Khalani Akuchita—Osati Akumva Okha
1 Akristu oona lerolino amalabadira chilangizo cha Baibulo cha kukhala akuchita mawu, osati akumva okha. (Yak. 1:22) Zimenezi zimawasiyanitsa kwambiri ndi aja amene, ngakhale kuti amati ndi Akristu, amangochita utumiki wapakamwa kwa Mulungu. (Yes. 29:13) Yesu ananena momveka bwino kuti aja okha ochita chifuniro cha Mulungu ndiwo adzapulumuka.—Mat. 7:21.
2 Kulambira kopanda ntchito zaumulungu nkopanda tanthauzo. (Yak. 2:26) Chotero tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ntchito zanga zimasonyeza motani kuti chikhulupiriro changa chili chenicheni? Kodi nchiyani chimasonyeza kuti ndimachita mogwirizana ndi zimene ndimakhulupirira? Kodi ndi motani mmene ndingatsanzirire Yesu bwino kwambiri?’ Mayankho oona mtima pamafunso ameneŵa adzatithandiza kuona kupita patsogolo kumene tachita kapena kumene tifunikabe kuchita pochita chifuniro cha Mulungu.
3 Monga otsatira a Yesu, tiyenera kukhala ndi chonulirapo m’moyo chofanana ndi chija chotchulidwa ndi wamasalmo kuti: “Mwa Mulungu tidzitamanda tsiku lonse, ndipo dzina lanu tidzaliyamika kosatha.” (Sal. 44:8) Chikristu ndiwo moyo wathu umene timasonyeza tsiku ndi tsiku ndi zonse zimene timachita. Timapezadi chikhutiro pamene mwa zochita zathu zonse tisonyeza chikhumbo chotamanda Yehova!—Afil. 1:11.
4 Kutamanda Yehova Kumaphatikizapo Zambiri Kuposa Kukhala ndi Moyo Wolungama Chabe: Ngati Mulungu anali kungofuna khalidwe labwino, tikanangolimbikira kuwongolera umunthu wathu. Komabe, kulambira kwathu kumaphatikizaponso kulengeza ponseponse zoposa za Yehova ndi kulengeza poyera dzina lake!—Aheb. 13:15; 1 Pet. 2:9.
5 Kulalikira poyera uthenga wabwino kuli imodzi ya ntchito zofunika koposa zimene timachita. Yesu anadzipereka kuchita ntchito imeneyi chifukwa anadziŵa kuti idzapatsa moyo wosatha kwa iwo akumva. (Yoh. 17:3) Lerolinonso ‘utumiki wa mawu’ ngwofunikabe; ndiwo njira yokha imene anthu angapulumukire. (Mac. 6:4; Aroma 10:13) Pokhala tikuzindikira mapindu ake aakulu, titha kumvetsa chifukwa chake Paulo anatilangiza ‘kulalikira mawu’ ndi ‘kuchita nawo panthaŵi yake.’—2 Tim. 4:2.
6 Kodi tiyenera kutamada Yehova m’moyo wathu kufikira pati? Wamasalmo anati kunali m’maganizo ake tsiku lonse. Kodi si mmenenso timamvera? Inde, ndipo tidzaona nthaŵi iliyonse pamene tikumana ndi munthu wina kukhala yoyenera kulankhula za dzina la Yehova. Tidzafunafuna mpata wabwino wa kusintha makambitsirano athu ndi kuyamba kukambitsirana zauzimu. Tidzayesayesanso kutengamo mbali nthaŵi zonse m’ntchito ya utumiki wakumunda yolinganizidwa ndi mpingo. Aja amene mikhalidwe imawalola angaganizepo kwambiri pa kuthekera kwa kuchita utumiki waupainiya, pakuti zimenezi zimatithandiza kuika ntchito yolalikira patsogolo m’moyo wathu tsiku ndi tsiku. Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti mwa kukhala akuchita chifuniro cha Mulungu mwakhama, tidzapeza chimwemwe.—Yak. 1:25.