Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/07 tsamba 4
  • Phunzitsani Ana Anu Kutamanda Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Phunzitsani Ana Anu Kutamanda Yehova
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Kuthandiza Ena Kulambira Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Phunzitsani Ana Anu Kuti Adzakhale Atumiki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Makolo—P̃hunzitsani Ana Anu kulalikira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 5/07 tsamba 4

Phunzitsani Ana Anu Kutamanda Yehova

1. Kodi ana angathe kutamanda Yehova?

1 Lemba la Salmo 148:12, 13 limalimbikitsa anyamata ndi atsikana kuti “alemekeze dzina la Yehova.” M’malemba muli zitsanzo zambirimbiri za ana amene anachita zimenezi. Mwachitsanzo “Samueli anatumikira pamaso pa Yehova akali mwana.” (1 Sam. 2:18) “Buthu” ndi limene linauza mkazi wa Namani kuti mneneri wa Yehova ku Isiraeli angathe kuchiritsa khate la mwamuna wake. (2 Maf. 5:1-3) Yesu atalowa m’kachisi n’kuchita zozizwitsa, “anyamata” ndiwo ankafuula kuti: “Apulumutsidwe Mwana wa Davide!” (Mat. 21:15) Kodi makolo angaphunzitse bwanji ana awo kutamanda Yehova?

2. N’chifukwa chiyani makolo amafunika kupereka chitsanzo chabwino kwa ana awo?

2 Chitsanzo Chanu: Asanakhomereze choonadi m’mitima mwa ana awo, atate achiisiraeli analangizidwa kuti, ayambe ndi iwowo kukonda Yehova ndi kukhomereza malamulo ake m’mitima mwawo. (Deut. 6:5-9) Mukamakonda kunena nkhani zolimbikitsa zokhudza utumiki komanso n’kuchita utumiki mlungu uliwonse, ana anu sangavutike kuona kuti utumiki n’ngofunikira ndiponso n’ngosangalatsa.

3. Kodi mlongo wina anathandizidwa bwanji ndi chitsanzo cha makolo ake?

3 Mlongo wina akukumbukira kuti: “Ndili mwana, Loweruka ndi Lamlungu lililonse banja lathu linkalowa m’munda. Zinali zoonekeratu kuti makolo anga ankakonda kulalikira. Motero ana tonse m’banja mwathu tinakula tikuona kuti utumiki ndi ntchito yosangalatsa.” Mlongo ameneyu anakhala wofalitsa wosabatizidwa ali ndi zaka 7 ndipo tsopano wakhala akuchita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zopitirira 32.

4. Kodi mungaphunzitse bwanji ana anu kuti apite patsogolo?

4 Aphunzitseni Kuti Apite Patsogolo: Pochita utumiki muzitenganso ana anu. Auzeni kuti agogode kapena kuodira, kupereka kapepala kwa mwininyumba, kapenanso kuwerenga lemba. Zimenezi zingathandize kuti azisangalala ndi utumiki ndiponso kuti akhale opanda mantha kuuza ena uthenga wa Ufumu. Akamakula, anawo aziwonjezeranso ntchito imene akuchita mu utumiki. Motero, athandizeni kupita patsogolo ndi kukhala ndi zolinga zauzimu.

5. Kodi n’chiyani chimafunika kuti mwana ayeneretsedwe kukhala wofalitsa wosabatizidwa?

5 Uzani akulu mukangoona kuti ana anu akuyenerera kukhala ofalitsa osabatizidwa ndiponso anawo akanena kuti akufuna kutero. Kukhala wofalitsa kumawathandiza kuona kufunika kwa udindo wawo wotamanda Yehova. Komano musaiwale kuti, kuti mwana ayenerere kukhala wofalitsa, safunikira kufika podziwa zinthu zambiri ngati munthu wamkulu wobatizidwa. Kodi mwana wanuyo amamvetsa mfundo zofunikira kwambiri za m’Baibulo? Kodi amatsatira mfundo za m’Baibulo za khalidwe labwino? Kodi amafuna kuchita nawo utumiki ndi kudziwika ngati wa Mboni za Yehova? Ngati ndi choncho, akulu angaone kuti n’ngoyenerera kukhala ofalitsa osabatizidwa.—Onani buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, tsamba 79 mpaka 82.

6. N’chifukwa chiyani kuphunzitsa ana anu kuli kopindulitsa?

6 Pamafunika khama kuti tiphunzitse ana kutamanda Yehova mochoka pansi pamtima. Komabe kuona ana awo akupita patsogolo mwauzimu kumasangalatsa makolo zedi kuposa zinthu zambiri. Ndipotu chofunika kwambiri n’chakuti Yehova amasangalala ana akamauza ena za ntchito zake zodabwitsa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena