Kodi Ana Anu Mwawaikira Zonulirapo Zotani?
1 Chipambano m’moyo chimadalira pa kukhala ndi zonulirapo zoyenera ndi kuzifikira. Aja amene amalondola zonulirapo zosanunkha kanthu kapena zonkitsa amangogwiritsidwa mwala nakhala osakhutira. Pamafunika nzeru kuti munthu azindikire zonulirapo zomwe ayenera kulondola kuti “akagwire moyo weniweniwo.” (1 Tim. 6:19) Ndife oyamikira chotani nanga kuti Yehova, mwa Mawu ake ndi gulu lake, amatisonyeza njira yeniyeni yoyendamo!—Yes. 30:21.
2 Mwa kupereka chitsogozo chotero chachikondi, Yehova amaikira makolo chitsanzo chabwino. M’malo mongosiyira ana achibwana kuti adzisankhire okha njira yabwino koposa, makolo anzeru amawalangiza njira imene ayenera kuyendamo, ndipo atakalamba, “sadzachokamo.” (Miy. 22:6) Malinga ndi kudziŵa kwawo, makolo Achikristu amazindikira kuti sayenera kudalira nzeru zawo; ayenera kudalira Yehova. (Miy. 3:5, 6) Ndipotu ana, pokhala ndi chidziŵitso chochepa, amafunika zimenezi kwambiri.
3 Makolo angaikire ana awo zonulirapo zoyenera zimene zidzawathandiza kusumika maganizo pa “zinthu zofunika kwambiri.” (Afil. 1:10, NW ) Angayambe ndi phunziro labanja, akumalimbikitsa ana kuzindikira kufunika kwake ndi kulangizidwa nalo. Ndi bwino ngati ana akhala ndi chizoloŵezi cha kuchita phunziro pasadakhale kaamba ka misonkhano ya mpingo ndi kukonzekera kukayankha m’mawu awo. Kuchita ntchito yolalikira nthaŵi zonse nkofunika. Ana aang’ono angachirikize mwa kugaŵira matrakiti, kuŵerenga malemba, kapena kugaŵira magazini. Pamene adziŵa kuŵerenga, kulembetsa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki kungafulumize kupita kwawo patsogolo. Kuyenerera kukhala wofalitsa wosabatizidwa kapena kuloledwa kubatizidwa ndiko kupita patsogolo kwambiri.
4 Pamene ana awo ayandikira zaka zaunyamata, kapena ngakhale akali ocheperapo, makolo ayenera kulankhula nawo moona mtima za ntchito zimene zingakhale zonulirapo zawo. Aphungu a sukulu ndi mabwenzi a m’kalasi angawasonkhezere mosavuta kusankha ntchito zapamwamba za kudziko. Makolo ayenera kuthandiza ana awo kusankha maphunziro akusukulu amene amaphunzitsa ntchito, kuwakonzekeretsa kuti akasamalire zofuna zawo zakuthupi popanda kunyalanyaza zinthu za Ufumu. (1 Tim. 6:6-10) Angawalimbikitse kukulitsa ‘mphatso’ ya umbeta, ndiyeno ngati adzafuna kukwatira pambuyo pake, adzakhoza kusenza mathayo olemera a ukwati. (Mat. 19:10, 11; 1 Akor. 7:36-38) Mwa kulankhula zolimbikitsa ponena za upainiya, kutumikira kumene kusoŵa kuli kokulira, utumiki wa pa Beteli, kapena ntchito ya umishonale, makolo angakhomereze mwa ana chikhumbo cha kugwiritsira ntchito moyo wawo mwa njira yokondweretsa Yehova, yopindulitsa ena, ndi yodzetsa madalitso kwa iwo ngakhale akali aang’ono.
5 Sizinachitike mwangozi kuti tikhale ndi achichepere ambiri m’gulu lerolino amene amatsatira miyezo yapamwamba Yachikristu ndi amene amalondola zonulirapo zateokrase. Amene atheketsa zonsezo ndi makolo awo achikondi. Ngati ndinu kholo, kodi ana anu alunjika kuti? Kodi akupita patsogolo kulinga ku moyo wokonda zinthu za Ufumu? Kumbukirani, chimodzi cha zinthu zofunika koposa chimene mungachite ndicho kukhomereza choonadi mwa ana anu, ndi kuchilankhula masiku onse. Mungadalitsidwe ndi banja lokhulupirika pa kutumikira Yehova.—Deut. 6:6, 7; Yos. 24:15.