Yamikani Yehova “Masiku Onse”
1 Salmo 145:2 lili ndi lonjezo limene Mfumu Davide ananena kwa Yehova: “Masiku onse ndidzakuyamikani; ndi kulemekeza dzina lanu ku nthaŵi za nthaŵi.” Nafenso tili ndi chifukwa choyamikirira ndi kutamandira Atate wathu wakumwamba! Koma kodi tingatsanzire motani chitsanzo cha Davide pokuza ulamuliro wa Yehova “masiku onse”?
2 Kudzaza Mtima Wathu ndi Kuyamikira Yehova: Phunziro la nthaŵi zonse la Mawu a Mulungu limazamitsa chithokozo chathu pa zimene Yehova watichitira, akutichitira, ndi zimene adzatichitira. Pamene tikulitsa chiyamikiro cha zochita zake zodabwitsa, timasimba zambiri pa ubwino wake. (Sal. 145:7) Tidzatamanda Yehova mwaphamphu panthaŵi iliyonse yoyenera.
3 Tamandani Yehova m’Makambitsirano Atsiku ndi Tsiku: Pokambitsirana ndi anansi, anzathu akusukulu, anzathu akuntchito, ndi ena amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku, tingapeze mipata ya kuwauza za chiyembekezo chathu. Mwina mnansi wathu angasonyeze nkhaŵa ponena za upandu umene uli m’chitaganya; mnzathu wakusukulu angade nkhaŵa ndi anamgoneka kapena makhalidwe ena oipa; mnzathu wakuntchito angafotokoze malingaliro ake onena za nkhani ina yandale. Tingasonyeze mapulinsipulo ndi malonjezo a m’Mawu a Mulungu amene amasonyeza njira yoyenera kutenga tsopano ndi chothetsera mavuto ameneŵa chenicheni. Mawu otero onenedwa “panthaŵi yake” angakhale dalitso!—Miy. 15:23.
4 Lankhulani za Yehova Nthaŵi Yonse: Munthu woyamikira kwambiri Yehova amafuna kuuza ena ambiri omwe angathe za uthenga wabwino. (Sal. 40:8-10) Pamenepa tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikuchita zonse zimene mikhalidwe yanga ikundilola kuchita?’ Ambiri apeza kuti atapanga kusintha kwina koyenera, akhoza kukhala apainiya okhazikika. Ngati mikhalidwe imene ilipo siloleza zimenezo, kodi tingalembetse monga apainiya othandiza? Popeza kuti nyengo imene ikudzayo ya Chikumbutso ili nthaŵi ya ntchito yowonjezereka, miyezi ya March ndi April ingakhale nthaŵi yabwino ya kuwonjezera utumiki wathu mwa kuchita upainiya wothandiza.
5 Thandizani Atsopano Kuti Agwirizane Nafe m’Kuyamika Yehova: Chochitika cha Chikumbutso cha imfa ya Yesu chimatikumbutsa nthaŵi zonse zifukwa zothokozera Yehova ndi kutamanda dzina Lake. Imeneyi ili makamaka nthaŵi yabwino yolimbikitsa ophunzira Baibulo athu kugwirizana nafe kulankhula poyera za uchifumu wa Yehova. Alimbikitseni kusinkhasinkha mwapemphero pa zimene zafotokozedwa m’ndime 7-9 pamasamba 173-5 a buku la Knowledge That Leads to Everlasting Life. Ngati ali oyenerera, palibe chifukwa chowaletsa ngakhale kuti sadziŵa zambiri. Ofalitsa okhoza bwino alipo kuwasonyeza mmene ntchito yolalikira Ufumu amaichitira. Ngati atsopano angapeze kulimbika mtima kulankhula uthenga wabwino, adzakhala ndi chidaliro chakuti Yehova adzawathandiza.—Mac. 4:31; 1 Ates. 2:2.
6 Timadzipatsa mapindu osatha ife enife ndiponso kwa ena pamene tiyesayesa kuyamika Yehova masiku onse.