Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/96 tsamba 4
  • Thandizani Mwachikondi Awo Amene Amasonyeza Chikondwerero

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Thandizani Mwachikondi Awo Amene Amasonyeza Chikondwerero
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 2/96 tsamba 4

Thandizani Mwachikondi Awo Amene Amasonyeza Chikondwerero

1 Kumanga nyumba kumafuna kukonzekera mosamala ndi kuyesayesa kwakukulu. Pulani ya nyumba itapangidwa, malo odzamangapo ayenera kukonzedwa ndipo maziko olimba ayenera kuyalidwa. Ntchitoyo imapita patsogolo mpaka pomalizira pake imatha. Mofananamo, tiyenera kuthandiza anthu onga nkhosa kuphunzira choonadi mopita patsogolo. Timayesayesa kudzutsa chikondwerero paulendo woyamba. Ndiyeno, timapanga maulendo obwereza, tikumayala maziko mwa kuphunzitsa choonadi choyambirira cha Mulungu ndi chifuno chake pa anthu.—Luka 6:48.

2 Komabe, maziko asanayalidwe, tiyenera kukonza malo odzamangapo, titero kunena kwake, tikumalingalira za mikhalidwe ya mwini nyumba. Kodi ndi nkhani iti imene tinakambitsirana poyamba? Kodi ndi malemba ati amene tinagwiritsira ntchito? Kodi mwini nyumba anati bwanji? Kodi ndi buku liti limene tinasiya? Pamene mubwererako, khalani ndi mfundo zenizeni m’maganizo, ndipo mangani mazikowo mopita patsogolo. Paulendo uliwonse chidziŵitso cha mwini nyumba ndi chikhulupiriro chake mwa Mulungu zimakula.

3 Ngati paulendo wanu woyamba munakambitsirana za kufunika kwa kumvetsera kwa Mlengi wa ukwati, pitirizani makambitsirano anuwo, mukumagwiritsira ntchito njira imene ili patsamba 66 la buku la “Kukambitsirana” ndi kunena kuti:

◼ “Ena amalingalira kuti uphungu wa Baibulo sungagwire ntchito m’dziko lathu lamakono. Kodi inu mukulingalira bwanji pa zimenezo? [Yembekezerani yankho.] Kodi simungavomereze kuti buku limene limapereka uphungu umene ungatichitse kukhala ndi moyo wabwino wa banja ndi lothandiza? [Yembekezerani yankho.] Malingaliro ndi machitidwe pa moyo wa banja zasintha, ndipo zotulukapo zake zimene tikuona lerolino si zabwino. Koma mabanja amene amagwiritsira ntchito zimene Baibulo limanena kaŵirikaŵiri ngokhazikika ndi achimwemwe.” Ŵerengani Akolose 3:18-21. Mungaŵerengenso ziganizo ziŵiri zomaliza za m’ndime 9, patsamba 185 la buku la Moyo wa Banja. Fotokozani kuti tili ndi programu ya phunziro la Baibulo laulere.

4 “Adzamva bwanji wopanda wolalikira?” (Aroma. 10:14) Zoonadi, adzadziŵa bwanji tanthauzo la choonadi ngati sitipanga maulendo obwereza ogwira mtima? Mwini nyumba aliyense amene tinalankhula naye ponena za uthenga wa Ufumu afunikira ulendo wobwereza. Mwezi uno tidzafunikira kubwerera kumakambitsirano athu oyamba ndi malingaliro ena a m’Malemba ochokera mu buku la Moyo wa Banja, kapena chofalitsa china chilichonse chimene tinagaŵira, ndipo zimenezo zingachititse kuyamba phunziro la Baibulo mwachipambano.

5 Pamene mupanga ulendo wobwereza pambuyo pa kugaŵira buku la “Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe” mungayambe mwa kusonyeza chithunzithunzi patsamba 189 ndi kufunsa funso kuti:

◼ “Kodi mukulingalira kuti kukhala m’dziko langwiro kudzakhala kotani? [Mvetserani ndemanga za mwini nyumba.] Zimene mukuona pachithunzithunzichi si malingaliro ongopeka; nzozikidwa pa malonjezo odalirika otchulidwa m’Baibulo. [Ŵerengani Chivumbulutso 21:4 ndi Salmo 37:11, 29.] Ndingakonde kulongosola mmene inuyo ndi banja lanu mungapezere dalitso limeneli. Tingayambe mwa kukambitsirana ‘mutu umene uli wabwino kwambiri kwa inu ndi banja lanu.’” Ngati mwini nyumba asonyeza chikondwerero, pitirizani ndi makambitsiranowo, ndiyeno pemphani kuchita naye phunziro la Baibulo.

6 Pamene tipeza anthu oona mtima amene akufunafuna choonadi, timasonyeza chikondi chathu chenicheni mwa kubwererako kukawathandiza kugwiritsira ntchito zimene amva. Timagwiritsira ntchito choonadi chofunika kwambiri chimene tapatsidwa kuti chipereke madalitso osatha kwa ife eni ndi a awo amene amamva.—1 Tim. 4:16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena