Nyimbo 14
‘Kondwerani, Anthu Inu’!
1. Kondwerani, ndi anthu ake!
Ufumu wayamba.
Kristu wakhala mu Ziyoni;
Kondwerani konse!
Nthaŵi za akunjazo zatha;
Tsiku lawo latha.
Kondwerani, ndi anthu ake!
Mfumu ilamula.
2. Kondwerani, ndi anthu ake!
Dongosolo litha
Nkhondo ya’magedo iridi
Pafupi kwambiri.
Anthu potamanda chonyansa
Pokana Kalonga,
Ife titama Kalongayo;
Adzawonjezeka.
3. Kondwerani, ndi anthu ake!
Nenani pakhomo
Mbiri yabwino ya Ufumu;
Lengezani ponse
Kristu alamula mwanzeru,
Ndiponso m’chikondi.
Kondwerani, ndi anthu ake!
Mtumikirenitu.