Chitani Zonse ku ulemerero wa Mulungu
1 Nkotsitsimula chotani nanga kuyanjana ndi abale ndi alongo athu okondedwa! (1 Akor. 16:17, 18) Timachita zimenezi pamisonkhano yampingo, yadera, yachigawo, ndi mu utumiki wakumunda. Timayanjananso panthaŵi za kucheza, monga ngati pamene alendo afika panyumba pathu. Potero, timasonyeza kuchereza ndipo timalimbikitsana wina ndi mnzake. (Aroma 12:13; 1 Pet. 4:9) Polinganiza mapwando aukwati, kumbukirani uphungu wabwino wa mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1984.
2 Kucheza Kolinganizidwa: ‘Tingakhale tidya, tingakhale timwa, tingakhale tichita kanthu kena,’ tiyenera ‘kuchita zonse ku ulemerero wa Mulungu.’ (1 Akor. 10:31-33) Ena samamvera uphungu umenewu, ndipo mavuto amapitiriza kukhalapo chifukwa cha anthu ochuluka amene sangalamulirike bwino pamacheza. Nthaŵi zina, mazana a anthu amaitanidwa kumacheza ambambande kumene kumakhala chikondwerero chaudziko. Macheza otero amafanana kwambiri ndi a dziko, amene mzimu wake uli wosiyana ndi kudekha ndi miyezo ya Baibulo.—Aroma 13:13, 14; Aef. 5:15-20.
3 Kwasimbidwa kuti Mboni zochuluka kwambiri zasonkhana pamalo opempha kumene zikondwerero zake zimakhala zoipa ndi zaudziko ndi kumene kulibe uyang’aniro weniweni. Chifukwa cha kukhala kovuta kuyang’anira magulu aakulu amenewo, pabuka mavuto. Kusasamala zinthu, kumwetsa zakumwa zaukali, ndipo ngakhale chisembwere chachitika nthaŵi zina. (Aef. 5:3, 4) Macheza amene ali ndi khalidwe lotero samalemekeza Yehova. M’malo mwake, amatonzetsa dzina labwino la mpingo ndi kukhumudwitsa ena.—1 Akor. 10:23, 24, 29.
4 Akristu amalimbikitsidwa kuchereza ena, koma chigogomezero chake chili pa kulimbikitsana mwauzimu. (Aroma 1:11, 12) Macheza a anthu ochepa kaŵirikaŵiri ndiwo abwino kwambiri. Buku lathu la Uminisitala pamasamba 135-6 limati: “Nthaŵi zina, mabanja angapo angaitanidwire kunyumba kaamba ka utsamwali Wachikristu. . . . Kwenikweni, awo amene ali oitana m’zochitika zoterozo ayenera kuona kukhala athayo iwo eni kaamba ka zimene zikuchitika. Pokumbukira zimenezi, Akristu ozindikira aona nzeru yochepetsa ukulu wa magulu oterowo ndi utali wa kusonkhanako.” Yesu anasonyeza kuti sipamafunikira kanthu kena kambambande pamene chonulirapo chathu chili cha kulimbikitsa mabwenzi athu mwauzimu.—Luka 10:40-42.
5 Kuchereza Akristu anzathu ndi chinthu chabwino. Komabe, pali kusiyana kwakukulu pakati pa macheza oyenera panyumba pathu ndi ambambande osonyeza mzimu wa dziko pamalo opempha. Pamene muitana ena kudzakhala alendo anu, muyenera kutsimikizira kuti mudzakhala ndi thayo lonse la zimene zidzachitika.—Onani Nsanja ya Olonda ya August 15, 1992, masamba 17-20.
6 Zoonadi, Yehova watidalitsa ndi ubale umene timapezamo chilimbikitso chotsitsimula chimene chimatisonkhezera kupitiriza kuchita ntchito zabwino. (Mat. 5:16; 1 Pet. 2:12) Mwa kukhala odekha ndi osapambanitsa pamacheza, nthaŵi zonse tidzalemekeza Mulungu wathu ndi kumangirira ena.—Aroma 15:2.