Tsitsimulani Achibale Anu ndi Madzi a Chowonadi
“MONGA madzi ozizira kwa munthu wotopa, momwemo mawu abwino akuchokera kudziko lakutali,” adatero Solomo. (Miyambo 25:25) Ndichokumana nacho chothutsa mtima chotani nanga kwa munthu wotopa kumvetsera kumbiri yanu yabwino ya moyo wosatha m’Paradaiso irinkudzayo! Mwanjirayi, pakamwa panu padzakhala “magwero a moyo.”—Miyambo 10:11; Yesaya 52:7.
Madzi amanyowetsa nthaka ndi kumeretsa, pamene liyambwe lingakhale langozi. Ndiponso, madzi mumpangidwe wa madzi ozizira amakhala otsitsimula, koma kodi ndani amene angafune kupezereredwa ndi mkuntho kapena mvula yamatalala? Popeza kuti zimene zimatuluka mkamwa mwathu zayerekezeredwa ndi madzi, chisamaliro chathithithi ku chiphunzitso chathu chiri choyenerera. (1 Timoteo 4:16) Tiyenera kukhaladi odera nkhaŵa za ziyambukiro zosiyana za “madzi” amenewa pamene tilalikira kwa achibale.
“Kuthirira” Achibale
M’nthaŵi zakale, Rahabi anatsegulira banja lake njira yopita kuchipulumutso, ndipo Korneliyo anachitira umboni kwa achibale ake. (Yoswa 2:13; 6:23; Machitidwe 10:24, 30-33) Andreya mbale wake wa Petro anamthandiza kukhala wophunzira wa Yesu. (Yohane 1:40-42) Ndipo lerolino Mboni za Yehova zambiri zimalola chowonadi cha Baibulo kulalikidwa kwa achibale awo. Miyambo 11:25 imalonjeza kuti: “Wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.”
Mkazi wina ku Ulaya anakhumba kugaŵana chipembedzo chake chatsopano ndi makolo ake, abale, ndi alongo okhala ku Filipino. Iye akusimba kuti: “Ndidatero m’kalata iriyonse imene ndinaŵalembera. Ubatizo wanga usanachitike, ndidaatumizanso mabukhu kwa iwo ndi kuwafunsa ngati adafuna kuchezeredwa ndi Mboni za Yehova.” Anachisangalala kwambiri, pamene iwo anavomera kuchezeredwako, ndipo tsopano asanu ndi atatu a iwo akulambira Yehova. Mboni zina zawona zotulukapo zabwino mwa kutumiza mphatso ya masabusikripisheni a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwa achibale awo.
Koma bwanji ngati ziwalo zabanja sizikusonyeza chikondwerero? Yesu anayang’anizana ndi mkhalidwe umenewu, popeza kuti panthaŵi ina “ngakhale abale ake sanakhulupirire iye.” Komabe, pambuyo pake, “ndi mtima umodzi” anachita khama m’pemphero, limodzi ndi atumwi. (Yohane 7:5; Machitidwe 1:14) Kodi nchifukwa ninji kusintha kwamtima? Mwachiwonekere Yesu anapereka chithandizo kwa achibale ake asanakwere kumwamba. Kodi ziri choncho motani? Iye adaŵathandiza kukhala ndi chikhulupiriro mwa kuwonekera kwa Yakobo mbale wake mwa bambo wina. (1 Akorinto 15:7) Chotero, musaleke kuyesa kuthandiza achibale anu. Mboni zambiri zakhala zokhoza kukambitsirana ndi achibale osakhulupirira ponena za chowonadi cha Baibulo pambuyo pa kuyembekezera moleza mtima nthaŵi yabwino.
Komabe, “kuthirira” achibale sikumatanthauza kuwakhathamiritsa ndi mawu. Aŵiri okwatirana a ku Yugoslavia akuti: “Nthaŵi zonse pamakhala ngozi ya kulalikira kwa iwo mopambanitsa.” Woyang’anira wina woyendayenda adaati: “Kaŵirikaŵiri abale amachita mopambanitsa, kusonyeza changu chonkitsa.” Ludwig akukumbukira nthaŵi pamene adayamba kuphunzira Baibulo naati: “Pamenepo ndinalalikira amayi kwa maora angapo ndi kumaliza kulongosola pafupifupi kanthu kalikonse kamene ndinaphunzira m’Baibulo, ndipo kaŵirikaŵiri zimenezi zinachititsa mikangano, makamaka kwa atate.”
