Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/06 tsamba 3-4
  • Uzani Ena za “Kuunika kwa Dziko Lapansi”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Uzani Ena za “Kuunika kwa Dziko Lapansi”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Nkhani Yofanana
  • Lengezani Ulemerero wa Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Apainiya Othandiza 3,000 Akufunika
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • ‘Lalikirani Mokwanira Mawu a Mulungu’
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Kodi Mungachite Upainiya Wothandiza?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 2/06 tsamba 3-4

Uzani Ena za “Kuunika kwa Dziko Lapansi”

1. Kodi n’kuwala kwakukulu kotani kumene Mawu a Mulungu analosera, ndipo ndi mwambo wotani umene mwapadera umatilimbikitsa kuuza ena za kuwala kumeneku?

1 Kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova analosera kuti: “Anthu amene anayenda mumdima, aona kuwala kwakukulu; iwo amene anakhala m’dziko la mthunzi wa imfa, kuwala kwatulukira kwa iwo.” (Yes. 9:2) “Kuwala kwakukulu” kumeneko kunaoneka m’zochita za Mwana weniweniyo wa Mulungu, Yesu Kristu. Ntchito yolalikira imene anachita ali padziko lapansi limodzi ndi madalitso amene anabwera chifukwa chopereka moyo wake, zinaombola anthu kuchoka mu mdima wauzimu. Kuwala kotere n’kumene anthu akufuna m’nthawi zamdima zino. Mgonero wa Ambuye umatipatsa mwayi wapadera wouza ena za “kuunika kwa dziko lapansi.” (Yoh. 8:12) Chaka chatha anthu mamiliyoni ambiri anasonyeza chikhulupiriro pogwirizana nafe kumvera lamulo la Yesu lakuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.” (Luka 22:19) Pamene Chikumbutso cha chaka chino chikuyandikira, kodi tingatani kuti titenge nawo mbali youza ena za kuwala kumene Yehova wakhazikitsa?—Afil. 2:15.

2. Kodi tingakulitse motani mtima woyamikira nsembe ya dipo, ndipo kuchita zimenezi kungakhale ndi zotsatirapo zotani?

2 Kulitsani Mtima Woyamikira: Nyengo ya Chikumbutso ndi nthawi yabwino kwambiri yosinkhasinkha za chikondi chachikulu chimene Yehova ndi Yesu anasonyeza popereka nsembe ya dipo kaamba ka anthu onse. (Yoh. 3:16; 2 Akor. 5:14, 15) N’zosakayikitsa kuti kusinkhasinkha pa zinthu zimenezi kudzakulitsa mtima wathu woyamikira mwambo wopatulika umenewu. Anthu onse a Mulungu akufunikira kupeza nthawi yowerenga ndi kusinkhasinkha malemba okhudza Chikumbutso, amene asonyezedwa mu Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku. Kuganizira za makhalidwe osayerekezereka a Yehova amene anawasonyeza bwino kwambiri pa kupereka dipo, kumatithandiza kukhala onyadira kwambiri podziwa kuti iye ndiye Mulungu wathu. Ngati tonsefe payekhapayekha tiganizira ubwino wa dipo, kukonda kwathu Mulungu ndi Mwana wake kochokera m’mtima kumakula ndipo kumatilimbikitsa kuti tichite zambiri pokwaniritsa chifuniro chake.—Agal. 2:20.

3. Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira kwathu Chikumbutso?

3 Ngati titakulitsa kuyamikira kwathu njira imene Yehova wakonza kuti apulumutsire anthu, ophunzira Baibulo athu, anthu amene timawapitira pa ulendo wobwereza, abale athu, anzathu akusukulu, anthu ogwira nawo ntchito, ndi anthu enanso amene tingawaitanire ku mwambo wapadera umenewu, adzaona kuti timakonda Chikumbutso. (Luka 6:45) Choncho, yesetsani mwapadera kuwaitana anthu onsewa, ndipo apatseni kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso kuti kadziwakumbutsa. Pofuna kuti musaiwale wina aliyense, mungachite monga mmene ambiri amachitira, kusunga mayina a anthu amene amawaitana nthawi zonse ku Chikumbutso n’kumangowonjezerapo ena chaka ndi chaka. Mwa kukhala ndi dongosolo limeneli ndi kuyesetsa kuitanira anthu achidwi ku Chikumbutso, tingasonyeze bwino kwambiri kuti tikuyamikira Yehova Mulungu “chifukwa cha mphatso yakeyake yosatheka kuneneka.”—2 Akor. 9:15.

4. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kukhala mu utumiki nthawi yochulukirapo m’miyezi ya March ndi April?

4 Onjezerani Nthawi Yanu Yokhala mu Utumiki: Kodi kungatheke kuwonjezera nthawi yanu ya mu utumiki m’mwezi wa March ndi April? Kuyesetsa kuuza ena “Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Kristu” sikungalephere kutibweretsera madalitso a Mulungu. Yehova, monga gwero la kuunika kwauzimu walamula kuti: “Kuunika kudzawala kutuluka mumdima.” (2 Akor. 4:4-6) Ngati kungakhale kothandiza, akulu angakonzenso masiku ena ndi nthawi kuti azipita mu utumiki wa kumunda, kutsogolera ndi kuchirikiza ofalitsa amene akufuna kukhala ndi nthawi yochulukirapo mu utumiki. Zimenezi zingaphatikizepo kulalikira m’mamawa m’misewu kapena kukonza zolalikira malo azamalonda ndi m’maofesi ndiponso kulalikira patelefoni masana kapena chakumadzulo. Kuti mukhale ndi nthawi yochuluka mu utumiki, ziikireni maola amene mukufuna kukwaniritsa, ndipo yesetsani kuti muwakwanitse. Ambiri amaona kuti njira yabwino yom’patsira Yehova zochuluka ndiyo kuchita nawo upainiya wothandiza.—Akol. 3:23, 24.

