Funafunani Ufumu wa Mulungu Choyamba—Mwa Kupereka Nsembe za Chitamando Nthaŵi Zonse
1 Awo amene amafunafuna Ufumu choyamba nthaŵi zonse amakumbukira kulankhula za Yehova ndi kunena za Ufumu wake. (Sal. 145:11-13) Tsiku lililonse limakhala ndi mipata ya kulemekeza dzina lake ndi kulankhula za mbiri yabwino. (Sal. 96:2) Kutamanda Yehova kunakondweretsa wamasalmo amene anati: “Mwa Mulungu tidzitamanda tsiku lonse.” (Sal. 44:8) Ngati tilingalira mofananamo, tidzakhala ofunitsitsa kukhala ndi phande mokhazikika mu utumiki wa Ufumu.
2 Yehova sanaike zofunika zakutizakuti ponena za kuchuluka kwa nthaŵi imene tiyenera kuthera mu utumiki, koma amatilimbikitsa kumtamanda “nthaŵi zonse.” (Aheb. 13:15, NW) Ngati mikhalidwe yathu yaumwini ilola, tiyenera kudziikira chonulirapo cha kuthera nthaŵi ina tikutamanda Yehova mlungu uliwonse. Awo amene akuchita kale zimenezo angakhoze kulinganiza zochita zawo kuti azitumikira monga apainiya othandiza nthaŵi ndi nthaŵi kapena ngakhale mosalekeza. Ena amene akhala akuchita upainiya wothandiza angalembetse kukhala apainiya okhazikika.
3 Mulimonse mmene mikhalidwe yathu ingakhalire, kodi kuli kotheka kwa ife kuwonjezera nsembe yathu ya chitamando? Changu chimasonkhezeredwa ndi chiyamikiro. Phunziro laumwini la Mawu a Mulungu limakulitsa chiyamikirocho. Misonkhano ya mpingo imatisonkhezera kusonyeza chiyamikirocho m’njira zogwira ntchito. Kuyanjana kwambiri ndi otamanda ena achangu ‘kungatifulumize ku ntchito zabwino.’ (Aheb. 10:24) Mwa kugwiritsira ntchito bwino lomwe makonzedwe opangidwa ndi mpingo, tingakhoze kuwonjezera nsembe yathu ya chitamando.
4 Mneneri wamkazi Anna anapereka chitsanzo chabwino mu utumiki wa Yehova. Ngakhale kuti anali ndi zaka 84, iye “sanachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu . . . usiku ndi usana.” (Luka 2:37) Kudziloŵetsa kwake m’ntchito za mpingo kwa mtima wonse kunamdzetsera chikhutiro chachikulu chaumwini. Cholembedwa cha Baibulo chonena za utumiki wake wokhulupirika chimatilimbikitsa lerolino.
5 Paulo analangiza kuti ‘amene ali olimba ayenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu.’ (Aroma 15:1) Mwinamwake mumpingo mwanu muli ena amene angapindule ndi thandizo lanu ndi chilimbikitso chanu chokoma mtima. Mwina chimene chingafunikire ndicho kuwapempha kutsagana nanu mu utumiki wakumunda basi. Wofalitsa wina angafunikire choyendera kapena wina wogwira naye ntchito. Kwa wina kulefuka ndiko kumene kungakhale vuto, ndipo mwina inu mungakhale munthuyo amene angapereke chichirikizo chomangirira chofunikira kudzutsanso changu chake mu utumiki wa Ufumu. (1 Ates. 5:14) Kufunitsitsa kwanu ‘kupatsa zosoŵa oyera mtima’ kumasonyeza chikhumbo chanu chaphamphu cha kuwonjezera chitamando ku dzina la Yehova.—Aroma 12:13.
6 Sitingathe kutchula zinthu zonse zimene Yehova watichitira kale ndi zimene adzatichitira. Palibe njira imene tingambwezere madalitso ameneŵa. Ha, pali zifukwa zamphamvu chotani nanga kuti “zonse zakupuma zilemekeze Yehova”!—Sal. 150:6.