Khalani “Chitsime cha Nzeru”
Timaŵerenga kuti “lirime lanzeru linena bwino zomwe adziwa; koma mkamwa mwa opusa mutsanulira utsilu,” ndipo “mtima wa olungama uganizira za mayankhidwe.” (Miyambo 15:2, 28) Chotero kulama maganizo, nzeru, ndi luntha nzofunika kuti mawu athu akhale otsitsimula ndi olimbikitsa. Nthaŵi pamene tilankhula, zimene tilankhula, ndi kuchuluka kwa zimene tilankhula nzofunika kwambiri.
Mwachitsanzo, patsiku lotentha, ndikotsitsimula chotani nanga chikho cha madzi ozizira kwa waludzu! (Mateyu 10:42) Komatu palibe aliyense amene angayerekezere kuthira mtsuko wodzala madzi pamutu wake! Woyang’anira dera wogwidwa mawu pamwambapa akuti: “Zotulukapo zabwino kwambiri zimafikiridwa ndi awo amene amadzutsa chikhumbo chofuna kudziŵa mwa achibale awo mwa kuchitira umboni pamlingo woyenelera.” Pamene wachibale wotsutsa akhala ndi ludzu, kunena kwake titero, ndi kuyamba kufunsa mafunso, kaŵirikaŵiri makambitsirano opindulitsa Abaibulo amatsatira.
Huriye, Mboni ya ku Turkey, anakwaniritsa chimenechi panyumbapo mwa kusiya mabukhu a Baibulo ali otsegulidwa pa nsonga zimene zikakhala zokondweretsa mwamuna wake wosakhulupirirayo. Iye anaŵerengera ana ake nkhani za Baibulo, ndipo—ngati mwamunayo anali kumvetsera—iye ankapereka malongosoledwe amene anali opindulitsa kwa iye. Nthaŵi zina ankafunsa kuti: “Ndaphunzira zakutizakuti m’phunziro langa lero. Kodi muganizanji za izi?” Iye akutchulanso malamulo a makhalidwe abwino amene anakumbukira: “Khalani wodekha, ndipo musakwiyitsidwe kapena kupezera mlandu. Musakhale wodziŵa zonse. Khalani wodzichepetsa ndi kulola kutsogozedwa.” Pambuyo pake mwamuna wakeyo anavomereza chowonadi Chaufumu ndipo tsopano akutumikira monga minisitala wanthaŵi zonse.
Marijan anathandiza achibale angapo kuvomereza chipembedzo chake. “Musakakamize zinthu koma yembekezerani nthaŵi yoyenera,” iye akulangiza motero. “Tifunikira kuwalemekeza atatipempha kusalankhula nawo chowonadi. Tiyenera kukhala oleza mtima ndi achikondi.” Makamaka pamene achibale ali otsutsa ndipamene Mlaliki 3:7 imagwira ntchito. Iyo imati pali “nthaŵi ya kukhala chete ndi nthaŵi ya kulankhula.” Zimenezo zimafunikiritsa kufunitsitsa kwa kumvetsera moleza mtima, osati kudodometsa, koma kulemekeza malingaliro a ena. “Kuli kupanda nzeru kupsa mtima pokambitsirana ndi achibale,” akutero Petar, amene kale anali wotsutsa kwambiri koma amene adasintha mkhalidwe wake.
Lolani Makhalidwe Abwino Alalikire
Kwazaka zingapo mwamuna wosakhulupirira anavutitsa mkazi wake Wachikristu, nthaŵi zina akumamtsekera kunja kwanyumba. Nthaŵi zina iye anakwiya kwambiri kotero kuti anang’amba bukhu limene mkaziyo anaiwala kuchotsa. Kodi chinasintha kachitidwe kake nchiyani? Iye akulongosola kuti: “Ndinapitirizabe kudzifunsa chifukwa chake mkazi wanga anali wosasunthika motero ndipo anapitirizabe kudalira pa Yehova. Sindikapeza cholakwa kwa iye, popeza adasunga nyumba bwino lomwe, ndipo adali mkazi wapanyumba wabwino ndi mayi wa ana athu.” Tsiku lina mwamunayo anali kufunafuna mfundo zabwino zokakamba paprogramu yamphindi zisanu, chotero mkazi wake anampatsa makope aŵiri a Galamukani! Iye mwamphwayi anasuzumiramo mofulumira, ndipo anadabwa kuti adapeza nkhani yopindulitsa yonena za kupangidwa kwa mapensulo. Mwanjirayi chikondwerero chake m’magazine amenewa chinadzutsidwa. Lerolino, banja limeneli nlogwirizana m’kulambira Yehova.
