Kodi Ziletso Zimakulefulani?
ZILETSO! Palibe aliyense amene kwenikweni amazikonda; komabe tonsefe tiyenera kuzipirira kumlingo wina wake. Komabe, kodi mumakhala wolefulidwa nthaŵi zina chifukwa chakuti moyo wanu umaoneka ngati wopanikizika kwambiri? Mwinamwake mungamve bwino ngati mungasinthe kaonedwe kanu ka zinthu. Mmalo movutika mtima ndi zimene simungathe kuchita, bwanji osagwiritsira ntchito bwino lomwe ufulu umene muli nawo?
Mwachitsanzo, anthu ambiri amene ali osauka amakhumba kukhala achuma. Komabe, pamene kuli kwakuti umphaŵi sumatilola kuchita zimene tingathe m’dongosolo lino, zinthu zofunika koposa m’moyo zimapezeka kwa onse. Anthu osauka ndi olemera omwe amakondana, amakwatira, amalera ana, amakhala ndi maubwenzi abwino, ndi zina zotero. Chofunika kwambiri, anthu osauka ndi olemera omwe amadziŵa Yehova ndipo amayembekezera mwachidwi dziko latsopano lolonjezedwa. Anthu osauka ndi olemera omwe amakula m’nzeru Yachikristu ndi chidziŵitso chake, zimene zili zabwino kuposa chuma. (Miyambo 2:1-9; Mlaliki 7:12) Onse—olemera ndi osauka—angadzipangire mbiri yabwino ndi Yehova. (Mlaliki 7:1) M’tsiku la Paulo unyinji umene unapanga mpingo Wachikristu anali anthu apansi—ena a iwo akapolo—amene anagwiritsira ntchito mwanzeru ufulu uliwonse umene mikhalidwe yawo inawapatsa.—1 Akorinto 1:26-29.
Umutu wa m’Malemba
Mu ukwati Wachikristu, mkazi ali wogonjera kwa mwamuna wake—makonzedwe olinganizidwa kupindulitsa banja lonse. (Aefeso 5:22-24) Kodi mkazi ayenera kulingalira kuti zimenezi zimamchepsa? Kutalitali. Mwamuna ndi mkazi wake amachita zinthu mogwirizana. Pamene mwamuna asamalira umutu wake motsanzira Kristu, amaikira mkazi wake ziletso zoŵerengeka chabe ndi kumsiyira mipata yambiri yakuti agwiritsire ntchito maluso ake. (Aefeso 5:25, 31) “Mkazi waluso” wa pa Miyambo chaputala 31 anali wotanganitsidwa ndi ntchito yosangalatsa koma yovuta. Mwachionekere, kugonjera kwa mwamuna wake sikunamlefule.—Miyambo 31:10-29, NW.
Mofananamo, palibe makonzedwe akuti mkazi azitsogolera amuna oyenerera mu mpingo Wachikristu. (1 Akorinto 14:34; 1 Timoteo 2:11, 12) Kodi akazi Achikristu ayenera kunyinyirika chifukwa cha chiletso chimenecho? Ayi. Ochuluka amayamikira poona mbali imeneyo ya utumiki Wachikristu ikusamaliridwa mwateokratiki. Iwo ali okondwa kupeza mapindu a kuŵeta ndi kuphunzitsa kwa akulu oikidwa ndipo amadzitanganitsa ndi ntchito yofunika kwambiri ya kulalikira ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Akazi Achikristu amachita zambiri m’ntchito imeneyi, ndipo zimenezi zimawadzetsera ulemu pamaso pa Yehova Mulungu.—Salmo 68:11; Miyambo 3:35.
