Nyimbo 53
Kuwonjezeka kwa Teokrase
1. Tama Teokrase wowonjezeka!
Kukula kwake kukuchitika.
Chitamando cha Yehova nchosatha
Kwa oyenda m’kuunika kwake.
Panali chiyambi chochepa pomwe
Mombolo anayenda padziko.
Tsopano “Otsalira” ndi khamulo
Atamanda Mfumu ya Mulungu.
2. Kristu pachimpando alamulira;
Anthu aima pamaso pake.
Adzakweza Ufumu wa Mulungu,
Powonongatu adani ake.
Phungu Wodabwitsa ndi Wautate,
Wamphamvu, Kalonga waMtendere.
Yehova adzabweretsa mtendere
Ufumu wake nuwonjezeka.
3. Amwaŵi ife pokhala ndi moyo!
Mukondwe nacho chiwonjezeko.
Khalanibe ndi chimwemwe m’kupatsa,
Khalani ndi phande muumboni.
Chenjezani onyoza dzina la Ya;
Kuti Armagedo yayandika.
Mwachangu ubukitseni Ufumu
Kwa ofatsa ndi ousa moyo.