Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/11 tsamba 7
  • Phunzitsani Ana Anu Kuti Adzakhale Atumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Phunzitsani Ana Anu Kuti Adzakhale Atumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Nkhani Yofanana
  • Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Makolo—Phunzitsani Ana Anu Kuyambira Ukhanda Wawo
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Kodi Ana Anu Mwawaikira Zonulirapo Zotani?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Makolo Ayenera Kuphunzitsa Ana Awo Kukonda Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
km 1/11 tsamba 7

Phunzitsani Ana Anu Kuti Adzakhale Atumiki

1. Kodi lemba la Salimo 148:12, 13 limalimbikitsa makolo achikhristu kuchita chiyani?

1 Yehova amafuna kuti achinyamata azimutamanda. (Sal. 148:12, 13) Choncho, makolo achikhristu samangophunzitsa ana awo choonadi cha m’Baibulo ndi malamulo a Mulungu okhudza makhalidwe abwino. Iwo amawaphunzitsanso kuti adzakhale atumiki a uthenga wabwino. Kodi angachite bwanji zimenezi pang’onopang’ono?

2. Kodi chitsanzo chabwino cha kholo chingakhudze bwanji ana?

2 Chitsanzo Chabwino: Woweruza Gidiyoni anauza asilikali ake 300 kuti: “Muonetsetse ndi kuphunzira pa zimene ine ndikuchita.” (Ower. 7:17) Mwachibadwa ana amaonetsetsa ndi kutsatira zimene makolo awo amachita. Mwamuna wina amagwira ntchito usiku, koma m’malo mofikira kugona m’mawa wa Loweruka, iye amatenga ana ake n’kupita nawo mu utumiki ngakhale kuti amakhala ali wotopa kwambiri. Zomwe amachitazi zimaphunzitsa anawo kudziwa kuti utumiki ndi wofunikira. (Mat. 6:33) Kodi ana anu amakuonani mukuchita mosangalala mbali zosiyanasiyana za kulambira monga kupemphera, kuwerenga Baibulo, kuyankha pa misonkhano komanso kulalikira? Ndi zoona kuti simungachite kukhala chitsanzo chabwino kwambiri. Komabe, ana anu adzaphunzira kulambira Yehova ngati ataona kuti inuyo mumachita khama kumutumikira.—Deut. 6:6, 7; Aroma 2:21, 22.

3. Kodi ndi zolinga zauzimu zotani zimene makolo angathandize ana awo kukhala nazo ndiponso kuzikwaniritsa?

3 Muziwaikira Zolinga Nthawi Zonse: Makolo satopa kuphunzitsa ana awo kuyenda, kulankhula, kuvala okha ndi zina zambiri. Anawo akamakula n’kumakwaniritsa zolingazo, makolo amawaikira zolinga zina zatsopano. Ngati makolowo ndi Akhristu, amathandizanso ana awo kukhala ndi zolinga zauzimu ndiponso kuzikwaniritsa. Zolingazo zimakhala zoti akhoza kuzikwanitsa komanso zogwirizana ndi zaka zawo. (1 Akor. 9:26) Kodi mukuwaphunzitsa ana anu kupereka ndemanga m’mawu awoawo komanso kukonzekera nkhani zawo za mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu? (Sal. 35:18) Kodi mukuwaphunzitsa kuchita utumiki wosiyanasiyana? Kodi mukuwathandiza kukhala ndi cholinga chobatizidwa ndiponso kuyamba utumiki wanthawi zonse? Kodi mumawathandiza kuzolowerana ndi anthu amene amachita utumiki mosangalala komanso ndi mtima wonse kuti aziwalimbikitsa?—Miy. 13:20.

4. Kodi ana amene makolo awo amawaphunzitsa utumiki adakali aang’ono amapindula motani?

4 Wamasalimo anati: “Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira pa unyamata wanga, ndipo mpaka pano ndikunena za ntchito zanu zodabwitsa.” (Sal. 71:17) Yambani kuphunzitsa ana anu adakali aang’ono kuti adzakhale atumiki. Kuchita zimenezi kungakhale kuyala maziko a zinthu zimene zingawathandize panopa mpaka akadzakula.—Miy. 22:6.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena