Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 10/1 tsamba 25-28
  • Samalirani Changu Chanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Samalirani Changu Chanu
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nyengo Zapadera za Changu
  • Changu m’Nthaŵi Zachikristu
  • Kodi Changu Chimenecho Chinali Cholakwika?
  • Chilimbikitso Chowonjezeka cha Changu
  • Zotulukapo Zabwino za Changu
  • Khalanibe Odzipereka
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kodi Tingatani Kuti Tiziona Kuti Ntchito Yolalikira Ndi Yofunika Kwambiri?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • “Tsiku la Yehova Lili Pafupi”
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Khalani Odzipereka pa Kulambira Koona
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 10/1 tsamba 25-28

Samalirani Changu Chanu

KODI ndi njira imodzi iti yotsimikizirika, imene ili yovomerezedwa ndi Mulungu yopitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wonse? Ndiyo kukhala ndi changu chenicheni pansi pa mtima wathu. Kutumikira Mulungu ndi mtima wonse kumatanthauza kumtumikira tili amphumphu, ndipo zimenezi zimafuna kumvera kwakhama ndi kosasunthika pa zonse zimene akutipempha kuchita.

Mneneri Mose anagogomezera chofunika chimenechi pamene analangiza mtundu wa Israyeli kuti: “Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.” (Deuteronomo 6:5) Zaka mazana ambiri pambuyo pake lamulo limodzimodzilo linabwerezedwa ndi Kristu Yesu kuti: “Uzikonda [Yehova, NW] Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.” (Mateyu 22:37) Mtumwi Paulo anakhudza chofunika chimodzimodzichi pamene anauza Aefeso kuchita “chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima,” ndi pamene analimbikitsa Akolose kuti: “Chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa [Yehova, NW], osati kwa anthu ayi.”​—Aefeso 6:6; Akolose 3:23.

Komabe, nkovuta kuika mtima wathu pa utumiki wa Mulungu ngati tilibe changu chachikulu mwa ife kapena ngati changu chimene tinali nacho chakhala chofooka tsopano​—kapenanso kutayika chonse. Lerolino, tikukhala mu nthaŵi yofuna changu chosalingana ndi cha m’nyengo ina iliyonse ya mbiri ya munthu.

Nyengo Zapadera za Changu

Chikristu chisanakhaleko panali nyengo zofunikira changu. M’tsiku la Nowa ndi m’nyengo imene inafika ku chiwonongeko cha Sodomu ndi Gomora zinalidi nthaŵi zofunikira changu chenicheni. (2 Petro 2:5, 6; Yuda 7) Zaka zimene zinaliko Chigumula chisanadze mosakayikira zinali zodzala ndi ntchito ya changu. Ngakhale kuti Nowa ndi banja lake sanadziŵe bwino pamene Chigumula chidzayamba, ‘mantha awo aumulungu’ anawachititsa kusazengereza.​—Ahebri 11:7, NW.

Mofananamo, Sodomu ndi Gomora asanawonongedwe, angelo “anafulumiza Loti” ndi kumuuza kuti: “Tapulumuka ndi moyo wako.” (Genesis 19:15, 17) Inde, panthaŵi imeneyonso, changu chinapulumutsa anthu olungama. Zaka mazana ambiri pambuyo pake, akapolo Achiyuda ku Babulo anauzidwa kuti: “Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babulo; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake.” (Yesaya 52:11) Mu 537 B.C.E., pafupifupi andende 200,000 anafulumira kutuluka m’Babulo momvera lamulo lofuna changu la ulosi limenelo.

M’mikhalidwe yonseyo changu chinachititsa awo amene anaona ndi kukhutira kuti anali kukhala panthaŵi zofuna changu kuchita utumiki ndi mtima wonse.

Changu m’Nthaŵi Zachikristu

Malemba onse Achigiriki Achikristu amatchula kufunikanso kwa changu mobwerezabwereza. “Yang’anirani,” “dikirani,” “[khalani maso, NW],” “khalani inunso okonzekeratu”​—onsewa ndi mawu amene Kristu Yesu anagwiritsira ntchito kusonkhezera changu choyenera mwa otsatira ake. (Mateyu 24:42-44; Marko 13:32-37) Ndiponso, mafanizo ake onena za anamwali khumi, kapolo woipa, matalente, ndi kulekanitsidwa kwa nkhosa ndi mbuzi zonsezo zimasonkhezera chiyembekezo ndi kuyambitsa changu.​—Mateyu 25:1, 14, 15, 32, 33.

Yesu sanangolankhula za changu komanso anachirikiza choonadi cha mawu ake mwa kugwira ntchito ndi changu. Panthaŵi ina anauza makamu pamene anayesa kumchititsa kukhalabe nawo kuti: “Kundiyenera ine ndilalikire uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu ku midzi inanso: chifukwa ndinatumidwa kudzatero.” (Luka 4:42, 43) Ndiponso, analimbikitsa ophunzira ake kupempha Mbuye wa kututa kuti atumize antchito ambiri ku kututa Kwake chifukwa chakuti “zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka.” (Mateyu 9:37, 38) Mapempho otero kwa Mulungu amasonyezadi mzimu wa changu.

