Nyimbo 128
Chitani Zochuluka—Monga Anaziri
1. Anaziri—Tiwatsanzire?
Kodi tingateronso?
Opatulidwira Yehova
Munjira yapadera.
Pendani! Tikusamalire.
Nthaŵi ikutha mwamsanga.
Kodi tingawonjezere
Utumiki wathu?
2. Anaziri—Moyo wawotu
Unali wodzikana.
Unawadzetsa kwa Mulungu.
Kodi tingateronso?
Analola ziletso zina;
Za kulumbira kwawoko.
Abale athu ambiri
Achita motero.
3. Anaziri—Anasiyana
Anali apadera.
Anachitadi mogonjera;
Anamvera Mulungu.
Monga antchito a Mulungu
Tiri ndi chikhulupiro.
Mulungu atidalitse,
Tichitetu changu.
4. Anaziri—Ngachitsanzodi.
Anali osamala.
Tikhaletu osadetsedwa;
Ya anawadalitsa.
Daliranitu Yehovayo.
Asamala anthu ake.
Tichite zambiri ndithu
Tipeze chimwemwe.