Khalani ndi Phande m’Ntchito Imene Sitidzaibwerezanso
1 Panthaŵi zosiyanasiyana m’mbiri yonse ya mtundu wa munthu, Yehova anayenera kupereka chiweruzo pa adani ake. Komabe, chifukwa cha chifundo chake, anapatsa oongoka mtima mpata wakupulumuka. (Sal. 103:13) Zotsatirapo zake zinadalira pa kulabadira kwawo zimenezo.
2 Mwachitsanzo, Chigumula chisanadze, mu 2370 B.C.E., Nowa anali “mlaliki wa chilungamo.” Amene anawonongeka ndi aja omwe ananyalanyaza chenjezo la Mulungu. (2 Pet. 2:5; Aheb. 11:7) Yerusalemu asanawonongeke mu 70 C.E., Yesu anafotokoza mwatsatanetsatane zimene aliyense anayenera kuchita kuti apulumuke chiwonongeko chimene chinali kudza pamzindawo. Onse omwe ananyalanyaza chenjezo lake tsoka linawagwera. (Luka 21:20-24) Machenjezo a Mulungu ndi ziweruzo zake zotero zinachitikanso nthaŵi zambiri m’mbiri yonse yakale.
3 Ntchito Yamakono Yochenjeza: Kalekale Yehova ananena kuti adzatsanulira mkwiyo wake padongosolo loipa lalero ndi kuti ofatsa okha ndiwo adzapulumuka. (Zef. 2:2, 3; 3:8) Nthaŵi yolalikira chenjezo limeneli ikutha msanga! ‘Chisautso chachikulu’ chili patsogolopa, ndipo ofatsa tsopano akusonkhanitsidwa. Inde, ‘m’minda mwayera kale kufikira kumweta.’ Chifukwa chake, kulibe ntchito yofunika ndi yofulumiza kwambiri kuposa imeneyi.—Mat. 24:14, 21, 22; Yoh. 4:35.
4 Tiyenera kukhala ndi phande pakupereka chenjezo lamakono kwa ena, “ngakhale akamva kapena akaleka kumva.” Imeneyi ndi ntchito yopatsidwa ndi Mulungu imene sitiyenera kuinyalanyaza ayi. (Ezek. 2:4, 5; 3:17, 18) Kukhalamo kwathu ndi phande lalikulu m’ntchitoyi kumapereka umboni wokhutiritsa wakuti timamkonda kwambiri Mulungu, timaderadi nkhaŵa anansi athu, ndi kuti tili ndi chikhulupiriro chosagwedera mwa Mpulumutsi wathu, Yesu Kristu.
5 Ino Ndiyo Nthaŵi Yochitapo Kanthu: Kale ziweruzo za Yehova zitaperekedwa, kuipa kunali kubukanso nthaŵi zonse chifukwa Satana ndi ziŵanda zake anali okangalikabe. Koma panthaŵi ino simmene zidzakhalira ayi. Chisonkhezero cha Satana chidzafafanizidwa. Sipadzafunikiranso kupereka chenjezo padziko lonse lonena za “chisautso chachikulu.” (Chiv. 7:4; Aroma 16:20) Tili ndi mwaŵi wapadera wokhala ndi mbali m’ntchito imene sitidzaibwerezanso. Ino ndiyo nthaŵi yogwiritsira ntchito kwambiri mwaŵi umenewu.
6 Mtumwi Paulo mwachidaliro anati ponena za ntchito yake yolalikira: “Ndilibe kanthu ndi mwazi wa anthu onse.” (Mac. 20:26) Sanadzimve waliwongo la mwazi chifukwa cholephera kupereka chenjezo mwanjira iliyonse. Chifukwa? Chifukwa anati za utumiki wake: “Kuchita ichi ndidzivutitsa ndi kuyesetsa.” (Akol. 1:29) Tiyeni nafenso tipeze chikhutiro chimodzimodzi mwa kukhala ndi phande lalikulu kwambiri m’ntchito imene sitidzaibwerezanso!—2 Tim. 2:15.