Nyimbo 34
Kukhala ndi Moyo Mogwirizana ndi Dzina Lathu
1. Yehova, wamphamvuyonse, wamyaya,
Wosayerekezeka m’chikondi,
Magwero a chowonadi ndi nzeru,
Inu mulamula monga Mfumu.
Angelo akondwera m’ntchito yanu;
Chilengedwe chinena za inu.
Mwatcha ife kukhala Mboni zanu;
Tigwirizane ndi dzina lathu!
2. Mutithandize, M’lungu nthaŵi zonse
Kulilemekeza dzina lanu,
Kuziwongolera mphatso za ntchito
Posamala malangizo anu.
Tikasamale mayendedwe athu,
Kuti chitonzo china chisadze.
Amwaŵidi pokhala Mboni zanu;
Tigwirizane ndi dzina lathu!
3. Pokhalabe muutumiki wanu,
Limodzi mtendere ndi chikondi,
Chikhutiro chikhala gawo lathu;
Potamandanu tisangalala.
Tigwirizane ndi dzina lathulo;
Kuuza cho’nadi kwa’nthu onse;
Ndipo koposa zonse chikondwero,
Kumtima wanu, Yehova Mfumu!