Nyimbo 143
Imani ndi Yehova!
1. Kale tinalitu achisoni,
Kumwa za chipembedzo chonyenga;
Koma mwachimwemwe tadzutsidwa
Pakumva za Ufumu (Ufumu).
(Korasi)
2. Ndi mtima wonse timtumikire
Kugaŵana cho’nadi ponsepo,
Kuthandizira abale onse,
Kutama dzina lake (lakelo).
(Korasi)
3. Sitidzamuwopa Satanayo,
Yehova adzatipulumutsa.
Tingachepe iwo nachuluka,
M’lungu ndi mphamvu yathu (yathudi).
(KORASi)
Ima kwa Yehova; Musekerere.
Sadzakusiyani; Yenda mwa iye.
Nenani mbiriyo Ya ufuluwo.
Kulamula kwake Sikudzathadi.