Nyimbo 40
Kupanga Njira Yathu Kukhala Yachipambano
1. M’lungu anauza Yoswa:
‘Khalabe m’Lamulo.
Uŵerenge nthaŵi zonse,
Ulisamalire.
Likutsogozetu m’zonse,
Likhalebe mkamwa (ndithudi).
Udzapambana, cho’nadi
Chidzakutsogoza (zo’nadi).’
Udzapambana, cho’nadi
Chidzakutsogoza.
2. Mafumu mu Israyeli
Analamulidwa:
‘Adzilembere Lamulo
La Mulungu mwini,
Naŵerenge nthaŵi zonse
Nadzichepetsetu (indedi).’
Ya akamuwonjezera;
Masiku ambiri (ambiri).
Ya akamuwonjezera;
Masiku ambiri.
3. M’Baibulo timapeza
Zofuna za M’lungu.
Poti sitingadzipende,
Atithandizetu.
Tikamvera mawu ake
Tidzamdziŵa ndithu (o inde).
M’lungu akatiphunzitsa,
Tidzasunga mawu (akewo).
M’lungu akatiphunzitsa,
Tidzasunga mawu.