Nyimbo 130
Utumiki Wosangalatsa
1. Mokondwa titumikire Mfumuyo,
Podza nazo mphatso kuntchito yake.
Nkana utumikiwo ukachepa
Chikondi chathu chikuwonekera.
2. Ntchito ya Yehova iri kwa onse,
Antchito alikuitanidwabe.
Talandira ntchito yopatulika;
Madalitso adza mwa ntchito yathu.
3. Nkana anthu akane chowonadi,
Tidziŵa kuti “M’lungu sanganame.”
Motero tilalikire Mawuwo,
Chifukwa mwa iwo timadalira.
4. Pogaŵana mokondwa muntchitoyo
Timachitira umboni kwa onse,
Chifukwa M’lungu wathu atiyanja,
Watipanga kukhala atumiki.