Uphungu wa mtumwi Petro wakuti mkazi angakole mwamuna wosakhulupirira popanda mawu kupyolera mwa makhalidwe okoma limodzi ndi ulemu wakuya’ umagwiranso ntchito kuziwalo zina za banja. (1 Petro 3:1, 2) Pamene okwatirana aŵiri adasiya mwambo wakale wosagwirizana ndi Baibulo ndi chipembedzo cha makolo awo a ku Romania, mabanja awo adakhala otsutsana moipitsitsa. Mkaziyo anafikira pa kuukiridwa ndi apongozi ake, amene adayesayesa kumupha. “Sitinalole chimenechi kutilefula kapena kutiputa. Tidaponya nkhaŵa zathu zonse pa Yehova,” akutero Nikolic. Zaka khumi ndi chimodzi pambuyo pake makolo ake, ponse paŵiri a mlongo wake, ndi amuna a alongo ake anakhala Mboni zobatizidwa. Kodi chinathetsa vutolo nchiyani? “Chitsanzo chabwino kwambiri ndi mkhalidwe Wachikristu. Mwamawu ena, sitinathere nthaŵi yokulira tikumalankhula nawo za chowonadi. Mmalo mwake, tinayesa kuzigwiritsira ntchito.”
Musataye Chiyembekezo!
Pamene kuli kwakuti kumakondweretsa kwambiri kuwona achibale akuyamba kulambira Mulungu wowona, kodi bwanji ngati ena apitirizabe kutsutsa? Kodi muyenera kuchita motani? Yesu adawoneratu kuti nthaŵi zina kulambira kowona kukadzetsa magaŵano aakulu pakati pa achibale. (Mateyu 10:34-37) Marica ananyanyalidwa ndi ziwalo zonse za banja pamene anakhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Pamene kuli kwakuti iye sanagonjere m’kulambira kwake, akuvomerezabe “kuti ngakhale achibale ali ndi kuyenera kwa kusonyeza malingaliro awo ndi ziganizo.” Mkhalidwe wake unafulumiza kumlemekeza monga momwe adachitira kalero.
Ludwig adazindikira kuti anali ndi thayo la kukonda makolo ake ngakhale ngati iwo angasankhe njira yamoyo yosiyana. iye anakumbukira mobwerezabwereza mawu oyenera a Baibulo, onga ngati akuti: “Lemekeza atate wako ndi amako”; “mawu anu nthaŵi zonse akhale abwino, okometseredwa ndi mchere”; “[khalani] okonzekera kudzichinjiriza . . . ndi kufatsa ndi ulemu waukulu”; ndi “kapolo wa Ambuye sachita ndewu.” (Aefeso 6:2; Akolose 4:6; 1 Petro 3:15, NW; 2 Timoteo 2:24) “Nthaŵi iriyonse imene ndichita telefoni kwa makolo anga kapena kuwachezera, ndinapemphera kwa Yehova kaamba ka nzeru, ndipo mwapang’ono ndi pang’ono unansi wathu udakhala waphee koposerapo, waubwenzi koposerapo,” iye akusimba tero.
Musataye chiyembekezo pakuti mbewu za chowonadi potsirizira pake zidzamera m’mitima ya achibale anu. Atabatizidwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova zaka 31 pambuyo pa mkazi wake, mwamuna wina adathirira ndemanga zakuti: “Nditayang’ana kumbuyo, ndiyenera kuvomereza kuti mkazi wanga adaali woleza nane mtima kwambiri. Ndidaadziwa bwino lomwe kuti iye kaŵirikaŵiri anali kundipempherera kwa Yehova.”
Mawu otuluka mkamwa mwanu nthaŵi zonse akhaletu atawatawa ndi othetsa ludzu monga madzi ozizira! Inde, gaŵanani “mbiri yabwino yaulemerero ya Mulungu wachimwemwe” ndi anthu onse, kuphatikizapo achibale anu. (1 Timoteo 1:11 NW; Chivumbulutso 22:17) Kenaka mawu a Yesu adzagwira ntchito akuti: “Iye wokhulupirira ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi ya moyo idzayenda, kutuluka mkati mwake.”—Yohane 7:38.