5. Kodi ambiri akupindula motani ndi kuchepetsedwa kwa maola a upainiya wothandiza?

5 Kodi Mungachite Upainiya Wothandiza? Tsopano patha zaka seveni kuchokera pamene maola a apainiya othandiza anachepetsedwa. Kusintha kumeneku kwathandiza abale ndi alongo enanso ambiri kupeza nawo madalitso ochita utumiki wa upainiya wothandiza. Kodi mwayeserapo kuchita upainiya? Ambiri ali ndi chizolowezi chabwino chimenechi chomachita upainiya chaka ndi chaka. M’mipingo yambiri ofalitsa angapo amatenga upainiya nthawi yofanana kuti azichitira utumiki umenewu limodzi, ndipo imakhala ntchito yopindulitsa kwambiri ya mpingowo chaka chimenecho. Kodi nanunso mungakonze zoti musangalale ndi upainiya mwezi wina m’nyengo imeneyi ya Chikumbutso? Mwezi wa April ungakhale wabwino kwa ena makamaka chifukwa chakuti uli ndi milungu isanu yathunthu.

6. Kodi ndi makonzedwe abwino kwambiri otani amene alipo?

6 Kodi mpingo wanu udzakhala ndi woyang’anira dera m’kati mwa miyezi ya March ndi April? Ngati ndi choncho, ndiye kuti muli ndi mwayi wapadera. Monga mmene tinalengezera kale, onse amene adzakhale akuchita upainiya wothandiza pa nthawi imene woyang’anira dera adzayendera mpingo wawo m’chaka chautumiki cha 2006, adzaitanidwa kukakhala nawo pa chigawo choyamba cha msonkhano wa apainiya umene woyang’anira dera adzachititsa mlungu umene akuyendera mipingowo. Sitikukayikira konse kuti mfundo zolimbikitsa zauzimu zimene zidzakambidwa pa msonkhano umenewu zidzathandiza apainiya ambiri othandiza kuti akalimire upainiya wokhazikika. Ndiponso, m’mwezi wa March tidzakhala okondwa kuthandiza anthu kuti ayambe kuona kuwala kwauzimu pogwiritsa ntchito buku latsopano lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Bwanji osakhala ndi cholinga choyambitsa phunziro pogwiritsa ntchito buku latsopanoli?

7, 8. (a) Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kuti tipange ndandanda yochitira upainiya wothandiza? (b) Kodi kugwirizana pabanja n’kothandiza motani, ndipo banja lonse lingapindule bwanji?

7 Pamene mukuganizira za maola 50 amene apainiya othandiza amafunikira kukwanitsa, yesetsani kupanga ndandanda imene ingakuthandizeni kuwalitsa kuunika kwa choonadi kwa maola 12 pa mlungu uliwonse. Ndiponso, lankhulani ndi amene akhala akuchita bwino pa nkhaniyi, komanso lankhulani ndi anthu enanso. Zimenezi zingawalimbikitse kuti nawonso achite upainiya. Ofalitsa obatizidwa aang’ono ndi aakulu omwe, aona kuti mwa kukonzekera bwino, sizovuta kwenikweni kukwanitsa maola ofunikawo. Pemphererani nkhaniyi. Ndiyeno, ngati mungathe, konzekerani bwino ndipo sangalalani ndi upainiya wothandiza!—Mal. 3:10.

8 Mabanja ambiri aona kuti kuchita zinthu mogwirizana kungathandize kuti munthu mmodzi kapena angapo a pabanja pawo achite upainiya. Banja lina linagwirizana kuti anthu asanu a pabanjalo alembetse upainiya wothandiza. Pabanja limeneli ana ena awiri amene anali ofalitsa osabatizidwa anasonyeza khama lapadera kuti awonjezere nthawi yawo ya mu ulaliki. Kodi banjalo linapindula motani powonjezera khama lawolo? Iwo analemba kuti: “Unali mwezi wosangalatsa kwambiri, ndipo zimenezi zinathandizira kuti banja lathu likhale lolimba ndi logwirizana kwambiri. Tikuyamika Yehova chifukwa cha madalitso ake odabwitsa amenewa!”

9. Kodi tingatani kuti kuunika kwathu kuwale mu nyengo imeneyi ya Chikumbutso?

9 Kodi ntchito yathu yapadera ya miyezi ya March ndi April idzakhaladi yolimbikitsa, kutithandiza kuyandikana ndi Atate wathu wakumwamba? Tingapinduledi ngati aliyense payekha atachita khama kulimbikitsa chikondi chake pa Mulungu ndi Mwana wake ndiyeno n’kuwonjezera nthawi imene amakhala mu utumiki. Tiyeni tisonyeze mtima ngati wa wamasalmo, amene anayimba kuti: “Ndidzayamika Yehova kwakukulu pakamwa panga; ndi pakati pa anthu aunyinji ndidzam’lemekeza.” (Sal. 109:30) Yehova adzadalitsa utumiki wathu wakhama panyengo imeneyi ya Chikumbutso. Choncho tiyeni tiwalitse kuunika kwakukuluko kotero kuti anthu ambiri asayendenso mu mdima koma kuti ‘akhale nako kuunika kwa moyo.’—Yoh. 8:12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena