Nyimbo 168
Kuzindikira Mfumu Yatsopano ya Dziko Lapansi
1. Tawonani padzikoli
Chondikondweretsadi—
Gulu lake la Yehova
Muumodzi liyenda.
Zisoti zawo ziŵala,
Ndi kuchotsatu zolakwa.
Afuula molimbika:
“Kristu alamulira.”
(Korasi)
2. Mfumu Kristu, atsogoza;
Ndipo amamtsatira.
Ponena iye amvera
Kulibenso chisoni.
Lupanga lakuthwa Mawu.
Avala iwo mbiriyo.
Amlondola Mbuye wawo;
Kufikira kuimfa.
(Korasi)
3. Tsono nthaŵi yafikatu
Yakulamula Yesu.
Adani onse adzagwa;
Nadzagwidwa ndi mantha.
Yehova achita mphamvu.
Ndi kulizanso lipenga.
Chenjerani mafumunu;
Etu muvomereze.
(KORASi)
Mpsopsonenitu Mwanayo
Kuti mungatayike.
Achimwemwetu
okhulupilira iye!