Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/02 tsamba 8
  • Makolo—Phunzitsani Ana Anu Kuyambira Ukhanda Wawo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Makolo—Phunzitsani Ana Anu Kuyambira Ukhanda Wawo
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Nkhani Yofanana
  • Makolo, Kondwerani mwa Ana Anu
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Phunzitsani Ana Anu Kuti Adzakhale Atumiki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Makolo Ayenera Kuphunzitsa Ana Awo Kukonda Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Onani Zambiri
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 1/02 tsamba 8

Makolo—Phunzitsani Ana Anu Kuyambira Ukhanda Wawo

1 “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.” (Miy. 22:6) Ngati inu makolo simukufuna kuti ana anu ‘achoke’ panjira ya choonadi, ndi liti pamene mufunika kuyamba kuwaphunzitsa? Adakali aang’ono!

2 Mmene Paulo amanena kuti Timoteo anaphunzitsidwa zauzimu “kuyambira ukhanda,” mwachionekere anatanthauza kuyambira pamene anali mwana wamng’ono. (2 Tim. 3:14, 15) Ndiye chifukwa chake Timoteo anakula nakhala munthu wabwino wokonda zauzimu. (Afil. 2:19-22) Inunso makolo muyenera kuphunzitsa ana anu “kuyambira ukhanda” zimene afunika kuti ‘akule pamaso pa Yehova.’—1 Sam. 2:21.

3 Apatseni Madzi Ofunika Kuti Akule: Mofanana ndi timitengo tanthete timene timafuna madzi nthaŵi zonse kuti tikule kukhala mitengo yaikulu, ananso a misinkhu yonse afunika madzi ambiri a choonadi cha m’Baibulo kuti akule nakhale atumiki okhwima a Mulungu. Njira yaikulu yophunzitsira ana choonadi ndi kuwathandiza kum’dziŵa Yehova ndiyo phunziro la Baibulo la banja lokhazikika. Koma mufunika kukumbukira nthaŵi imene mwana aliyense amatha kukhala wachidwi. Kwa ana aang’ono, zimene zingathandize kwambiri ndi kuphunzira nawo nthaŵi zambiri zigawo zifupizifupi kusiyana ndi kuphunzira nthaŵi yaitali maulendo ochepa.—Deut. 11:18, 19.

4 Musachepse nzeru zophunzirira zimene ana ali nazo. Asimbireni nkhani za anthu ofotokozedwa m’Baibulo. Auzeni kujambula zithunzi za malo ndi zochitika za m’Baibulo kapena kuchita seŵero la zochitikazo. Gwiritsani ntchito bwino mavidiyo athu ndi makaseti, kuphatikizapo a maseŵero a m’Baibulo. Sinthani phunziro la banja kuti ligwirizane ndi misinkhu ya ana anu ndi nzeru zawo za kuphunzira. Poyamba muzim’phunzitsa zinthu pang’ono, zosavuta, koma pamene akukula, muyenera kuwonjezera zomwe mukum’phunzitsa komanso liŵiro lake. Onetsetsani kuti phunzirolo ndi losangalatsa. Liphatikizeponso zinthu zosiyanasiyana. Inuyo mukufuna kuti ana anuwo akhale ndi “chilakolako” cha Mawu, choncho yesetsani kuti phunzirolo lizikhala lokoma.—1 Pet. 2:2, NW.

5 Aphatikizeni m’Zochitika pa Mpingo: Aikireni zolinga zoti angapite nazo patsogolo kuti azitenga nawo mbali kwambiri m’zochitika pa mpingo. Kodi cholinga choyamba chingakhale chiyani? Makolo ena a ana aŵiri ang’onoang’ono anati: “Ana athu aŵiri tinayamba kuwaphunzitsa kukhala chete m’Nyumba ya Ufumu.” Kenako athandizeni ana kuyankha pamisonkhano m’mawu awoawo ndi kuti akhale ndi cholinga cholembetsa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase. Mu utumiki wa kumunda, zolinga zabwino zofuna kuzikwaniritsa zingakhale kugaŵira thirakiti pakhomo la munthu, kuŵerenga lemba, kuchita ulaliki wa magazini, ndi kukambirana ndi eninyumba zinthu zatanthauzo.

6 Aikireni Chitsanzo Chabwino cha Changu: Kodi ana anu amakumvani masiku onse mukulankhula za Yehova, kupemphera kwa iye? Kodi amakuonani mukuphunzira Mawu ake, kupezeka pamisonkhano, kupita mu utumiki wa kumunda, ndi kusangalala kuchita chifuniro cha Mulungu? (Sal. 40:8) M’pofunika kuti azikuonani mukutero ndi kuti muzichitira nawo limodzi zinthu zimenezi. Mwana wina wamkazi amene ndi wamkulu tsopano ananena za amayi ake amene analera ana asanu ndi mmodzi mpaka onse atakhala Mboni zokhulupirika. Anati: “Zimene zinatisangalatsa kwambiri ndi chitsanzo cha amayi—chinali champhamvu kuposa mawu.” Kholo lina la ana anayi linati: “Tinkakonda kunena mawu akuti ‘Yehova ndiye woyamba.’ Koma sizinali kungothera chabe m’kulankhula. Pamoyo wathu wonse tinali kutsata zomwezo.”

7 Makolo, yambani kulangiza ana anu akali aang’ono, kuwaphunzitsa choonadi cha Mawu a Mulungu, kuwaikira zolinga zoti angapite nazo patsogolo ndi kuwaikira chitsanzo chabwino kwambiri. Mukatero, simudzachita chisoni koma mudzasangalala kwambiri!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena