Nyimbo 72
Zisangalalo ndi Zipatso za Utumiki Waufumu
1. Muutumiki wa M’lungu wathu,
Mulidi chimwemwe choposa,
Pakuti tilalikira mbiri
Kuti ena atonthozedwe.
Yesu anatitsimikizira:
Kupatsa kudzetsa chimwemwe.
Ndipo kodi tingaperekenji
Koposa chowonadi cha kumoyo.
2. Ngakhale pomka khomo ndi khomo
Tipeza onyoza ndi mphwayi,
Tisunga chitsimikizo chathu
Ndi kugwiritsa umphumphuwo.
Ngati tikumana ndi chizunzo
Pochiriki za dzina la Ya,
Yesu anatitu tikondwere,
Aneneriwo anavutikanso.
3. Utumikiwo ngwosangalatsa
Potsatira njira ya Mbuye;
Lalika za tsiku la Yehova
Ndi kulemekeza Yehova!
Tiwadzetsera chiyembekezo
Cha dziko lopanda uchimo.
Izi zitipatsa chikhutiro,
Chiyembekezo cha moyo wosatha.