Kodi Changu Chimenecho Chinali Cholakwika?

Ena angadzutse funso lanzeru lakuti, Kodi nchifukwa ninji changu chinafunika nthaŵiyo ngati ‘chisautso chachikulu’ chonenedweratu chinali kudzachitika patapita zaka mazana ambiri?​—Mateyu 24:21.

Timakhulupirira kuti zimenezi sizinali machenjera a Yesu a kuchititsa otsatira ake kukhala otanganitsidwa m’ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa. Ayi chinali chikondi cha Kristu pa ophunzira ake, ndiponso kuzindikira bwino kwake za mmene Yehova amaonera nthaŵi, zimenezo zinali maziko a uphungu wake wonena za changu. Inde, Kristu Yesu anadziŵa kuti mzimu wachangu unafunika kuti chifuniro cha Yehova chichitike mogwirizana ndi chifuno cha Mulungu. Ndiponso, anadziŵa kuti ophunzira ake adzapindula iwo eni mwauzimu mwa kukhala ndi changu kufikira pamene adzabwera.

Yesu Kristu anali atasonyeza bwino lomwe kuti padzakhala ntchito yochitira umboni padziko lonse yofunikira kumalizidwa m’nthaŵi yochepa. (Mateyu 24:14; Marko 13:10) Mbali zake za kupita patsogolo za ntchito imeneyi zinavumbulidwa kokha pamene ntchito inafutukuka. Koma changu chinafunika kuti mbali iliyonse ichitidwe. Yesu anasonyeza za kupita patsogolo kwa ntchito imeneyi pamene anati: “Mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) Ndipo ndi mmene ntchito yafutukukira kufikira tsopano lino. Zimenezi zadabwitsa atumiki a Mulungu m’kupita kwa nthaŵi, akumafunikira kusintha kumvetsa kwawo zinthu nthaŵi zina.

Changu cha Chikristu chakwaniritsa chifuno cha Yehova. Chathandiza ophunzira a Kristu kuchita ntchito yawo mopita patsogolo mogwirizana ndi programu ya Yehova yosasintha. Motero lerolino, pamene tilingalira za zaka 2,000 zapitazo, timadziŵa bwino kwambiri za programu imeneyo ya Mulungu.

Changu cha Chikristu chinathandiza ophunzira kupereka umboni wokwanira mu Yerusalemu, Yudeya, Samariya ndi kwa Ayuda obalalika 36 C.E. asanafike pamene kuyanja Israyeli kunatha. (Danieli 9:27; Machitidwe 2:46, 47) Momwemonso, changu cha Chikristu chinathandiza mpingo woyambirira popereka chenjezo lomveka kwa Ayuda onse lakuti posachedwa dongosolo lawo lidzatha. (Luka 19:43, 44; Akolose 1:5, 6, 23) Ndipo pamene linatha mwadzidzidzi mu 70 C.E., changu chinathandiza mboni za Kristu za m’zaka za zana loyamba kulengeza chiyembekezo cha kumwamba kwa ambiri mpatuko usanafunge monga mdima wandiweyani. (2 Atesalonika 2:3; 2 Timoteo 4:2) Ndiyeno, m’zaka mazana zonse za Dark Ages, Akristu oŵerengeka onga tirigu anasunga chiyembekezo cha Ufumu chili chamoyo, monga momwe Kristu Yesu anali ataneneratu. (Mateyu 13:28-30) Potsirizira pake, panthaŵi yake yoikika, Yehova anautsa mpingo wamphamvu, wamakono, wosonkhezeredwa ndi uthenga wake wachiweruzo wofulumira kwa awo okhala mu mbadwo uno wotsiriza.​—Mateyu 24:34.

Monga Danieli wanthaŵi zakale, Mboni zamakono zokhulupirika za Mulungu sizingakayikire konse Yehova, ndi kumufunsa kuti: “Muchitanji?” (Danieli 4:35) Zili ndi chidaliro chakuti Yehova amadziŵa bwino kwambiri chimene chili chofunika kuti ntchito yake ichitidwe mogwirizana ndi programu yake. Chotero m’malo mwa kukayikira mmene Yehova amalinganizira zinthu, ali ndi chimwemwe chakuti Mulungu wawapatsa mwaŵi wa kugwira naye ntchito m’nthaŵi ino yosangalatsa.​—1 Akorinto 3:9.

Chilimbikitso Chowonjezeka cha Changu

Chifukwa china chochitira changu ndicho kusatha kwathu kudziŵa bwino za tsiku ndi ola la kuulika kwadzidzidzi kwa chisautso chachikulu. Kristu Yesu anatsimikiza kuti palibe aliyense pa dziko lapansi amene akudziŵa tsiku loikikalo ndi ola la kuyambika kwa chochitika chachikulu chimenecho. (Mateyu 24:36) Nthaŵi ina iye anauza ophunzira ake achidwiwo kuti: “Sikuli kwa inu kudziŵa nthaŵi kapena nyengo, zimene Atate anaziika mu ulamuliro wake wa iye yekha.” (Machitidwe 1:7) Inde, zotsatirapo zake tikuzidziŵa, komano ife sitingathe kudziŵa zonse zoloŵetsedwamo.

