Nyimbo 6
Lengezani Mbiri Yabwino Yosatha
1. Kuzungulira dziko mngelo wa M’lungu,
Auluka mmwamba ndi mbiri yabwino.
Ati: ‘Opani Mfumu iri pampando.
Inde, lambirani Yehova yekhayo.
Tsono ora lachiweruzo lafika,
Posachedwa oipa adzachotsedwa.’
Alaliki a Ufumu asawope
Alankhule mwamphamvu mbiri ponsepo.
2. Mngelo wachiŵiri akulengezanji
Kuti, ife Mboni za Ya tigaŵane?
Anena za kugwa kwa Babulo mkulu,
Kuti posachedwa adzawonongedwa.
Potero Ya alamula tibukitse
Kulipsira ndi kukwezedwa kwa dzina.
Munda tilalikira ngwaukuludi;
Koma mngelo wa Mulungu atsogoza.
3. “Mwana wa munthu” pamodzi ndi angelo
Wayambatu kuweruza amitundu.
Dana nacho choipa. Konda chabwino.
Opa M’lungu ndi kusunga malamulo.
Thayo loikidwa kwa ife ndi ’mbuye
Ndiro kulalikira mbiri yabwino.
Chotero ife tilangiza molimba,
“Idzani kudzalambira Ya mokondwa.”