Makolo—Phunzitsani Ana Anu kulalikira
1 Mipingo yathu njodala chifukwa cha ana amene amakondadi kutumikira Mulungu. (Mlal. 12:1) Iwo ali pakati pa ana omwe Yehova akuitana kuti amtamande. (Sal. 148:12-14) Chotero, makolo akamaphunzitsa ana awo tsiku ndi tsiku ayeneranso kuwalangiza mmene angauzire ena za chikhulupiriro chawo pantchito yolalikira Ufumu.—Deut. 6:6, 7.
2 Phunzitsani Ana Njira Zopitira Patsogolo: Ana ayenera kuphunzitsidwa adakali aang’ono kwambiri kumatsagana ndi makolo awo ku utumiki. Musanapite ku utumiki, athandizeni ana anu kukonzekera kukatengamo mbali. Auzeni pasadakhale zimene adzachita pamakomo. Ana aang’ono kwambiri angagaŵire matrakiti ndi kuitanira anthu ku Nyumba ya Ufumu. Ana amene amaŵerenga bwino mungawapemphe kuŵerenga malemba pakhomo. Angagaŵire magazini, mwakugwiritsira ntchito ulaliki waufupi. Mmene luso lawo likukula, aphunzitseni kugwiritsira ntchito Baibulo paulaliki wawo. Ofalitsa aang’ono ambiri ayamba njira zamagazini zawozawo ndipo amapanga maulendo obwereza kaŵirikaŵiri. Zimakhala bwino kuti mwana agwire ntchito ndi wachikulire osati ndi mwana mnzake. Wachikulireyo angauze mwini nyumba kuti mwanayo akuphunzira kulalikira.
3 Mtsikana wina wamng’ono anapempha kuti akulu amthandize kuti ayenerere kukhala wofalitsa Ufumu. Ngakhale anali wazaka zisanu zokha panthaŵiyo ndipo sanali kudziŵa nkuŵerenga komwe, anali kupereka uthenga wa Ufumu mogwira mtima pamakomo. Anali kungoloŵeza tsamba pamene panali malemba, nkulivundukula, kenako nkumpempha mwini nyumbayo kuwaŵerenga, ndiyeno iye nkufotokoza.
4 Ana ayeneranso kuphunzitsidwa mwa chitsanzo cha makolo ubwino wakukhala ndi ndandanda yabwino yotengamo mbali kaŵirikaŵiri mu utumiki. Makolo afunikira kukhazikitsa ndandanda yosasinthasintha ya mlungu uliwonse yoloŵera mu utumiki ndipo aziitsatira, kuti anawo azidziŵa kuti ndi masiku ati a mlungu amene nthaŵi zonse amapatulidwa kukhala a ntchito yolalikira.
5 Ngati muwaphunzitsa ana adakali aang’ono kukonda utumiki ndi kusangalala nawo, adzasonkhezereka kukalimira maudindo ena okulirapo mtsogolo, mwinanso utumiki waupainiya. (1 Akor. 15:58) Tonsefe tiyeni tiziwalimbikitsa ana amene ali nafe kupita patsogolo monga atamandi a Yehova.