Nyimbo 43
Patsogolo, Inu Aminisitala Aufumu!
1. Lalikiranibe Ufumu
Kwa anthu onse m’dziko.
Mwachikondi cha paanansi,
Thandizani ofatsa.
M’kulemekeza utumiki
Tisamale mavalidwe.
Uministala ngwapamwamba;
Tifuna kudalitsa Ya.
(Korasi)
2. Aministala atsopano
Pitani patsogolo.
Muiŵale zomwe mwasiya,
Pezani nyonga mwa Ya.
Monga zotengera za M’lungu
Musiyane ndi dzikoli.
Anthu a M’lungu ayenera
Kusiya njira zadziko.
(Korasi)
3. Tonse tipite patsogolo,
Otsalira ndi “nkhosa.”
Amuna, akazi, ndi ana,
Tiyende m’chowonadi.
Ntchito yathu njopatulika
Tifuna kuiyeretsa.
Imatonthoza olungama
Nalemekeza Yehova.
(KORASI)
Pitanibe,
Falitsani Ufumu kulikonse.
Khalanibe
Okhulupirika kwa Yehovayo.