Ziletso pa Ana
Nthaŵi zina ana nawonso amadandaula kuti moyo wawo uli ndi ziletso zambiri, kaŵirikaŵiri chifukwa chakuti ali pansi pa ulamuliro wa makolo awo. Komatu zimenezi zilinso za Malemba. (Aefeso 6:1) Mmmalo moipidwa ndi ziletso zimene makolo awo amawaikira, anyamata anzeru Achikristu amasumika maganizo pa kusangalala ndi ufulu umene ali nawo—kaŵirikaŵiri, kuphatikizapo ufulu wa kusakhala ndi mathayo olemera. Motero angagwiritsire ntchito bwino lomwe nyonga yawo yaunyamata ndi mikhalidwe yawo kudzikonzekeretsa kaamba ka uchikulire.
Woyang’anira dera wakale ku Brazil amakumbukira bwino mnyamata wina wazaka 12 m’kagulu kena ka ofalitsa kokhala kutali, amene anali wosakhoza kuchita zinthu zina. Wosamalira zolembapo za mpingo anali wotanganitsidwa ndi ntchito yakuthupi ndipo sankapereka chisamaliro chokwanira ku kaguluko, koma analinganiza kuti mnyamata ameneyu azimthandiza. Iye anadzadziŵa kumene mafomu onse anali kusungidwa ndipo nthaŵi zonse anali kukhalapo kuti athandize. Kufunitsitsa kwake kunali kolimbikitsa, ndipo anali bwenzi lokhulupirika mu utumiki wakumunda. Tsopano mnyamata ameneyo ndi mkulu woikidwa.
Pali mikhalidwe yambiri imene ingachepetse ufulu wa munthu. Ena amalephera kuchita zinthu chifukwa cha matenda. Ena amakhala m’mabanja ogaŵanika ndipo ufulu wawo umachepetsedwa ndi zofuna za mnzawo wa mu ukwati wosakhulupirira. Pamene kuli kwakuti awo okhala ndi ziletso angakonde kuti zinthu zisinthe, iwo angakhalebe ndi miyoyo yokhutiritsa. Magazini ano afalitsa nkhani zambiri ponena za anthu otero amene akhala olimbikitsa kwambiri kwa ena chifukwa chakuti iwo anadalira Yehova nagwiritsira ntchito bwino lomwe mikhalidwe yawo.
Polankhula za mkhalidwe wofala m’tsiku lake, mtumwi Paulo anati: “Kodi unaitanidwa uli kapolo? Usasamalako; koma ngati ukhozanso kukhala mfulu, chita nako ndiko.” (1 Akorinto 7:21) Ha, limenelo lili lingaliro lachikatikati chotani nanga! Mikhalidwe ina imasintha. Achinyamata amakula. Nthaŵi zina wa mu ukwati wotsutsa amalandira choonadi. Mikhalidwe ya zachuma imawongokera. Odwala angachire. M’zochitika zina, zinthu sizingasinthe kufikira dziko latsopano la Yehova litadza. Chikhalirechobe, kodi munthu angapindulenji ngati avutika mtima chifukwa chakuti sangathe kuchita zimene ena angachite?
Kodi munaonapo mbalame zikuuluka m’mwambamwamba ndi kukhumbira mayendedwe ake okongola ndi ufulu umene zimakhala nawo? Mwinamwake munalingalira kuti nanunso mukanauluka motero. Eya, simungatero ndipo simudzakhoza konse kuuluka monga momwe mbalame zimachitira! Koma mwinamwake simumadandaula. Mmalomwake, ndinu wokondwa ndi maluso amene Mulungu anakupatsani. Mukukhala bwino lomwe ngakhale mwa kuyenda kulikonse padziko lapansi. Mofananamo, mulimonse mmene mkhalidwe wathu wa moyo ungakhalire, ngati tisumika maganizo pa zimene tingathe kuchita mmalo movutika mtima ndi zimene sitingathe kuchita, moyo udzakhala wokhutiritsa, ndipo tidzapeza chisangalalo mu utumiki wa Yehova.—Salmo 126:5, 6.
[Chithunzi patsamba 28]
Kodi mumalingalira kuti makolo anu amakutchingirani?