Nyimbo 48
Tamani Yehova
1. Tamani Yehova.
M’chikondi chake
Mwapatsidwa ntchito
Younikira.
Palibenso chomwe
Simulandira
Kwa M’lungu wanuyo;
Mumlemekeze.
2. M’kwezeni iyeyo;
Dzichepetseni.
Tero mudzaŵala
Ndi za kumwamba.
Yenda mwa Iyeyo,
Mumfunefune,
Mukumatsogoza
Ntchito yakeyo.
3. Mukatu mokondwa
Kumtumikira;
Thokozadi zonse
Aperekazi.
Tamatu Yehova,
Lalikiratu,
Kufikira onse
Amlemekeze.