Nyimbo 77
“Yehova ndi Mbusa Wanga”
(Salmo 23)
1. Yehova ndi Mbusa wanga;
Kodi ndingawopenji?
Pakuti wosamala nkhosa
Sadzaiŵala zake.
Anditengera kumadzi,
Moyo wanga upuma.
Atsogoza mapazi anga
M’njira za chilungamo.
Atsogoza mapazi anga
M’njira za chilungamo.
2. Nkana munthunzi wa imfa
Ndiyenda wosawopa,
Mbusa wanga ali pafupi;
Kumanditonthozabe.
Amandidzoza mafuta;
Wadzaza chikho changa.
Ukoma wake unditsate,
Ndikhale m’nyumba yake.
Ukoma wake unditsate,
Ndikhale m’nyumba yake.
3. Wachikonditu mbusayo!
Ndimtamanda moimba.
Mbiri yake yosangalatsa
Kwa nkhosa ndidzanena.
Mawu ake ndidzatsata,
Poyenda m’njira yake.
Chuma changa chomtumikira
Ndigwiritsira ntchito.
Chuma changa chomtumikira
Ndigwiritsira ntchito.