za Mlungu;
Alibe mantha za iye.
Ena alambira fano;
Ndi kutama Kaisara.
Adzawachenjeza ndani
Za nkhondo yaikuluyo?
“Mbuye, ine ndiri pano!
Ndidzachenjeza zolimba;
(Korasi)
3. Lero ofatsa alira
Chifukwa cha zoipazi.
Mowona afunafuna
Chowonadi chomasula.
Ndani adzawatonthoza
Akufuna chilungamo?
“Mbuye, ine ndiri pano!
Ndidzaphunzitsa ofatsa;
(KORASI)
Palibenso ulemu wina.
Mbuye, munditumize!”