Nyimbo 75
Kutamanda Yehova Mokondwera
1. Ndi milomo yokondwera
Titamanda mwachimwemwe.
Yehova amagaŵira
Zonse zimene tifuna.
Ndi mitima yokondwera
Tifuula kwa Yehova.
Timamthokozadi nthaŵi zonse;
Moyo wathu ukondwera.
2. Anapereka Mwana’ke,
Akhale chipulumutso.
Timakweza manja athu,
Kupempherera chiyero.
Unansi wathu ulidi,
Monga chuma chapatali.
Chikondicho sichidzazirala;
Timkonda ndi moyo wonse.
3. Tiwona ulemerero.
Tikondwa ndi chitsogozo!
Mwachimwemwe timlambira,
Tidaliradi mwa iye.
Pansi pamapiko ake,
Tipezapo tchinjirizo!
Mtima uimba moyamikira;
Pakuti timamkondadi.