Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/95 tsamba 1-2
  • Tamandani Yehova Nthaŵi Zonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tamandani Yehova Nthaŵi Zonse
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Ananu, Tamandani Yehova!
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Funafunani Ufumu wa Mulungu Choyamba—Mwa Kupereka Nsembe za Chitamando Nthaŵi Zonse
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Lemekezani Yehova Tsiku Lililonse
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Tamandani Yehova Tsiku ndi Tsiku
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 10/95 tsamba 1-2

Tamandani Yehova Nthaŵi Zonse

1 Pali zochita zingapo zofunika kwambiri kwakuti nthaŵi zonse zimafuna chisamaliro chathu. Pakati pa zimenezo timaphatikizapo kudya, kupuma, ndi kugona. Zimenezi nzofunika ngati tifuna kudzisamalira mwakuthupi. Mtumwi Paulo anaika kulalikira uthenga wabwino m’gulu limodzimodzi pamene analimbikitsa kuti: “Tipereke chiperekere [“nthaŵi zonse,”NW] nsembe yakuyamika Mulungu.” (Aheb. 13:15) Motero, kutamanda Yehova kumafunanso chisamaliro chathu cha nthaŵi zonse. Kumatamanda Atate wathu wakumwamba nthaŵi zonse ndiko chinthu chimene tiyenera kuyesa kuchita tsiku lililonse.

2 Pamene ena anayesa kupambutsira maganizo ake kwinakwake, Yesu anayankha nati: “Kundiyenera ine ndilalikire uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.” (Luka 4:43) Zilizonse zimene anachita tsiku lililonse mkati mwa zaka zitatu ndi theka za utumiki wake zinali m’njira ina zolemekeza Mulungu mwachindunji. Tikudziŵa kuti Paulo analingalira chimodzimodzi, monga mwa lingaliro limene anamveketsa pa 1 Akorinto 9:16 kuti: “Tsoka ine ngati sindilalikira uthenga wabwino.” Akristu enanso okhulupirika analimbikitsidwa kukhala okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira cha chiyembekezo chawo kwa ena. (1 Pet. 3:15) Zikwi mazana za apainiya achangu ndi mamiliyoni a ofalitsa a mpingo lerolino akuyesayesa kutsanzira zitsanzo zabwino zimenezi.

3 Pamene tisinkhasinkha za changu chochokera mu mtima chosonyezedwa ndi Yesu Kristu, Chitsanzo chathu, timalimbikitsidwa kulondola mapazi ake mosamalitsa. (1 Pet. 2:21) Tingafooke nthaŵi zina pamene tiyang’anizana ndi mavuto a umoyo wa tsiku ndi tsiku. Kodi ndimotani mmene tingagwiritsirire ntchito mipata ya tsiku ndi tsiku ya kutamanda Yehova pamene tikugwira ntchito yolembedwa ya nthaŵi zonse? Sitinganyalanyazenso mathayo a pa banja amene amafuna nthaŵi yathu yochuluka. Achichepere ambiri ngotanganitsidwa ndi maphunziro ofunika a tsiku ndi tsiku. Ena angalingalire kuti sikotheka kutamanda Yehova poyera tsiku lililonse. Nthaŵi zina, ena angathe mwezi wonse osagaŵana ndi ena uthenga wabwinowu m’njira ina iliyonse.

4 Yeremiya ndi munthu amene sanaleke kulalikira. Pamene kwakanthaŵi analephera kulankhula m’dzina la Yehova, anamva moto wosapiririka ukutentha mkati mwake. (Yer. 20:9) Mosasamala kanthu za mavuto omwe anaoneka ngati othetsa mphamvu, Yeremiya nthaŵi zonse anapeza njira yolankhuliramo uthenga wa Yehova kwa ena. Kodi tingatsanzire chitsanzo chake cha kulimba mtima ndi kulimbikira kufunafuna mipata yotamandiramo Mlengi wathu tsiku lililonse?

5 Kulankhula kwathu za Yehova sikuyenera kukhala chabe kwa panthaŵi zolinganizidwiratu zolalikira ndi ofalitsa ena mu gawo la mpingo. Timangofuna munthu womvetsera. Timakumana ndi anthu mosalekeza tsiku lililonse—amabwera kunyumba kwathu, timagwira nawo ntchito kuntchito, timaima nawo pamzere kusitolo, kapena timakwera nawo basi. Zimene zimangofunika ndizo moni waubwenzi ndi funso kapena ndemanga yosonkhezera maganizo imene idzayambitsa makambitsirano. Ambiri apeza ulaliki wa mtundu umenewu kukhala wobala zipatso koposa. Pamene tili ndi mipata yambiri yolankhula kwa ena za uthenga wabwino, sikungakhale kwa nzeru kwa ife kutha mwezi wonse popanda kuchita umboni wa Ufumu.

6 Mwaŵi wotamanda Yehova sudzatha kunthaŵi yonse. Monga mmene wamasalmo anasonyezera, chopuma chilichonse chiyenera kumatamanda Yehova, ndipo mosakayikira tikufuna kuphatikizidwapo. (Sal. 150:6) Ngati mtima wathu utisonkhezera kuchita zimenezo nthaŵi zonse, tidzagwiritsira ntchito mipatayo tsiku ndi tsiku kulankhula za Yehova ndi Mawu ake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena