Nyimbo 162
“Lalika Mawu”!
1. ‘Lalikirani Mawuwo,’
Walamula leroli.
Ife tapatsidwa nthaŵi
Kumvera lamulolo.
“Lalika” ndi kuphunzitsa;
Thandizani ofo’ka.
Lalikabe, osawopa
Pamakwalala ponse.
2. “Lalika” munyengo yonse,
Wokonzeka kuyankha
Aliyense wakufunsa
Chiyembekezo chathu.
“Lalika” mopanda nyengo
Otsutsa alekeni.
Khala wokhulupirika;
Kwa M’lungu wamkuluyo.
3. “Lalika” mosalekeza.
Onse chonde amvetu!
Kuipa kuli kukula
Mapeto akufika.
“Lalika” mupulumuke
Inu ndi anthu ena.
“Lalika,” nthaŵi yafika
Kutamanda Yehova.