Mtumwi Paulo anali ndi mkhalidwe wabwino pa changu. Mwina anali kukumbukira mawu a Yesu pamene analembera Atesalonika za kukhalapo kwa Kristu kuti: “Koma za nthaŵizo ndi nyengozo, abale, sikufunika kuti tidzakulemberani.” (1 Atesalonika 5:1) Analemba kalatayi patapita zaka 17 Yesu atanena kuti: “Mudzakhala mboni zanga . . . kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) Panthaŵiyo sakanatha kulemba zina chifukwa panalibenso zina zimene zinavumbulidwa. Komabe iwo anali ndi chidaliro chakuti tsiku la Yehova lidzafikadi “monga mbala usiku” pamene Akristu adzakhalabe akulalikira mwachangu.​—1 Atesalonika 5:2.

Kukuoneka kukhala kosatheka kuti pokumbukira mawu ameneŵa, Akristu a m’zaka za zana loyamba analingalira kuti tsiku la Yehova linali kutali kwambiri. Zoonadi, anadziŵa za mafanizo a Yesu onena za mfumu imene inapita kudziko lakutali ndi munthu amene anayenda ulendo. Anadziŵanso kuti mafanizowo anasonyeza kuti mfumuyo idzabwera “potsirizira pake” ndipo waulendoyo adzabwera “itapita nthaŵi yaikulu.” Koma mosakayikira iwo anasinkhasinkha mafunso onga akuti, Kodi “potsirizira pake” pamenepo ndi liti? Ndipo kodi tanthauzo lakuti “itapita nthaŵi yaikulu” nlotani? Ndizo zaka khumi kodi? Zaka makumi aŵiri? Zaka makumi asanu? Kapena nyengo yaitali? (Luka 19:12, 15, NW; Mateyu 25:14, 19) Iwo anakumbukirabe mawu a Yesu akuti: “Khalani okonzeka inunso; chifukwa nthaŵi imene simulingirira, Mwana wa munthu akudza.”​—Luka 12:40.

Zotulukapo Zabwino za Changu

Inde, changu chosonkhezeredwa ndi Mulungu chinawalimbikitsa kwambiri Akristu a m’zaka za zana loyamba, chikumawathandiza kukhala otanganitsidwa ndi ntchito yofunika kwambiri ya kulalikira ndi kuphunzitsa. Chikupitiriza kutilimbikitsa lerolino m’njira zambiri. Chimatitetezera pa kuganiza kuti zonse zili bwino kapena pa ‘kulema pakuchita zabwino.’ (Agalatiya 6:9) Chimatitetezera pa kuyanjana kwambiri ndi dziko ndi pa mzimu wake wonyenga wokonda chuma. Chimachititsa maganizo athu kusumikidwa pa “moyo weniweniwo.” (1 Timoteo 6:19) Ambuye Yesu anati ophunzira ake adzakhala ngati “nkhosa pakati pa afisi,” ndipo anadziŵa za kufunikira kwathu mtima wotsimikiza kotero kuti tilimbane ndi dziko. Inde, tatetezeredwa, tachinjirizidwa ndi changu chathu cha Chikristu.​—Mateyu 10:16.

Yehova Mulungu mu nzeru yake yosatha nthaŵi zonse wapatsa atumiki ake chidziŵitso chokwanira kuti asunge changu chawo chamoyo. Watitsimikizira mokoma mtima kuti tili mu “masiku otsiriza” a dongosolo lino loipa la zinthu. (2 Timoteo 3:1) Nthaŵi zonse timakumbutsidwa kuti tiyenera kuŵala monga mauniko kufikira pamene mbadwo umene tikukhalamo upita pa chisautso chachikulu, ndi pachimake chake pa Armagedo.​—Afilipi 2:15; Chivumbulutso 7:14; 16:14, 16.

Inde, changu chaumulungu ndicho mbali yofunika kwambiri ya utumiki wa mtima wonse kwa Yehova. Chimaletsa ndipo chimathandiza kuthetsa zoyesayesa za Mdyerekezi za kuchititsa atumiki a Mulungu ‘kulema ndi kukomoka m’moyo [wawo]’ (Ahebri 12:3) Kunthaŵi zomka muyaya, kudzipereka ndi mtima wonse kudzachititsa atumiki a Yehova kumumvera, koma tsopano, m’masiku ano omka ku Armagedo, changu chachikulu chenicheni chili mbali yofunika pa kudzipereka kwa mtima wonse.

Yehova, Mulungu wathu athandizetu tonsefe kusamalira changu chathu pamene tikupitiriza kubwereza mawu a mtumwi Yohane akuti: “Amen; idzani, Ambuye Yesu.”​—Chivumbulutso 22:20.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena